Misonkhano Yautumiki ya August
Mlungu Woyambira August 1
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo ndi Zilengezo zoyenerera za mu Utumiki Wathu Waufumu. Sonyezani mfundo zokambitsirana za m’magazini atsopano zimene zingagogomezeredwe muutumiki wakumunda kumapeto kwa mlungu uno.
Mph. 15: “Khalani ndi Mkhalidwe Wabwino Wamaganizo.” Mafunso ndi mayankho. Funsani mwachidule mpainiya kapena wofalitsa wakale amene adzasimba mmene kwakhalira kotheka kukhala ndi mkhalidwe wabwino wamaganizo mosasamala kanthu za mphwayi kapena chitsutso m’gawo.
Mph. 15: “Mabrosha—Zipangizo za Muutumiki Zamtengo Wapatali.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Konzani zitsanzo ziŵiri zokonzekeredwa bwino za maulaliki operekedwa. Sonyezani ena a mabrosha amene adzagaŵiridwa mu August. Kumbutsani omvetsera kuwombola makope ogwiritsira ntchito muutumiki mlungu uno.
Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 8
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Pendani lipoti lautumiki la mpingo la July.
Mph. 15: “Dziŵani Bwino Abale Anu.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvetsera kufotokoza zokumana nazo zachidule zosonyeza mmene anakhalira okhoza kudziŵana bwino ndi ena mwa kugwiritsira ntchito malingaliro a m’ndime 6.
Mph. 20: Mlembi akambitsirana ndi mtumiki wotumikira wosamalira maakaunti a mpingo. Mtumiki wa maakauntiyo afunsa mlembi za mmene akuchitira mu ntchito yake. Mlembi amuyamikira ndi kumlimbikitsa kupitiriza kutsegula mabokosi a zopereka ndi kuŵerengera ndalamazo ali ndi munthu wina. Awonjezera kuti ayenera kuŵerenga ndi kutsatira mosamalitsa “Malangizo a Kasungidwe ka Maakaunti Ampingo—S-27.” Mbali yaikulu ya kukambitsiranako izikidwa pa nkhani yakuti “Kodi Nkubadi?” ya mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1994, masamba 19-21.
Nyimbo Na. 182 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 15
Mph. 5: Zilengezo zapamalopo, kuphatikizapo lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro za zopereka.
Mph. 15: “Kukulitsa Chikondwerero pa Maulendo Obwereza.” Kambitsiranani ndi omvetsera. Phatikizanipo zitsanzo ziŵiri za mphindi zitatu zosonyeza mmene maulaliki angagwiritsiridwe ntchito kupanga maulendo obwereza. Limbikitsani zoyesayesa za kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mph. 25: “Pitirizani Kuyenda Mopita Patsogolo m’Njira Yakachitidwe Yadongosolo.” Mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 96 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 22
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo ndi “Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Ngati mukulidziŵa, lengezani deti la programu ya tsiku la msonkhano wapadera wotsatira ndipo limbikitsani onse kupanga makonzedwe a kupezekapo.
Mph. 15: “Kodi Ndingayandikire Bwanji kwa Mulungu?” Chitsanzo cha phunziro labanja. Makolo akambitsirana ndi ana azaka zapakati pa 13 ndi 19 nkhani ya m’mutu 39 wa buku la Achichepere Akufunsa. Kambitsiranani mutu waung’ono wakuti “Kulengeza Poyera Unansi Wanu ndi Mulungu,” masamba 315-18. Anawo akudandaula kuti amachita manyazi pamene akupita kukhomo ndi khomo ndipo akulongosola misonkhano kukhala yobwerezabwereza ndi yochitika kaŵirikaŵiri. Makolo akambitsirana nawo mokoma mtima, akumasonyeza malamulo a mkhalidwe Amalemba amene amasonyeza kuti zochitika zimenezi zili zofunika kuti iwo akhale ndi unansi wabwino ndi Yehova.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Kapena kambani nkhani pa mutu wakuti “Kukhala Otanganitsidwa Kwambiri ndi Mbiri Yabwino” wa mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1991, masamba 28-30.
Nyimbo Na. 184 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 29
Mph. 13: Zilengezo zapamalopo. Pendani Lipoti Lautumiki la April. Yamikirani ofalitsa chifukwa cha kugwira ntchito kwawo zolimba muutumiki wakumunda. Funsani ndemanga za mmene tingawongolere avareji ya maola 11.1 pa wofalitsa mmodzi. Funsani wofalitsa mmodzi kapena aŵiri amene anali okhoza kuchita upainiya wothandiza kapena kufutukula mwa njira ina ntchito yawo mkati mwa miyezi yoŵerengeka yapita. Simbani zina za zisangalalo zimene anakhala nazo.
Mph. 15: “Kodi Mungaloŵenso Pamzerawo?” Kambitsiranani ndi omvetsera. Phatikizanipo zokumana nazo zilizonse zakumaloko zosonyeza mmene wina wakhalira wokhoza kuloŵanso utumiki waupainiya kapena mmene banja lina linagwirizanirana kuthandiza chiŵalo cha banja kutenga mwaŵi umenewu.
Mph. 17: Gawirani Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha m’September. Limbikitsani zoyesayesa zamphamvu za kugaŵira bukuli ndi kuyambitsa maphunziro m’September. Linatulutsidwa mu 1982 ndipo kuyambira pamenepo lagwiritsiridwa ntchito monga chipangizo chachikulu chochititsira maphunziro a Baibulo. Makope amene anatulutsidwa pa misonkhano yachigawo anali ndi uthenga uwu: “Buku lophunzirira latsopanoli lili ndi zimene zikufunikira kuthandiza ambiri kukhala ndi chiyembekezo chimodzimodzi chimene tili nacho. . . . Lili ndi choonadi cha Baibulo chonse chofunika chimene atsopano afunikira kumvetsetsa kotero kuti apatulire miyoyo yawo kwa Yehova ndi kumtumikira movomerezeka.” Zotulukapo zake zasonyezedwa ndi chiwonjezeko cha ofalitsa kuchokera pa 2,652,323 mu 1983 kufika pa 4,709,889 mu 1993. Pemphani anthu kusimba mmene anaphunzirira choonadi mwa kuphunzira bukuli kapena mmene anathandizira ena mwa kuphunzira nawo. Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mbali zina za bukuli zimene zingasonyezedwe poligaŵira.
Nyimbo Na. 161 ndi pemphero lomaliza.