Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?
“NDIKUFUNA kuti moyo wanga ukhale wopindulitsa kwambiri.” Mtsikana wina anatero. Mosakayika, inu mukufunanso mutapindula. Koma kodi mungatani kuti moyo wanu ukhale “wopindulitsa kwambiri”? Manyuzipepala, mabuku, wailesi, ma TV ndi anzanu, mwinanso ngakhale aphunzitsi anu anganene kuti mungakhale ndi moyo wopindulitsa kwambiri ngati mukhala ndi ndalama zambiri ndi kugwira ntchito yapamwamba zedi—kukhala ndi mbiri yoti mwachita zazikulu.
Koma Baibulo limachenjeza achinyamata kuti kufunafuna kulemera kapena kutchuka ndi “kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Chifukwa chimodzi n’chakuti ndi achinyamata ochepa okha amene amadzakhaladi olemera ndi otchuka. Komanso nthaŵi zambiri amene amapezadi zimenezi amadzakhumudwa nazo. Wachinyamata wina wa ku Britain amene anaphunzira ntchito yapamwamba anati: “Kulemera ndi kutchuka zili ngati bokosi lopanda kanthu. Ukayang’ana m’katimo, upeza kuti mulibe kanthu.” N’zoona kuti nthaŵi zina ntchito ingakulemeretseni ndi kukhala munthu wolemekezeka. Koma siingakupatseni ‘zosoŵa zanu zauzimu.’ (Mateyu 5:3, NW) Ndiponso, 1 Yohane 2:17 amachenjeza kuti “dziko lapansi lipita.” Ngakhale mulemere ndi kukhala wotchuka m’dziko lino, sizidzakhala nthaŵi yaitali.
N’chifukwa chake Mlaliki 12:1 amalimbikitsa achinyamata kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” Inde, njira yabwino kwambiri imene mungagwiritsire ntchito moyo wanu ndiyo kutumikira Yehova Mulungu. Komabe choyamba mufunika kukhala woyenerera kutumikira Mulungu. Kodi mungayenerere bwanji? Ndipo kodi kutumikira Mulungu kumafuna chiyani?
Zofunika Kuti Mukhale Mboni ya Yehova
Choyamba, muyenera kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu. Sizimangochitika zokha kuti mufune kutumikira Mulungu, ngakhale makolo anu atakhala Akristu. Muyenera kukhala paubale ndi Yehova. Mtsikana wina anati: “Kupemphera kumathandiza kuti ukhale paubale ndi Yehova.”—Salmo 62:8; Yakobo 4:8.
Pa Aroma 12:2 akufotokoza chinthu china chimene mufunika kuchita. Akuti: ‘Zindikirani [“tsimikizirani nokha,” NW] chimene chili chifuno cha Mulungu chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.’ Kodi nthaŵi zina mumakayikira zinthu zimene anakuphunzitsani? Ngati ndi choncho, tsatirani langizo la m’Baibuloli, ndipo “tsimikizirani nokha” kuti zimenezi n’zoona. Fufuzani nokha. Ŵerengani Baibulo ndi mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Komabe, kuphunzira za Mulungu sinkhani yongofufuza mfundo chabe ayi. Khalani ndi nthaŵi yosinkhasinkha zimene mwaŵerenga kuti zikhazikike mumtima wanu wophiphiritsa. Zimenezi zidzakuthandizani kukonda kwambiri Mulungu .—Salmo 1:2, 3.
Chotsatira, yesani kuuza ena pa mpata uliwonse zimene mukuphunzira, mwina anzanu a kusukulu. Kenako, yambani kulalikira kunyumba ndi nyumba. Nthaŵi zina mungakumane ndi mnzanu wa kusukulu pamene mukulalikira, ndipo mwina poyamba mungamangike. Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tisachite manyazi ndi uthenga wabwino.’ (Aroma 1:16) Mukulalikira uthenga wopatsa moyo ndi chiyembekezo. Nanga n’kuchitiranji manyazi?
Tsopano, ngati makolo anu ali Akristu, muyenera kuti mumatsagana nawo muulaliki. Koma kodi mumatha kuchita zambiri osati kungokhala chete pakhomo kapena kungogaŵa magazini ndi mathirakiti basi? Kodi panokha mumalankhula mukafika panyumba ya munthu, kuphunzitsa mwini nyumbayo pogwiritsa ntchito Baibulo? Ngati simutha kuchita zimenezi, pemphani makolo anu kapena Mkristu aliyense wokhwima mwauzimu mumpingo wanu kuti akuthandizeni. Khalani ndi cholinga choti muyenerere kukhala wofalitsa wosabatizidwa wa uthenga wabwino.
Pakapita nthaŵi, mudzalimbikitsidwa kuti mudzipatulire—kulumbira kwa Mulungu kuti mudzam’tumikira kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo. (Aroma 12:1) Komabe, munthu sumangodzipatulira kwa wekha basi ayi. Mulungu amafuna kuti anthu onse ‘avomereze [“alengeze kwa anthu onse,” NW] kutengapo chipulumutso.’ (Aroma 10:10) Panthaŵi ya ubatizo, choyamba mumalengeza chikhulupiriro chanu ndi pakamwa. Kenako mumabatizidwa m’madzi. (Mateyu 28:19, 20) Inde, ubatizo si nkhani ya maseŵera. Koma musasiye kufuna kubatizidwa chifukwa choganiza kuti mwina mudzalephera kukwaniritsa kudzipatulira kwanu. Ngati mudalira Mulungu kuti akupatseni mphamvu, adzakupatsani “ukulu woposa wa mphamvu [“mphamvu zoposa zaumunthu,” NW]” kuti mukhalebe wolimba.—2 Akorinto 4:7; 1 Petro 5:10.
Panthaŵi ya ubatizo, mumakhala mmodzi wa Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10) Zimenezi ziyenera kukhudza kwambiri mmene mungagwiritsire ntchito moyo wanu. Kudzipatulira kumafuna kuti ‘mudzikane nokha.’ (Mateyu 16:24) Mungasiye zolinga ndi zofuna zanu zina ndi ‘kuthanga mwafuna Ufumu wa Mulungu.’ (Mateyu 6:33) Motero, kudzipatulira ndi kubatizidwa zimatsegula mwayi waukulu wochitira zimenezo. Tiyeni tikambirane zina mwa izo.
Mwayi Wosiyanasiyana Wotumikira Mulungu Nthaŵi Zonse
● Upainiya ndi umodzi wa mwayi wautumiki. Mpainiya ndi Mkristu wobatizidwa wachitsanzo chabwino amene amakonza zolalikira uthenga wabwino kwa maola osachepera 70 mwezi uliwonse. Kuthera nthaŵi yaikulu m’munda kudzakuthandizani kukulitsa luso lanu lolalikira ndi kuphunzitsa. Apainiya ambiri apeza chimwemwe chifukwa chothandiza anthu amene amaphunzira nawo Baibulo kukhala Mboni zobatizidwa. Kodi pali ntchito yosangalatsa ndiponso yokhutiritsa ngati kutumikira Mulungu?
Apainiya ambiri amagwira ganyu kuti azipeza zosoŵa pa moyo wawo. Ena amakonzeratu za mmene azidzapezera zosoŵazi mwa kuphunzira ntchito yamanja kusukulu kapena kwa makolo awo. Ngati inu ndi makolo anu mukuona kuti zingakhale bwino kuchita maphunziro ena owonjezera mukamaliza maphunziro a ku sekondale, onetsetsani kuti cholinga chanu sindicho kupeza ndalama zambiri koma kuti maphunzirowo akuthandizeni kutumikira ndiponso mwina kuchita utumiki wanthaŵi zonse.
Komabe, chofunika kwambiri kwa mpainiya si ntchito yake yopezera ndalamayo koma utumiki wake—kuthandiza ena kuti apeze moyo. Bwanji osakhala ndi cholinga chochita upainiya? Upainiya umatsegulanso mpata wochita mautumiki ena. Mwachitsanzo, apainiya ena amapita ku madera kumene kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri. Ena amaphunzira chinenero china ndiyeno n’kumatumikira mumpingo umene amalankhula chinenero chimenecho m’dziko lawo lomwelo kapena amapita kudziko lina. Inde, kuchita upainiya n’kopindulitsa kwambiri!
● Utumiki waumishonale ndi mwayi winanso wautumiki. Kuyambira mu 1943, Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo yaphunzitsa bwino apainiya oyenerera kuti akhale amishonale. Omaliza maphunziro aumishonale amawatumiza kudziko lina kukakhala ofalitsa a nthaŵi zonse. Kumayiko ambiri kumene amapita, kakhalidwe n’kovutirapo, motero amishonale amafunika kukhala a thanzi labwino ndiponso amphamvu. Ngakhale izi zili choncho, amishonale amasangalala ndiponso kukhutira ndi moyo wawo.
● Sukulu Yophunzitsa Utumiki anaikhazikitsa kuti iziphunzitsa akulu ndi atumiki otumikira oyenerera omwe sanakwatire. Kosiyi yomwe amaphunzira mwakathithi kwa milungu isanu ndi iŵiri, imakhudza maudindo a akulu ndi atumiki otumikira, kulinganiza zinthu, ndi kulankhula pamaso pa anthu. Akamaliza maphunzirowo, ena amatumikira m’dziko lawo lomwelo. Ena amawapempha kukatumikira m’mayiko ena.
● Utumiki wa pa Beteli ndi utumiki umene munthu amadzipereka kutumikira pa nthambi ya Mboni za Yehova. Ena a m’banja la Beteli amagwira ntchito yopanga mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Ena amagwira ntchito zina zothandizira ntchito yopanga mabuku, monga kukonza nyumba ndi zipangizo zikawonongeka kapena kusamalira banja la Beteli. Ntchito zonsezi ndi mwayi wautumiki wopatulika kwa Yehova. Ndiponso, amene ali pa Beteli amasangalala kudziŵa kuti zimene akuchita zikupindulitsa abale awo ambirimbiri padziko lonse.
Nthaŵi zina amene amawaitana kukatumikira pa Beteli amakhala abale amene akudziŵa ntchito inayake yapadera. Komabe, ambiri amaphunzira atafika pa Beteli. Amene ali pa Beteli satumikira chifukwa chofuna phindu lakuthupi, m’malo mwake amakhutira ndi chakudya chimene amalandira, malo ogona, ndiponso kandalama kochepa kopezera zosoŵa zazing’ono. Wachinyamata wina yemwe ali pa Beteli anafotokoza za utumiki wake kuti: “Ndi utumiki wosangalatsa kwambiri. Ndandanda ya zimene timachita siyophweka, koma ndapindula kwambiri chifukwa chotumikira pano.”
● Utumiki wa m’mayiko osiyanasiyana umathandiza munthu kugwira nawo ntchito yomanga nthambi ndi Nyumba za Ufumu. Atumiki ogwira ntchito m’mayiko osiyanasiyana, lomwe ndilo dzina lawo, amapita ku mayiko ena kukathandiza ntchito yomanga imeneyo. Umenewu ndi utumiki wina wopatulika, wofanana ndi ntchito imene anagwira anthu omwe anamanga kachisi wa Solomo. (1 Mafumu 8:13-18) Atumiki ogwira ntchito m’mayiko osiyanasiyana ameneŵa amasamalidwa mofanana ndi a m’banja la Beteli. Ndi mwayi waukulutu umene abale ndi alongo ameneŵa ali nawo, kutumikira m’ntchito imeneyi yotamanda Yehova!
Tumikirani Yehova ndi Mtima Wonse
Njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito moyo wanu ndiyo kutumikira Yehova. Bwanji osakhala ndi cholinga chotumikira Mulungu nthaŵi yonse? Kambiranani za utumiki wanthaŵi zonse ndi makolo anu, akulu a mpingo wanu, ndi woyang’anira dera wanu. Ngati mukufuna ku Beteli, ku Gileadi, kapena ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, khalani nawo pa msonkhano wa anthu ofuna kufunsira kupita ku malo ameneŵa umene umachitika pa msonkhano wadera ndi wachigawo.
N’zoona kuti si onse amene angayenerere kapena angathe kuchita utumiki wanthaŵi zonse. Nthaŵi zina matenda, mavuto a zachuma, ndi udindo wa m’banja zimalepheretsa munthu kuchita zambiri. Ngakhale zili choncho, Akristu onse odzipatulira ayenera kumvera lamulo la m’Baibulo lakuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:37) Yehova amafuna kuti muchite zonse zimene mungathe malinga ndi mmene zinthu zilili kwa inu. Motero, kaya zinthu zili motani, kutumikira Yehova kukhale cholinga chanu chachikulu m’moyo. Khalani ndi zolinga zimene mungazikwanitse mu utumiki wanu kwa Mulungu. Inde, ‘kumbukirani Mlengi wanu m’masiku a unyamata wanu,’ ndipo mukatero, mudzapindula mpaka muyaya.
Malemba m’thirakiti lino akuchokera m’Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version, kusiyapo ngati tasonyeza Baibulo lina. Komabe Chinyanjacho tachilemba m’kalembedwe kamakono.