PHUNZIRO 49
Kupereka Zifukwa Zomveka
PAMENE munena mawu alionse, omvera anu salakwa akamadzifunsa kuti: “Kodi zimenezo n’zoona? Nanga pali umboni wotani kuti tikhulupirire zimene akunenazi?” Monga mphunzitsi, muli ndi udindo woyankha kapena kuthandiza omvera anu kupeza mayankho. Ngati mfundoyo ndi yofunika kwambiri pankhani yanu, onetsetsani kuti mukupereka zifukwa zamphamvu kuti aikhulupirire. Zimenezi zidzachititsa kuti nkhani yanu ikhale yokopa.
Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito kukopa. Mwa zifukwa zomveka, mafotokozedwe otsatirika, ndi kupembedzera anthu moona mtima, iye anayesetsa kusintha maganizo a anthu amene analankhula nawo. Anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri. (Mac. 18:4; 19:8) Koma pali akatswiri ena odziŵa kulankhula amene amasocheza anthu powakopa ndi mawu osalala. (Mat. 27:20; Mac. 14:19; Col. 2:4) Iwo angayambe ndi mfundo zongoziganizira, amatenga mfundo zawo kwa anthu okondera, amapereka zifukwa zachiphamaso, amasiya mfundo zoona zotsutsa maganizo awo, kapena m’malo mopereka zifukwa zomveka amadalira kunena zinthu zongoti anthu atengeke nazo maganizo. Tiyenera kusamala kuti tipeŵe njira zoterozo.
Kambani Zochokeradi M’Mawu a Mulungu. Zimene timaphunzitsa zisamachokere mwa ife tokha. Timafuna kuuza anthu ena zimene timaphunzira m’Baibulo. Pambali imeneyi, zofalitsa za kapolo wokhulupirika ndi wanzeru zatithandiza kwambiri. Zofalitsa zimenezi zimatilimbikitsa kusanthula Malemba mosamala. Tikatero, timaphunzitsanso ena Baibulo, osati ndi cholinga chowagometsa, koma kuti aone okha zimene limanena. Timagwirizana ndi Yesu Kristu, amene m’pemphero kwa Atate wake anati: “Mawu anu ndi choonadi.” (Yoh. 17:17) Palibe wina wamkulu woposa Yehova Mulungu, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kuti zifukwa zathu zikhale zodalirika ziyenera kuchokera m’Mawu ake.
Nthaŵi zina mungalankhule ndi anthu osalidziŵa bwino Baibulo kapena osalikhulupirira kuti ndi Mawu a Mulungu. Kwa anthu otero, samalani kuti muone bwino pamene mungayenere kuloŵetsapo mawu a m’Baibulo. Koma mpata woyenerera ukapezeka, musazengereze kukambirana nawo mawu ochokera ku gwero lodalirika limenelo.
Kodi kungoŵerenga lemba loyenerera n’kokwanira kuti munthu akhulupirire zifukwa zimene mukupereka? Si nthaŵi zonse. Mungafunikire kufotokoza lembalo posonyeza kuti limaikiradi umboni zimene mukunena. Ngati mukungofunapo mfundo ina pa lembalo koma kwenikweni silikufotokoza nkhani imene mukukambiranayo, pezani umboni wina wowonjezera. Mungagwiritse ntchito malemba ena okhudzana ndi nkhaniyo kotero kuti omvera anu aone kuti zimene mukunena n’zochokeradi m’Malemba.
Peŵani kukokomeza zimene lemba likunena. Liŵerengeni mosamala. Lembalo lingakhudze zambiri pa nkhani imene mukukambirana. Koma kuti zifukwa zanu zikhale zogwira mtima, womvera wanu ayenera kuona mmene lembalo likutsimikizira nkhani imene mukukambirana.
Kambani Zimene Maumboni Enanso Amavomereza. Nthaŵi zina, ndi bwino kugwiritsa ntchito maumboni ena ochokera ku magwero ena odalirika osakhala Baibulo pofuna kuthandiza anthu kumvetsa nzeru ya m’Malemba.
Mwachitsanzo, mungasonyeze munthu zachilengedwe zooneka kumwamba ndi pansi pano ngati umboni wakuti Mlengi aliko. Mungatchulenso mphamvu zachilengedwe, ngati mphamvu yokokera zinthu pansi, kenako n’kufotokoza kuti kukhalapo kwa mphamvu zoterozo kumatsimikizira kuti alipo amene anazipanga. Mfundo yanu ingamveke pamene ikugwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu akunena. (Yobu 38:31-33; Sal. 19:1; 104:24; Aroma 1:20) Umboni woterowo umathandiza chifukwa umasonyeza kuti zimene Baibulo limanena n’zogwirizana ndi zimene timaona.
Kodi pakali pano mukuthandiza wina kuzindikira kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu? Mwina mungapereke umboni wa zimene akatswiri a Baibulo anena povomereza kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu, koma kodi umenewo ndi umboni wokwanira? Kugwira mawu anthu oterowo kumangothandiza anthu amene amakhulupirira akatswiriwo. Kodi mungagwiritse ntchito sayansi ngati umboni wosonyeza kuti Baibulo ndi loona? Kupereka maganizo a asayansi opanda ungwirowo ngati umboni wotsimikizira kuti Baibulo ndi loona ndiko kugwiritsa ntchito umboni wopanda maziko olimba. Koma ngati muyamba ndi Mawu a Mulungu, kenako n’kutchula zimene asayansi apeza zosonyeza kulondola kwa Baibulo, zifukwa zanu zidzaima pa maziko olimba.
Pofuna kutsimikizira chilichonse, perekani umboni wokwanira. Kuchuluka kwa umboni wofunikira kudzadalira omvera anu. Mwachitsanzo, ngati mukukambirana za masiku otsiriza onenedwa pa 2 Timoteo 3:1-5, mungatchulire omvera anu nkhani imene yamveka panyuzi yosonyeza kuti anthu ndi “opanda chikondi chachibadwidwe.” Chitsanzo chimodzi chimenecho chingakhale chokwanira potsimikizira kuti chizindikiro cha masiku otsiriza chimenechi tsopano chikukwaniritsidwa.
Kufanizira zinthu ziŵiri zokhala ndi mbali zofunika zofanana kumathandizanso. Koma kufanizira kokhako sikutsimikizira chilichonse, kuyenera kuyerekezedwa ndi zimene Baibulo limanena. Komabe kufanizira kungathandize munthu kuona nzeru ya mfundoyo. Mwachitsanzo, kufanizira koteroko kungathandize pofotokoza kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni. Mungasonyeze kuti mofanana ndi maboma a anthu, Ufumu wa Mulungu uli ndi olamulira, anthu ake, malamulo, zachiweruzo, ndi zamaphunziro.
Mungatchulenso zochitika zenizeni pofuna kusonyeza kuti kugwiritsa ntchito uphungu wa m’Baibulo n’kwanzeru. Ngakhalenso zochitika pa moyo wanu zingathandize kutsimikizira zimene munena. Mwachitsanzo, potchulira munthu za kufunika kwa kuŵerenga ndi kuphunzira Baibulo, mungafotokoze mmene kuchita zimenezo kwasinthira moyo wanu. Polimbikitsa abale ake, mtumwi Petro anatchula za kusandulika kwa Yesu, kumene anadzionera ndi maso ake. (2 Pet. 1:16-18) Paulonso anatchula zinthu zimene zinam’chitikira. (2 Akor. 1:8-10; 12:7-9) Koma musagwiritse ntchito zokuchitikirani nthaŵi zonse, kuti anthu asamangoganiza za inu.
Pakuti anthu amasiyana m’kakulidwe ndi kalingaliridwe, umboni umene ungakhutiritse munthu wina, wina sungam’khutiritse. Choncho, ganizirani malingaliro a omvera anu posankha zifukwa zoti mupereke ndi mmene mungaziperekere. Miyambo 16:23 imati: “Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake, nuphunzitsanso milomo yake.”