Kodi Mungaloŵenso Pamzerawo?
1 M’zaka zisanu zapitazo, apainiya okhazikika mazana ambiri anakuona kukhala kofunika kuchoka pamzera wa apainiya. Kodi munali mmodzi wa iwo? Ngati ndi choncho, mosakayikira munali ndi chifukwa chosiyira mwaŵi umenewu. Mwinamwake chinali kanthu kamene simunakayembekezere kapena kamene simukanakhoza kulamulira. Kodi chifukwa chimenecho chikalipobe? Ngati thanzi, mavuto azandalama, kapena mathayo a banja ndizo zinakuchititsani kuleka, kodi mikhalidweyo yawongokera? Kodi mungapange masinthidwe oyenera amene angakuloleni kupeza madalitso a upainiya wokhazikika? Kodi mwaganizirapo za kufunsiranso?
2 Monga mudziŵa, dongosolo labwino ndi kukonza ndandanda mosamalitsa nkofunika ngati muti mupambane monga mpainiya. Pamene kuli kwakuti kaŵirikaŵiri sipamakhala nthaŵi yochuluka yoseŵera, kaŵirikaŵiri nyengo zazifupi za kupuma za mpainiya zimakhaladi zokhutiritsa ndi zofupa kwambiri. (Miy. 19:17; Mac. 20:35) Mwa kukhala otanganitsidwa muutumiki, mumatetezeredwa ku chisonkhezero cha moyo wosavuta ndi wofuna za mwini yekha umene dziko limafunafuna. Yehova walonjeza kuti adzakulemeretsani mwauzimu ngati muli wodzimana ndipo ngati mumaika zinthu za Ufumu poyamba. Kunena zoona mudzapeza chimwemwe ndi chikhutiro mwa kuchita utumiki wa Yehova ndi mtima wonse.—Miy. 10:22; Akol. 3:23, 24.
3 Kodi utumiki wanthaŵi yonse uyenera kuonedwa monga mwaŵi wotsegukira anthu oŵerengeka apadera okha? Iyayi. Polingalira za choŵinda chathu cha kudzipatulira, Mkristu aliyense ayenera kulingalira mwamphamvu za utumiki wanthaŵi yonse kusiyapo ngati mikhalidwe simulola.—Marko 12:30.
4 Ngati mosakayikira konse thanzi lanu ndi mathayo anu a m’Malemba sakulolani kuchita upainiya pakali pano, tikutsimikizirani kuti Yehova akudziŵa ndipo amamvetsetsa. Adzakufupani kaamba ka kukhulupirika kwanu pa zimene mikhalidwe yanu imakulolani. (1 Akor. 4:2; 2 Akor. 8:12) Komabe, ngati tsopano mukukuona kukhala koyenera kuchitanso upainiya, bwanji osafikira woyang’anira wotsogoza ndi kupempha fomu yofunsirapo?
5 Kodi Banja Lanu Likhoza Kuthandiza? Mungakhale mutachoka pamzerawo chifukwa chakuti munafunikira kusamalira mathayo a banja. Kodi nzotheka kuti tsopano ziŵalo zina za banja zikhoza kupereka chithandizo chimene chingakukhozetseni kuloŵanso ntchito ya upainiya? Kwa ena, mwa kungolandira chithandizo pang’ono posamalira mathayo akutiakuti, upainiya ungakhalenso wotheka.
6 Kugwirizanika ndi kuyesayesa kokulirapo kwa ziŵalo zina za banja kungatheketse zimenezi. Chithandizocho chingaperekedwe mumpangidwe wa ndalama kapena choyendera, limodzi ndi makonzedwe okhazikika a kugwirira ntchito limodzi nanu muutumiki. Payeneranso kukhala njira zina zimene iwo angaperekere thandizo. Ngati mikhalidwe sikulolani kulandiranso mwaŵi umenewu wa utumiki, mwinamwake thandizo lotero lingaperekedwe kwa chiŵalo china cha banja chimene chingachite zimenezo.
7 Bwanji osakambitsirana nkhani imeneyi monga banja? Pangakhale zotulukapo zabwino ngati muchitira zimenezi pamodzi. Ngati mpainiya wina angawonjezeredwe pamzerawo, banja lonse lingamve moyenerera kuti likukhalamo ndi phande. Mzimu wowoloŵa manja wotero sudzangochirikiza umboni wa Ufumu m’gawolo komanso udzagwirizanitsa banja lonse pamodzi mwauzimu.—Luka 6:38; Afil. 2:2-4.