PHUNZIRO 22
Kugwiritsa Ntchito Malemba Moyenerera
POPHUNZITSA ena, sikokwanira kungoŵerenga malemba m’Baibulo. Mtumwi Paulo polembera mnzake Timoteo anati: ‘Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15.
Kuti tichite zimenezo tiyenera kutanthauzira malemba mogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Tiyenera kumvetsa nkhani yonse, osati kungosankha mawu otisangalatsa ndiyeno n’kuwagwirizanitsa ndi malingaliro athuathu. Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anachenjeza za aneneri omwe anali kunamiza anthu kuti anali kunenera za m’kamwa mwa Yehova koma ‘ananena masomphenya m’mitima yawo.’ (Yer. 23:16) Mtumwi Paulo anachenjezanso Akristu za kuipitsa Mawu a Mulungu ndi nzeru zaumunthu pamene analemba kuti: “Takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nawo mawu a Mulungu konyenga.” M’masiku amenewo amalonda achinyengo omwe anali kugulitsa vinyo anali kuthira madzi m’vinyo kuti achuluke ndi cholinga choti apezepo ndalama zambiri. Ife sitichita nawo monyenga Mawu a Mulungu mwa kuwasakaniza ndi nzeru zaumunthu. “Sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nawo mawu a Mulungu,” anatero Paulo, “koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.”—2 Akor. 2:17; 4:2.
Nthaŵi zina, mungagwire mawu lemba pofuna kuunika mfundo ya makhalidwe abwino. Baibulo lili ndi mfundo za makhalidwe abwino zambiri zothandiza pamakhalidwe ambiri osiyanasiyana. (2 Tim. 3:16, 17) Koma tsimikizani kuti mukugwiritsa ntchito lembalo molondola, osati kulikhotetsa kuti lioneke ngati likunena zimene inuyo mukufuna kuti linene. (Sal. 91:11, 12; Mat. 4:5, 6) Gwiritsani ntchito lemba malinga ndi cholinga cha Yehova, mogwirizana ndi Mawu a Mulungu onsewo.
‘Kulunjika nawo mawu a choonadi’ kumaphatikizaponso kuzindikira mzimu wa zimene Baibulo likunena. Mawu a Mulungu si “chibonga” choopsezera ena. Aphunzitsi achipembedzo amene anatsutsa Yesu Kristu anagwira mawu Malemba, koma sanayang’ane pankhani zenizeni zofunika—zokhudza chilungamo ndi chifundo ndi kukhulupirika—zimene Mulungu amafuna. (Mat. 22:23, 24; 23:23, 24) Pophunzitsa Mawu a Mulungu, Yesu anaonetsa mtima wa Atate wake. Kukangalika kwa Yesu pa choonadi kunatsagana ndi chikondi chake chozama chimene anali nacho pa anthu amene anali kuwaphunzitsa. Tiyeni tiyesetse kutengera chitsanzo chake.—Mat. 11:28.
Nanga tingatsimikize bwanji kuti tikugwiritsa ntchito malemba moyenerera? Kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse kungatithandize. Tiyeneranso kuyamikira mphatso ya Yehova ya “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” limene ndi bungwe la Akristu odzozedwa ndi mzimu. Yehova amagwiritsa ntchito bungwe limeneli kugaŵira chakudya chauzimu kwa a m’banja la chikhulupiriro. (Mat. 24:45) Phunziro laumwini, kufika pamisonkhano nthaŵi zonse ndi kutengamo mbali kudzatithandiza kupindula ndi malangizo operekedwa kudzera m’gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.
Ngati buku la Kukambitsirana za m’Malemba lilipo m’chinenero chanu ndipo ngati mungaphunzire kuligwiritsira bwino ntchito, lidzakuthandizani kugwiritsa ntchito moyenerera malemba ambirimbiri omwe timagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri mu utumiki wathu wa kumunda. Ngati mukufuna kugwiritsa ntchito lemba losazoloŵereka, kudzichepetsa kudzakupangitsani kufufuza kotero kuti pokalankhula, muzikalunjika nawo mawu a choonadi.—Miy. 11:2.
Gwiritsani Ntchito Malemba Momveka Bwino. Pophunzitsa ena, onetsetsani kuti akuona bwino lomwe mgwirizano womwe ulipo pakati pa nkhani imene mukufotokozayo ndi malemba amene mukuŵerenga. Ngati mutsogoza funso potchula lemba, omvera anu aone mmene lembalo liyankhire funsolo. Ngati cholinga choŵerengera lemba ndi kupereka umboni pa mfundo inayake, onetsetsani kuti wophunzirayo akuona bwino lomwe mmene lembalo likutsimikizira mfundoyo.
Kungoŵerenga lemba—ngakhale motsindika—kaŵirikaŵiri kumakhala kosakwanira. Kumbukirani kuti anthu ambiri salidziŵa bwino Baibulo moti sangamvetse mfundo yanu ngati mungoŵerenga lemba basi. Unikani mawu a lembalo okhudza mwachindunji nkhani imene mukukambirana.
Zimenezi zimafuna kuti mumveketse mawu ofunikira kwambiri, aja okhudza mwachindunji mfundo imene mukukambirana. Njira yosavuta yochitira zimenezo ndiyo kubwerezanso mawu opereka malingaliro ofunikawo. Ngati mukukambirana ndi munthu mmodzi, mungafunse mafunso omwe angam’thandize kuona mawu ofunikawo. Polankhula ku gulu la anthu, okamba nkhani ena amachita zimenezo mwa kugwiritsa ntchito mawu ofanana matanthauzo kapena mwa kubwerezanso mfundo. Komabe, mukasankha kuchita zimenezo, samalani kuti omverawo asataye mgwirizano wa pakati pa mfundo yanu ndi mawu a lembalo.
Popeza mwaunika mawu ofunika kwambiri, pamenepo mwayala maziko ofunikira. Tsopano pitirizani. Kodi potchula lembalo mwasonyeza bwino lomwe cholinga choliŵerengera? Ngati mwatero, sonyezani mmene mawu omwe mwaunikawo akusonyezera cholingacho. Sonyezani momveka bwino mgwirizano wa mawuwo ndi cholingacho. Ngakhale kuti simunachite kutchula cholingacho popereka lembalo, muyenera kuchitchulabe potsirizira pake.
Afarisi anafunsa Yesu funso limene m’maganizo mwawo analiona kukhala lovuta kwambiri. Iwo anati: “Kodi n’kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?” Yesu anayankha kuchokera pa Genesis 2:24. Onani kuti iye anangounika mbali imodzi yokha ya lembalo, kenako anapereka tanthauzo lofunikira. Atasonyeza kuti mwamuna ndi mkazi anakhala “thupi limodzi,” Yesu anati: “Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mat. 19:3-6.
Kodi muyenera kufotokoza zochuluka motani pofuna kumveketsa tanthauzo la lemba? Zimadalira mtundu wa omvera anu ndi kufunika kwa mfundo imene mukuifotokoza. Koma cholinga chanu nthaŵi zonse chizikhala kufeŵetsa zinthu ndi kulunjika pamfundo.
Lingalirani Nawo Kuchokera M’malemba. Kunena za utumiki wa mtumwi Paulo ku Tesalonika, Machitidwe 17:2, 3 amatiuza kuti iye ‘ananena za m’malembo.’ Mtumiki wa Yehova aliyense ayenera kuyesetsa kukhala ndi luso lolingalira kuchokera m’malemba. Mwachitsanzo, Paulo anafotokoza mfundo zokhudza moyo wa Yesu ndi utumiki wake, anasonyeza kuti Malemba Achihebri ananeneratu zimenezi, ndiyeno anaphera mphongo ndi ndemanga yakuti: “Amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.”
Pamene Paulo anali kulembera Ahebri, mobwerezabwereza anagwira mawu m’Malemba Achihebri. Pofuna kutsindika kapena kumveketsa mfundo, kaŵirikaŵiri anaunika liwu limodzi kapena mawu angapo kenako n’kufotokoza tanthauzo lake. (Aheb. 12:26, 27) M’nkhani yopezeka pa Ahebri chaputala 3, Paulo anagwira mawu Salmo 95:7-11. Onani kuti anaunika mbali zitatu za lembalo: (1) mtima wotchulidwawo (Aheb. 3:8-12), (2) tanthauzo la mawu akuti “Lero” (Aheb. 3:7, 13-15; 4:6-11), ndipo (3) tanthauzo la mawu akuti: “Ngati adzaloŵa mpumulo wanga” (Aheb. 3:11, 18, 19; 4:1-11). Yesetsani kutengera chitsanzo chimenecho pamene mugwiritsa ntchito lemba lililonse.
Onani mmene Yesu analingalirira mwaluso kuchokera m’Malemba pokambirana ndi munthu wina m’nkhani yopezeka pa Luka 10:25-37. Mwamuna wodziŵa Chilamuloyo anafunsa kuti: “Mphunzitsi, ndidzaloŵa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?” Yesu poyankha, choyamba anafunsa mwamunayo kuti anene maganizo ake pankhaniyo, kenako Yesu anatsindika kufunika kochita zimene Mawu a Mulungu anena. Yesu ataona kuti mwamunayo sanamve mfundo yake, anatenga kanthaŵi ndithu kuti afotokoze mofatsa liwu limodzi lokha pa lembalo—liwu lakuti “mnansi.” M’malo mongomasulira liwulo, anagwiritsa ntchito fanizo pofuna kuthandiza mwamunayo kuzindikira yekha mfundoyo.
N’zoonekeratu kuti Yesu pofuna kuyankha mafunso, sanangogwira mawu malemba opereka yankho lachindunji ndi lodziŵikiratu. Anasanthula zimene malembawo anali kunena ndiyeno anawagwiritsa ntchito poyankha funso loperekedwa.
Pamene Asaduki anatsutsa za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa, Yesu anatchula mbali imodzi yokha ya Eksodo 3:6. Koma iye sanangogwira mawuwo ndi kusiyira pomwepo. Analingalira nawo lembalo pofuna kusonyeza momvekera bwino kuti kuukitsa akufa ndi mbali ya cholinga cha Mulungu.—Marko 12:24-27.
Kupeza luso lolingalira moyenera ndi mwaluso kuchokera m’Malemba kudzakuthandizani kwambiri kukhala mphunzitsi waluso.