Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 25 tsamba 126-129
  • Kuŵerenga Malemba ndi Kuwatanthauzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuŵerenga Malemba ndi Kuwatanthauzira
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • **********
  • Kutsindika Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulozera Maganizo a Omvetsera ku Baibulo
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kugwiritsa Ntchito Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kutchula Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 25 tsamba 126-129

Phunziro 25

Kuŵerenga Malemba ndi Kuwatanthauzira

1-3. Polankhula nkhani, malemba tiyenera kuwaŵerenga motani?

1 Pamene mufotokozera ena zolinga za Mulungu, kaya mseri kapena poyera papulatifomu, nkhani yanu imasumika pa malemba amene muŵerenga m’Baibulo. Choncho m’pofunika kuti kaŵerengedwe ka malembako kachitidwe moyenera. Simuyenera kungoŵerenga chisawawa. M’malo mwake, kayenera kupereka mphamvu kunkhani yanu kuti cholinga choŵerengera lembalo chioneke. Pachifukwa chimenechi silipi la Uphungu wa Kulankhula limasonyeza mfundo yakuti “Kuŵerenga malemba ndi chigogomezo” kukhala yapadera yofunika kuti aliyense wofuna kukhala mlaliki wokhoza bwino aiphunzire.

2 Malemba ayenera kuŵerengedwa ndi mzimu wake, koma osati mopambanitsa. Chigogomezo cha lemba chiyenera kudalira mawu a lembalo ndi mbali yake m’nkhaniyo. Chiyenera kulimbikitsa mfundo yanu koma chisakopere maganizo onse a omvetsera ku kaŵerengedwe kanu.

3 Ndiponso, kaŵerengedweko kayenera kukopera maganizo kumbali ya lembalo limene likuchirikiza mfundo yanu. Kayenera kumveketsa mfundoyo moti omvetsera n’kukhutiritsidwa nayo. Inde, kuŵerenga malemba ndi chigogomezo choyenera kumapereka chidaliro. Kumapangitsa kuŵerengako kukhala ndi ukumu wake.

4, 5. Kodi kunena kuti “kugogomeza mawu oyenera” kumatanthauzanji? Perekani chitsanzo.

4 Kugogomeza mawu oyenera. Chifukwa choŵerengera lemba chiyenera kusonyeza mawu ofunika kuwagogomeza. Ngati tigogomeza mofanana ganizo lililonse m’lembalo, palibe chimene chidzaoneka chapadera ndipo mfundo yaikulu ya nkhaniyo idzatayika. Choncho onetsetsani kuti mawu ofunika chigogomezo chachikulu ndi aja okhala ndi ganizo limene mukufuna kulimveketsa poŵerenga lembalo.

5 Mwachitsanzo, ngati mugwiritsa ntchito Ezekieli 18:4 pofuna kupereka umboni wakuti uchimo umatsogolera ku imfa, osati ku chizunzo chosatha, mungaliŵerenge motere: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa,” mukumagogomeza kwambiri liwu lopendekeralo. Koma ngati mfundo imene mukufuna kumveketsa ndi yakuti si thupi lokha limene limafa komanso ngakhale moyo weniweniwo, mungasinthe chigogomezocho, ndi kunena kuti: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” Chifukwa choŵerengera lemba n’chimene chiyenera kukusonyezani mawu ofunika kuwagogomeza.

6-12. Kodi mawu okhala ndi ganizo m’lemba tingawagogomeze m’njira zotani?

6 Kugogomeza mwa njira yogwira mtima. Mawu okhala ndi ganizo amene mukufuna kuwamveketsa mungawagogomeze m’njira zosiyanasiyana, ndipo njira imene mukugwiritsa ntchito iyenera kugwirizana ndi lembalo komanso mtundu wa nkhaniyo.

7 Mbali imeneyi pamfundo yakuti “Kuŵerenga malemba ndi chigogomezo,” cholinga chake sikufotokoza njira zonse zogogomeza ndi mawu. Mudzapenda mfundo zimenezo mosamalitsa kwambiri pamene muphunzira kugogomeza ganizo. Koma panopa tandandalikapo njira zingapo kuti zikuthandizeni kuphunzira luso la kuŵerenga Malemba mogwira mtima.

8 Kugogomeza ndi mawu. Kumeneku kumaphatikizapo kusintha mawu kulikonse, kaya ndi ukulu wake, liŵiro kapena mphamvu, kumene kumapangitsa mawu okhala ndi ganizo kumveketsedwa kwambiri kuposa ena onse m’sentensi.

9 Kupuma. Mungapume pamene mufika pamawu ofunika kwambiri kapena pambuyo pake, kapenanso zonse ziŵiri. Kupuma kaye pamene mukufuna kuŵerenga mfundo yaikulu kumadzutsa chidwi; kupuma pambuyo pake kumazamitsa mfundoyo.

10 Kubwereza. Njira inanso yogogomezera mawu ndiyo mwa kulekeza kaye kuŵerengako, kenako n’kuŵerenganso liwulo kapena angapo. Njira imeneyi muyenera kuichita mosamala kwambiri.

11 Mwa kugwiritsa ntchito thupi, limodzi ndi manja ndi nkhope, mutha kugogomeza liwu limodzi kapena angapo.

12 Mamvekedwe a mawu. Nthaŵi zina mamvekedwe a mawu poŵerenga angakhudze tanthauzo lake ndi kuwagogomeza. Koma m’pofunika kusamala, makamaka poŵerenga mawu aukali.

13, 14. Pamene mwininyumba aŵerenga lemba, tingagogomeze motani mfundo zake zazikulu?

13 Malemba oŵerengedwa ndi mwininyumba. Pamene mwininyumba aŵerenga lemba, nthaŵi zina akhoza kugogomeza mawu olakwika mwinanso osagogomeza alionse. Kodi mungachitenji pamenepo? Zikatero, ndi bwino kuti inuyo mugogomeze mawu ofunikirawo potanthauzira lembalo. Mwininyumba akatha kuŵerenga, mungakopere maganizo ake ku mawuwo mwa kuwabwereza kapena kufunsapo mafunso.

14 Palinso njira ina imene mungachitire zimenezo, koma imafuna kusamala komanso luso. Pamene mwininyumba akuŵerenga, mukhoza kududukira pamalo oyenera, mukumapepesa pamene mukutero, ndiyeno kambanipo paliwu kapena mawu amene mukufuna kugogomeza. Ngati mukhoza kuchita zimenezo popanda kum’chititsa manyazi mwininyumbayo kapena kum’pomboneza kungakhale kogwira mtima, komanso kuyenera kuchitidwa kamodzikamodzi.

**********

15-17. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kutanthauzira lemba momveka bwino?

15 Kuŵerenga lemba, ngakhale mogogomeza, kaŵirikaŵiri sikukwaniritsa cholinga chanu. N’zoona kuti, nthaŵi zina lemba lokhalo lingapereke tanthauzo la mfundo yofunikira m’nkhani yanuyo. Koma, nthaŵi zambiri m’pofunika kutchulanso mawu opereka ganizo lofunikira m’lembalo ndiyeno kusonyeza tanthauzo lake. Ichi n’chimene silipi la Uphungu wa Kulankhula limatcha “Kumveketsa bwino tanthauzo la malemba.” Kumbukirani kuti anthu ambiri salidziŵa bwino Baibulo ndipo sangamvetse mfundo yanu pakuŵerenga kumodzi kokha. Kugogomezanso mawu ofunikawo ndi kuwatanthauzira kumalola mfundozo kukhazikika m’maganizo mwawo.

16 Kuti mukhoze kutanthauzira lemba, liyenera kugwirizana ndi nkhani yanu, komanso muyenera kulitulutsa bwino. Ndiyeno, pokumbukira kuti cholinga chanu ndi kuphunzitsa, mudzatanthauzira lembalo mwa njira yosavuta kumva.

17 Ndiponso, muyenera kulimvetsa bwino lembalo komanso kutanthauzira kwanu kukhale kolondola. Pendani nkhani yake, mfundo zopezekamo kapena anthu ophatikizidwamo, ngati malembawo afuna kuti mutero. Musagwiritse ntchito lemba mosiyana ndi cholinga cha wolemba wake. Tsatirani mosamalitsa kutanthauzira kopezeka m’mabuku a Sosaite.

18. Ndi motani mmene tingalekanitsire bwino mawu ofunika kutanthauzira?

18 Kulekanitsa mawu ofunika kuwatanthauzira. Musanatanthauzire lemba kapena m’kati molitanthauzira, nthaŵi zonse ndi bwino kugogomezanso mawu ofunikira kwambiri. Mumatero pofuna kutsimikiza kuti chilichonse m’lembalo chosakhudzana ndi mfundo yanu chisaonekere kwambiri kapena chidzakhala chosafunika kwambiri. Kuti muchite zimenezo sipofunikira kwenikweni kuti mubwereze mawu enieniwo a m’lembalo, ngakhale kuti ndi mmene timachitira nthaŵi zambiri. Koma nthaŵi zina mukhoza, mwanjira ina, kukopera maganizo a omvetsera anu ku mfundo zina zapadera zimene mukufotokoza. Njira imene mungachitire zimenezo ndiyo mwa kugwiritsa ntchito mawu ofanana pofuna kugogomeza ganizo. Njira inanso ndiyo kufunsa mafunso. Ngati nkhani yanu ikuphatikizapo mwininyumba, mafunso anu angakhale ofuna kutulutsa maganizo ofunikira kuchokera kwa munthu winayo.

19-22. Ndi kubwereza mawu kotani kumene timati “mfundo ya mawu oyamba poŵerenga lemba imveketsedwa”?

19 Mfundo ya mawu oyamba poŵerenga lemba imveketsedwa. Zimenezi zimangotanthauza kutsimikiza kuti cholinga chanu chogwiritsira ntchito lemba chadziŵika ndipo chamveketsedwa bwino. Mwina pachifukwa chakutichakuti simungafune kulankhula mawu oyamba poŵerenga lemba. Zimenezo sizikutanthauza kuti mfundo ya lembalo siyenera kumveketsedwa. Koma, mwalamulo lake, muyenera kukhala mutakonzekera mfundo zozifotokoza musanaŵerenge lembalo. Ndiyeno onetsetsani kuti mwabwereza mawu osonyeza bwino cholinga choŵerengera lembalo.

20 Mlingo wa kutanthauzira lemba udzadalira mtundu wa omvetsera anu komanso kufunika kwa mfundo yaikulu ya nkhani yonseyo. Kaŵirikaŵiri sikukhala kokwanira kungofotokoza lembalo. Muyenera kugwirizanitsa maganizo apalembalo ndi mfundo ya m’mawu anu oyamba oŵerengera lemba. Muyenera kufotokoza mgwirizanowo momveka bwino.

21 Kutanthauzira kwabwino ndi kuja kosavuta, koma kokwaniritsa cholinga chanu. Kuyenera kukhala kopanda mfundo zilizonse zosafunikira. Mungachite chimenecho mwa kuchepetsa mfundo zanu ndi kusiya maumboni oŵerengeka chabe ndiyeno kuwonjezapo mawu ofunikira kuti mfundozo zimveke bwino. Ngati pali mbali ina imene sinayankhidwe m’mawu oyamba poŵerenga lemba, kutanthauzirako kuyenera kupereka yankho.

22 Apa pamene mwafika tsopano m’pologalamu yophunzira kulankhula, cholinga chanu chiyenera kukhala kufeŵetsa nkhani ndi kulankhula molunjika. Pamene mufikira cholingacho, kaŵerengedwe kanu ndi kutanthauzira malemba kudzasonyeza khama lanu monga mphunzitsi waluso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena