Ndandanda ya Mlungu wa March 28
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 28
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 4, ndime 19-24 ndi bokosi patsamba 45 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yobu 11–15 (Mph. 10)
Na. 1: Yobu 13:1-28 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Yesu Ali “Mbuye wa Sabata”?—Mat. 12:8. (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yesu Anali ndi Moyo Kumwamba Asanakhale Munthu?—rs tsa. 431 ndime 1–2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Tchulani mabuku ogawira m’mwezi wa April ndipo muchite chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene mungayambire phunziro la Baibulo pa ulendo wobwereza kwa munthu amene analandira magazini.
Mph. 10: Kupereka Chithandizo pa Ntchito ya Ufumu Kwanuko ndi Padziko Lonse. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 127 mpaka 129 ndime 2.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa April. Nkhani yokambirana. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani mitu iwiri kapena itatu, ndipo funsani omvera kuti afotokoze mafunso ndiponso malemba amene akhoza kugwiritsa ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire magazini iliyonse.
Mph. 10: “Kodi Nthawi Ina Munakhalapo Mpainiya Wokhazikika?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Mungafunse mwachidule m’bale kapena mlongo amene anasiyapo upainiya kenako n’kuyambiranso utumikiwu zinthu zitasintha pa moyo wake. Kodi chinamuthandiza n’chiyani kuti ayambirenso upainiya? Kodi wapeza madalitso otani?
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero