Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 29, 2005. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 4 mpaka August 29, 2005. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Tikamauza anthu ena chiyembekezo chathu, kodi tingachite bwanji kuti ‘kulolera kwathu kuzindikirike ndi anthu onse,’ ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? (Afil. 4:5, NW; Yak. 3:17, NW) [be-CN tsa. 251 ndime 1-3, bokosi]
2. Kodi kudziwa pamene tikufunika kulolera kudzatithandiza bwanji kukambirana bwino ndi anthu ena? [be-CN tsa. 252 ndime 5–tsa. 253 ndime 1]
3. N’chifukwa chiyani kupereka mafunso mwaluso kuli kofunika tikamathandiza anthu kulingalira pa nkhani imene tikukambirana nawo? [be-CN tsa. 253 ndime 2-3]
4. Kodi tiyenera kuganizira mfundo ziti pofuna kuti nkhani yathu ikhale yokopa? [be-CN tsa. 255 ndime 1-4, bokosi; tsa. 256 ndime 1, bokosi]
5. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikafuna kugwiritsa ntchito zimene maumboni enanso amavomereza pofuna kusonyeza nzeru ya m’Malemba? [be-CN tsa. 256 ndime 3-5, bokosi]
NKHANI NA. 1
6. Kodi ndi umboni womveka uti umene umasonyeza kuti Yesu anakhalakodi? [w03-CN 6/15 mas. 4-7]
7. Kodi ‘m’kamwa mwa olungama mumawalanditsa’ bwanji, ndipo kodi banja la olungama “limaimabe” motani? (Miy. 12:6, 7) [w03-CN 1/15 tsa. 30 ndime 1-3]
8. Popeza Baibulo sanalilembe ngati m’ndandanda wa malamulo a zimene tiyenera kuchita ndi zimene sitiyenera kuchita, kodi ‘tingadziwe bwanji chifuniro’ cha Yehova? (Aef. 5:17) [w03-CN 12/1 tsa. 21 ndime 3–tsa. 22 ndime 3]
9. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe munthu atazigwiritsa ntchito zingamuthandize kulimbana ndi umphawi kapena mavuto a zachuma? [w03-CN 8/1 tsa. 5 ndime 2-5]
10. Kodi chitsanzo cha Yehova cha kupereka mwaulere chiyenera kutikhudza bwanji? (Mat. 10:8) [w03-CN 8/1 mas. 20-2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi nsanamira ziwiri zotchedwa Yakini ndi Boazi zomwe zinali pakhomo la kachisi yemwe Solomo anamanga zinkatanthauza chiyani? (1 Maf. 7:15-22)
12. Kodi zimene Solomo anachita popereka midzi 20 ya m’dziko la Galileya monga mphatso kwa Mfumu Hiramu ya Turo zinali zogwirizana ndi Chilamulo cha Mose? (1 Maf. 9:10-13)
13. Kodi tingaphunzire phunziro lotani pa kusamvera kwa “munthu wa Mulungu”? (1 Maf. 13:1-25)
14. Kodi Mfumu Asa ya ku Yuda inasonyeza bwanji kulimba mtima, ndipo tingaphunzire chiyani ku chitsanzo chake? (1 Maf. 15:11-13)
15. Kodi zomwe zinachitika pakati pa Mfumu Ahabu ndi Naboti zikusonyeza bwanji kuipa kodzimvera chisoni? (1 Maf. 21:1-16)