Zilengezo
◼ Mabuku amene adzagwiritsiridwa ntchito mu August: Lililonse la mabrosha amasamba 32 otsatirawa lingagwiritsiridwe ntchito: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, ndi Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani? September: Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. October: Masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! November: New World Translation of the Holy Scriptures ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? CHIDZIŴITSO: Mipingo imene sinaodebe zinthu zamkupiti zotchulidwa pamwambapa iyenera kutero pa fomu ya Literature Order (S-14) yawo yotsatira ya mwezi ndi mwezi.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1995 pa oda yawo yamabuku ya September. Makalenda adzakhalako m’Chicheŵa, Chibemba, ndi Chingelezi.
◼ Kuyambira pa 1 mpaka pa 7 September, Sosaite idzakhala ikuŵerengera mabuku amene alipo ku Beteli. Chifukwa cha kuŵerengera kumeneku, palibe maoda amabuku a mpingo amene adzasamaliridwa kuti atumizidwe kapena kutengedwa m’masiku amenewo.
◼ Mtokoma wokwanira wa mafomu ogwiritsira ntchito m’chaka chautumiki cha 1995 ukutumizidwa kumpingo uliwonse. Mafomu ameneŵa sayenera kuwawanyidwa. Ayenera kugwiritsiridwa ntchito pachifuno chokha chimene analinganizidwira.
◼ Mpingo uliwonse udzalandira mafomu atatu a Kuŵerengera Mabuku (S-18). Mlembi wa mpingo ayenera kukumana ndi mtumiki wa mabuku kuchiyambi kwa August ndi kukhazikitsa deti loŵerengera sitoko ya mabuku a mpingo pamapeto a mweziwo. Kuŵerengera kwenikweni kuyenera kuchitidwa pa mabuku onse amene ali m’sitoko, ndipo ziwonkhetso zake ziyenera kulembedwa pa fomu ya Kuŵerengera Mabuku. Chiwonkhetso cha magazini amene alipo chingapezedwe kwa mtumiki wa magazini. Chonde tumizani kope loyamba ku Sosaite mosapyola pa September 6. Sungani kope lachiŵiri m’mafaelo anu. Kope lachitatu lingagwiritsiridwe ntchito monga pepala logwirirapo ntchito. Kuŵerengerako kuyenera kuyang’aniridwa ndi mlembi, ndipo fomu yodzazidwa iyenera kupendedwa ndi woyang’anira wotsogoza. Mlembi ndi woyang’anira wotsogoza adzasaina fomuyo.
◼ Ofalitsa amene afuna kuyamba utumiki waupainiya wokhazikika pa September 1, 1994, ayenera kufunsira mosachedwa.
◼ Mlembi wa mpingo adzasonkhanitsa malipoti autumiki kuti awalembe pa fomu ya Lipoti la Kulongosola Ntchito za Mpingo (S-10). Ndiponso adzalangiza mosamalitsa mkulu kapena mtumiki wotumikira aliyense amene angamthandize pokonza lipotilo. Zimenezi zidzatsimikiziritsa kulembedwa kwa ziŵerengero zolondola zofunikira zotengedwa pa makadi a Cholembapo cha Wofalitsa cha Mpingo (S-21). Fomu ya Lipoti la Kulongosola Ntchito za Mpingo (S-10) iyenera kudzazidwa molondola ndi mwaudongo ndi kupendedwa mosamalitsa ndi komiti yautumiki. Chonde itumizeni ku Sosaite mwamsanga. Chaka chatha, mipingo 296 sinatumize malipoti awo.
◼ Tikufuna kudziŵitsa pasadakhale awo onse amene akhala pandandanda monga apainiya okhazikika kuyambira October 1, 1993 kapena lisanafike detilo, amene sanaloŵebe Sukulu Yautumiki Waupainiya kuti sukuluyo idzakhalako mu October 1994. Chonde pangani makonzedwe otsimikizirika kuti mukaloŵe Sukulu Yautumiki Waupainiya mu October. Kumbuyoku ena, popanda zifukwa zabwino, aphonya makonzedwe ameneŵa. Sitikufuna kuti mpainiya aliyense aphonye sukuluyo. Chidziŵitso chowonjezereka chidzatumizidwa kwa inu ndi woyang’anira dera.
◼ Zofalitsidwa Zimene Zilipo:
Chingelezi: American Standard Version (bi11); New World Translation of the Holy Scriptures (yachikuto chofeŵa, yaukulu wokhoza kuloŵa m’thumba, yofiirira—Dlbi25m); Comprehensive Concordance; Kukambitsirana za m’Malemba; Magazine File Case.
◼ Kaseti Yatsopano Imene Ilipo:
The Greatest Man Who Ever Lived. (Alabamu).
◼ Vidiyo Kaseti Yatsopano:
The Bible—Our Oldest Modern Book.