Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • od mutu 10 tsamba 105-115
  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu
  • Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUKHALA WOFALITSA PA MPINGO
  • KUTUMIKIRA KUMENE KUKUFUNIKIRA OFALITSA AMBIRI
  • KULALIKIRA KWA ANTHU ACHINENERO CHINA
  • UPAINIYA
  • UMISHONALE
  • KUYANG’ANIRA DERA
  • SUKULU ZOPHUNZITSA BAIBULO
  • KUTUMIKIRA PA BETELI
  • NTCHITO YA ZOMANGAMANGA
  • KODI INUYO MULI NDI ZOLINGA ZOTANI ZAUZIMU?
  • Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?
    Achinyamata—Kodi Moyo Wanu Mudzaugwiritsa Ntchito Bwanji?
  • Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
od mutu 10 tsamba 105-115

Mutu 10

Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu

PAMENE Yesu ankatumiza ophunzira ake kuti akalalikire za Ufumu, anawauza kuti: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.” Panali ntchito yambiri yoti agwire, n’chifukwa chake anawauzanso kuti: “Pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Yesu anawauzanso mmene angagwirire ntchito yolalikirayo. Pofuna kusonyeza kuti ntchitoyi ikufunika kugwiridwa mwamsanga kwambiri, iye ananena kuti: “Simudzamaliza kuzungulira mizinda yonse ya Isiraeli Mwana wa munthu asanafike.”​​​​—Mat. 10:23.

2 Masiku anonso pali ntchito yaikulu kwambiri yoti igwiridwe chifukwa mapeto ayandikira koma uthenga wabwino wa Ufumu ukufunika ulalikidwe mapeto asanafike. (Maliko 13:10) Popeza ntchitoyi ikufunika kugwiridwa padziko lonse lapansi, nafenso ikutikulira ngati mmene zinalili kwa Yesu ndi ophunzira ake. Tilipo anthu ochepa tikayerekezera ndi anthu ambirimbiri amene ali padziko lapansili, komabe sitiyenera kukayikira zoti Yehova atithandiza. Uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwa padziko lonse lapansi ndipo mapeto adzafika pa nthawi yake. Kuti tikwanitse utumiki umene tapatsidwa, tikufunika kuika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba pa moyo wathu. Koma kodi ndi zolinga ziti zimene zingakuthandizeni kuika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba?

3 Pofotokoza zimene Yehova amafuna kwa atumiki ake, Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Yehova amafuna kuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse. Izi zikutanthauza kuti tiyenera kuchita khama kwambiri potumikira Yehova kusonyeza kuti tinadzipereka ndi mtima wonse. (2 Tim. 2:15) Pali utumiki wosiyanasiyana umene tingachite mogwirizana ndi luso lathu komanso mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Taonani mautumiki ena amene mungachite komanso zolinga zauzimu zimene mungakhale nazo pochita utumiki wanu.

KUKHALA WOFALITSA PA MPINGO

4 Aliyense amene waphunzira choonadi amakhala ndi udindo wofalitsa uthenga wabwino. Imeneyi ndi ntchito yaikulu imene Yesu anapatsa ophunzira ake. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Wophunzira wa Yesu Khristu akangomva uthenga wabwino, nthawi yomweyo amayamba kuuzanso ena. Izi ndi zimene Andireya, Filipo, Koneliyo ndi ena anachita. (Yoh. 1:40, 41, 43-45; Mac. 10:1, 2, 24; 16:14, 15, 25-34) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthu akhoza kuuza ena uthenga wabwino ngakhale asanabatizidwe? Inde, munthu akangokhala wofalitsa wosabatizidwa ndiye kuti angayambe kulalikira nawo kunyumba ndi nyumba. Ndiponso angathe kumalalikira m’njira zina mogwirizana ndi luso lake komanso mmene zinthu zilili pa moyo wake.

5 Wofalitsa akabatizidwa, amafunitsitsa kuchita zonse zomwe angathe pofotokozera anthu ena za uthenga wabwino. Onse mumpingo, abale komanso alongo, ali ndi mwayi wogwira nawo ntchito yolalikira. Ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchito yopititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu. Munthu aliyense amene amawonjezera utumiki wake amasangalala kwambiri.

KUTUMIKIRA KUMENE KUKUFUNIKIRA OFALITSA AMBIRI

6 Zikhoza kutheka kuti gawo la mpingo wanu limalalikidwa pafupipafupi ndipo anthu ambiri amakhala ndi mwayi womva uthenga wabwino. Ngati zili choncho mukhoza kuona kuti ndi bwino kusamukira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri kuti muwonjezere utumiki wanu. (Mac. 16:9) Ngati ndinu mkulu kapena mtumiki wothandiza, dziwani kuti pakhoza kukhala mipingo imene ikufunikira thandizo lanu. Woyang’anira dera wanu angakudziwitseni za mpingo umene mukhoza kukathandiza m’dera lanulo. Ngati mukufuna kukatumikira kudera lina la m’dziko lanu lomwelo mungafunse ku ofesi ya nthambi.

7 Kodi mukufuna kukatumikira m’dziko lina? Ngati ndi choncho, mufunika kuganizira mofatsa za nkhaniyi. Ndipo mungachite bwino kukambirana nkhaniyi ndi akulu a mpingo wanu. Kusamukira kudziko lina kudzasintha kwambiri moyo wanu komanso wa anthu amene mungasamuke nawo limodzi. (Luka 14:28) Koma ngati mukuona kuti simungakwanitse kukhala m’dziko lina kwa nthawi yaitali, mungachite bwino kuganizira zongotumikira m’dera lina la m’dziko lanu lomwelo.

8 M’mayiko ena, abale amene amaikidwa pa udindo woyang’anira amakhala kuti aphunzira kumene choonadi. Abale odzichepetsa a m’mipingo yotere amakhala okonzeka kulola kuti akulu amene asamukira mumpingowo ndipo akhala akutumikira kwa nthawi yaitali azitsogolera pochita zinthu. Ngati ndinu mkulu ndipo mukuganiza zosamukira m’dziko loterolo, muyenera kudziwa kuti cholinga chanu si chokalanda udindo abale a m’dzikolo. Muyenera kutumikira nawo limodzi. Alimbikitseni abale a mumpingowo kukhala ndi mtima wofuna kutumikira. (1 Tim. 3:1) Muyenera kudekha ngati zinthu zina sizikuchitika ngati mmene zimachitikira kwanu. Afotokozereni abalewo mfundo zothandiza zimene mwaphunzira pa nthawi imene mwakhala mukutumikira ngati mkulu. Luso limeneli lingadzathandize abalewo kupitiriza kusamalira mpingowo inu mutabwerera kudziko lanu.

9 Ofesi ya nthambi idzakupatsani mayina a mipingo imene ikufunika thandizo pambuyo poti yalandira kalata yokuvomerezani yochokera ku Komiti ya Utumiki ya Mpingo wanu. Kalata imeneyi ndi yofunikirabe kaya mukutumikira ngati mkulu, mtumiki wothandiza, mpainiya kapena wofalitsa. Komiti ya Utumiki idzatumiza kalatayi limodzi ndi kalata yanu ku ofesi ya nthambi ya m’dziko limene mukufuna kukatumikiralo.

KULALIKIRA KWA ANTHU ACHINENERO CHINA

10 Kuti muwonjezere utumiki wanu, mukhoza kuphunzira chinenero china, kuphatikizapo chinenero chamanja. Ngati mukufuna kuphunzira chinenero china ndi cholinga choti muzilalikira m’chinenerocho, mungachite bwino kukambirana ndi akulu komanso woyang’anira dera. Iwo angakupatseni malangizo oyenerera komanso kukulimbikitsani. Ofesi ya nthambi imatha kukonza zoti m’madera ena muchitike sukulu zophunzitsa chinenero ofalitsa komanso apainiya kuti azitha kulalikira m’chinenerocho.

UPAINIYA

11 Ofalitsa onse ayenera kudziwa bwino zimene zimafunika kuti munthu akhale mpainiya wothandiza, wokhazikika, wapadera kapenanso kuti achite utumiki wina wa nthawi zonse. Mpainiya ayenera kukhala wofalitsa wobatizidwa wachitsanzo chabwino yemwe akhoza kumakwanitsa maola ofunikira. Komiti ya Utumiki ya Mpingo ndi yomwe imavomereza anthu amene akufuna kukhala apainiya othandiza kapena okhazikika, pomwe apainiya apadera amaikidwa ndi ofesi ya nthambi.

12 Wofalitsa angapemphe kuchita upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi, miyezi ingapo yotsatizana kapena mongopitiriza malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake. Ofalitsa ambiri amakonda kuchita upainiya wothandiza pa nthawi ya zochitika zapadera, monga Chikumbutso kapena mwezi umene woyang’anira dera akuchezera mpingo wawo. Enanso amasankha kuchita upainiya wothandiza pamene ali pa holide. Ofalitsa achinyamata obatizidwa amene ali pa sukulu angachitenso upainiya wothandiza pa nthawi yawo ya holide. Ofalitsa angasankhe kuchita upainiya wa maola ochepa m’miyezi ya March ndi April komanso m’mwezi umene woyang’anira dera akuchezera mpingo wawo. Mulimonse mmene zilili pa moyo wanu, ngati muli Mkhristu wachitsanzo chabwino, ngati mungathe kukwanitsa maola ofunikira ndiponso ngati mwapempha kuchita upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo, akulu adzakuvomerezani kuchita utumiki umenewu.

13 Mungaikidwe kukhala mpainiya wokhazikika, ngati mukuoneka kuti mungakwanitse maola ofunikira pa chaka. Monga mpainiya wokhazikika, mudzafunika kuyesetsa kumalalikira limodzi ndi mpingo wanu. Mpingo umadalitsidwa kwambiri ngati apainiya akuchita utumiki wawo mwakhama chifukwa zimathandiza kuti anthu enanso azilimbikira utumiki wakumunda. Zikhoza kuthandizanso kuti ena ayambe upainiya. Koma kuti mukhale mpainiya wokhazikika, muyenera kukhala wofalitsa wachitsanzo chabwino ndipo payenera kukhala patadutsa miyezi yosachepera 6 kuchokera pamene munabatizidwa.

14 Nthawi zambiri apainiya apadera amasankhidwa kuchokera pa apainiya okhazikika aluso komanso akhama mu utumiki. Ayenera kukhala okonzeka kukatumikira kulikonse kumene ofesi ya nthambi ingawatumize. Nthawi zambiri amatumizidwa m’madera akutali kumene kukhoza kupezeka anthu achidwi ndipo kungakhazikitsidwe mipingo. Nthawi zina apainiya apaderawa amatumizidwa kumipingo imene ikufunika kuthandizidwa kulalikira gawo lawo lonse. Apainiya ena apadera omwe ndi akulu amatumizidwa kuti akathandize mipingo ing’onoing’ono, ngakhale zitakhala kuti mipingoyo sikufunikira kuthandizidwa kulalikira gawo la mpingo wawo. Apainiya apadera amalandira kandalama kochepa kowathandiza kupeza zofunika pa moyo wawo. Ena amapemphedwa kuchita upainiya wapadera wakanthawi.

UMISHONALE

15 Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira ndi imene imasankha anthu kuti akhale amishonale. Kenako Komiti ya Nthambi ya m’dziko limene atumizidwalo imawatumiza kudera kumene kuli anthu ambiri. Utumiki umene amishonale amachita umathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira komanso kulimbikitsa mpingo. Nthawi zambiri anthu amene amachita utumikiwu amakhala oti analowa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Amishonale amalandira kandalama kochepa kowathandiza kupeza zofunika pa moyo wawo.

KUYANG’ANIRA DERA

16 Abale omwe amaikidwa ndi Bungwe Lolamulira kuti aziyang’anira madera, amakhala aluso komanso odziwa bwino ntchito yawo chifukwa amayamba kaye atumikira ngati oyang’anira madera ogwirizira asanapatsidwe madera awoawo. Abalewa amakonda kwambiri utumiki ndiponso Akhristu anzawo. Amakhalanso apainiya akhama, ophunzira Baibulo mwakhama ndiponso aluso pokamba nkhani ndiponso pophunzitsa. Amakhala anthu omwe ndi achitsanzo chabwino posonyeza makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa ndipo zochita zawo zimasonyeza kuti ndi oganiza bwino komanso ozindikira. Ngati ali wokwatira, mkazi wake ayenera kukhala mpainiya wachitsanzo chabwino komanso wotha kukhala bwino ndi ena. Mkaziyo ayeneranso kukhala waluso polalikira. Ayeneranso kukhala wogonjera mwamuna wake, osati wofulumira kuyankha pa nkhani zoyenera kusamalidwa ndi mwamuna wake kapenanso kumangolankhula yekha akamacheza ndi anthu ena. Oyang’anira dera limodzi ndi akazi awo amakhala ndi zochita zambiri, choncho anthu amene akufuna kuchita utumiki umenewu ayenera kukhala ndi thanzi labwino. Apainiya amene akufuna kukhala oyang’anira dera sachita kupempha utumikiwu. M’malomwake, amangofotokoza maganizo awo kwa woyang’anira dera ndipo iye amawauza zoyenera kuchita.

SUKULU ZOPHUNZITSA BAIBULO

17 Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu: Pakufunika anthu ambiri oti azilalikira m’madera amene salalikidwa pafupipafupi ndiponso kuti azithandiza mipingo. Choncho, abale ndi alongo omwe sali pa banja komanso omwe ali pa banja akhoza kufunsira kuti alowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu ndipo kusukuluyi amaphunzitsidwa mmene angachitire utumiki wawo. Akamaliza sukuluyi, abale ndi alongowo amatha kutumizidwa kukatumikira ngati apainiya okhazikika m’madera omwe mukufunika olalikira ambiri m’dziko lawo lomwelo. Komabe anthu amene akufuna kuwonjezera utumiki wawo akhoza kupatsidwa utumiki wina m’dziko lawo lomwelo kapena dziko lina. Ena ochepa akhoza kuikidwa kukhala apainiya apadera kapena apainiya apadera akanthawi. Apainiya amene akufuna kulowa sukuluyi angadziwe zambiri ngati atapezeka pa msonkhano wa ofuna kulowa sukuluyi umene umachitika pa nthawi ya msonkhano wachigawo.

18 Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo: Abale osakwatira, alongo osakwatiwa, ndiponso anthu a pa banja amene amasankhidwa kuti akalowe nawo sukuluyi amakhala oti amadziwa kulankhula Chingelezi ndipo amakhalanso kuti ndi atumiki a nthawi zonse apadera. Amakhala abale ndi alongo amene akuoneka kuti angathandize kulimbikitsa mipingo kapena kuyendetsa bwino ntchito za pa ofesi ya nthambi. Amakhalanso atasonyeza kuti amakonda kutumikira abale ndi alongo awo komanso kuwathandiza kutsatira mfundo za m’Malemba ndi malangizo a gulu. Komiti ya Nthambi ndi yomwe imavomereza abale ndi alongo omwe angalowe sukuluyi. Abale ndi alongowa akamaliza maphunziro awo, amatumizidwa kukatumikira m’mipingo kapena pa ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo lomwelo kapena ya m’dziko lina.

KUTUMIKIRA PA BETELI

19 Kutumikira pa Beteli ndi mwayi waukulu kwambiri. Dzina lakuti Beteli limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Dzinali n’loyeneradi chifukwa ntchito zonse zimene zimachitika pamalowa n’zokhudza Ufumu wa Mulungu. Abale ndi alongo amene amatumikira pa Beteli amagwira ntchito yofunika kwambiri yokhudzana ndi kupanga, kumasulira ndiponso kutumiza mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Bungwe Lolamulira, lomwe limayang’anira mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse, limayamikira kwambiri ntchito imene abale ndi alongowa amagwira. Abale ndi alongo ambiri omwe amagwira ntchito yomasulira mabuku amakhala m’madera amene chinenero chomwe amamasuliracho chimalankhulidwa. Zimenezi zimathandiza kuti azimvetsera mmene anthu akulankhulira tsiku ndi tsiku. Amathanso kuona mosavuta ngati anthu amamva bwinobwino akamawerenga mabuku amene amamasulira.

20 Ntchito zambiri zimene zimachitika pa Beteli zimafuna anthu amphamvu. N’chifukwa chake nthawi zambiri amene amaitanidwa kuti akatumikire pa Beteli amakhala abale achinyamata odzipereka, omwe ndi obatizidwa, athanzi labwino komanso amphamvu. Ngati ofesi ya nthambi imene imayang’anira dziko lanu ikufuna anthu oti akatumikire pa Beteli ndipo inuyo mukufuna kukatumikira, mungadziwe zimene zimafunika kuti muchite utumikiwu kuchokera kwa akulu a mumpingo wanu.

NTCHITO YA ZOMANGAMANGA

21 Kugwira ntchito yomanga malo kapena nyumba zimene gulu limagwiritsa ntchito ndi utumiki wopatulika ngati mmene zinalili ndi ntchito yomanga kachisi wa Solomo. (1 Maf. 8:13-18) Abale ndi alongo ambiri amasonyeza kuti ndi odzipereka chifukwa amalolera kugwiritsa ntchito nthawi yawo komanso chuma chawo kuti agwire ntchito imeneyi.

22 Kodi mungathandize nawo pa ntchito imeneyi? Ngati ndinu wofalitsa wobatizidwa ndipo mukufuna kugwira nawo ntchitoyi, abale amene amayang’anira ntchito yomanga m’dera lanu adzayamikira kwambiri thandizo lanu ndipo ndi okonzeka kukuthandizani ngati simukudziwa zambiri pa ntchito yomanga. Mungachite bwino kudziwitsa akulu zoti mukufuna kuthandiza nawo pa ntchitoyi. Ofalitsa ena obatizidwa omwe ndi oyenerera amatha kudzipereka kupita m’mayiko ena kukagwira nawo ntchito yomanga malo komanso nyumba zimene gulu limagwiritsa ntchito.

23 Gulu likufuna anthu ambiri oti azigwira ntchito zomangamanga. Ofalitsa achitsanzo chabwino omwe ali ndi luso ndipo angathe kuthandiza ntchito zomanga zomwe zikuchitika m’dera lawolo akhoza kutumikira monga Othandiza pa Ntchito ya Zomangamanga M’dera Lawo. Ena amakhala kuti akhoza kukathandiza kwakanthawi pa ntchito zomanga m’madera akutali ndipo amaikidwa ndi ofesi ya nthambi kukhala Ongodzipereka Kuchita Utumiki wa Zomangamanga. Anthu amenewa angapemphedwe kukathandiza ntchito yomanga kuyambira pa milungu iwiri mpaka miyezi itatu. Anthu amene angapemphedwe kugwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali kuposa pamenepa amatchedwa Ochita Utumiki wa Zomangamanga. Munthu wochita utumiki wa zomangamanga amene amatumizidwa kukagwira ntchitoyi m’dziko lina amadziwika kuti Wogwira Ntchito ya Zomangamanga Wochokera Dziko Lina. Gulu la Zomangamanga lomwe limapangidwa ndi anthu ochita utumiki wa zomangamanga komanso ongodzipereka kuchita utumiki wa zomangamanga ndi limene limatsogolera ntchito zonse zomanga. Gululi limathandizidwa ndi Othandiza pa Ntchito ya Zomangamanga M’dera Lawo ndiponso abale ndi alongo ochokera m’mipingo ya m’deralo. Magulu a Zomangamanga akamaliza kumanga, amasamukira kudera lina kumene kuli ntchito ina m’gawo la nthambi yawo.

KODI INUYO MULI NDI ZOLINGA ZOTANI ZAUZIMU?

24 Ngati munadzipereka kwa Yehova ndiye kuti cholinga chanu chachikulu ndi kumutumikira mpaka kalekale. Koma kodi muli ndi zolinga zilizonse pa utumiki wanu? Kukhala ndi zolinga zauzimu kudzakuthandizani kuti muzigwiritsa ntchito mwanzeru mphamvu zanu komanso chuma chanu. (1 Akor. 9:26) Zolinga zauzimuzi zidzakuthandizani kuti mukule mwauzimu komanso kuti maganizo anu onse azikhala pa zinthu zaphindu, zomwe zingachititsenso kuti muyenerere utumiki wina wowonjezera.​—Afil. 1:10; 1 Tim. 4:15, 16.

25 Mtumwi Paulo anatipatsa chitsanzo chabwino chimene tingatsatire pamene tikutumikira Mulungu. (1 Akor. 11:1) Paulo anatumikira Yehova modzipereka kwambiri. Anazindikira kuti Yehova wamupatsa mwayi wambiri wautumiki, n’chifukwa chake analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Khomo lalikulu la mwayi wautumiki landitsegukira.” Kodi si zoona kuti nafenso khomo lalikulu la mwayi wautumiki latitsegukira? Panopa tili ndi mwayi wambiri wotumikira Yehova limodzi ndi mpingo, makamaka pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Komabe mofanana ndi Paulo, kuti tidutse pa “khomo lalikulu” limeneli tikufunika kulimbana ndi “otsutsa ambiri.” (1 Akor. 16:9) Paulo ankayesetsa kulamulira thupi lake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo.” (1 Akor. 9:24-27) Kodi ndi zimene nafenso tikuyesetsa kuchita?

Kukhala ndi zolinga zauzimu kudzakuthandizani kuti muzigwiritsa ntchito mwanzeru mphamvu zanu komanso chuma chanu

26 Aliyense akulimbikitsidwa kuyesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu zimene ali nazo mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake. Anthu ambiri akuchita utumiki wa nthawi zonse chifukwa chakuti anali ndi zolinga zimenezi ali achinyamata. Kuyambira ali ana, makolo awo komanso anthu ena ankawalimbikitsa kuchita utumiki wa nthawi zonse. Zimenezi zathandiza kuti azisangalala potumikira Yehova ndipo samaona kuti analakwitsa kusankha ntchito imeneyi. (Miy. 10:22) Tikhozanso kukhala ndi zolinga zolowa nawo mu utumiki mlungu uliwonse, kuyambitsa phunziro la Baibulo kapena kuwonjezera nthawi imene timakonzekera misonkhano. Chofunika kwambiri ndi kukhalabe okhulupirika ndiponso kuyesetsa kukwaniritsa utumiki wathu. Tikamachita zimenezi, tidzalemekeza Yehova komanso tidzakwaniritsa cholinga chathu chachikulu chomwe ndi kumutumikira mpaka kalekale.​​​​—Luka 13:24; 1 Tim. 4:7b, 8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena