Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w12 9/15 tsamba 13-17
  • Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
  • Nsanja ya Olonda—2012
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • PINDULANI NDI MAPHUNZIRO OCHOKERA KWA MULUNGU
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Kodi Mukuchita Zonse Zimene Mungathe Kuti Muphunzire Zambiri Kwa Yehova?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Sukulu Imene Ophunzira Ake Amathandiza Anthu Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2012
w12 9/15 tsamba 13-17

Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

YEHOVA ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu.’ (Yes. 30:20) Iye amaphunzitsa ena chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, chifukwa choti Yehova amakonda kwambiri Yesu, ‘amamuonetsa zonse zimene iye akuchita.’ (Yoh. 5:20) Iye amatikondanso ndipo n’chifukwa chake amatipatsa “lilime la anthu ophunzitsidwa bwino” pamene tikuyesetsa kumulemekeza komanso kuthandiza anthu ena.—Yes. 50:4.

Potsanzira chikondi cha Yehova, Bungwe Lolamulira lakonza sukulu zokwana 10. Lachita zimenezi kudzera m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa. Sukulu zimenezi zimaphunzitsa anthu ofunitsitsa kuphunzira ndiponso amene angakwanitse. Kodi inuyo mumaona kuti sukulu zimenezi ndi umboni woti Yehova amatikonda?

Tiyeni tione sukulu zimenezi ndiponso ndemanga zimene anthu amene alowa sukuluzi anena. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo ndingatani kuti ndipindule ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu amenewa?’

PINDULANI NDI MAPHUNZIRO OCHOKERA KWA MULUNGU

Yehova ndi “Mulungu wachikondi” ndipo amatiphunzitsa kuti tizikhala ndi moyo wosangalala. Amatithandiza kuti tizithana ndi mavuto komanso kuti tizisangalala mu utumiki wathu. (2 Akor. 13:11) Mofanana ndi ophunzira oyamba a Yesu, ndife oyenera kuthandiza ena ndiponso “kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse” zimene talamulidwa.—Mat. 28:20.

Ngakhale kuti sitingalowe sukulu zonsezi, tikhoza kulowa imodzi kapena zingapo. Tikhozanso kugwiritsa ntchito mfundo zimene timaphunzira. Kulalikira limodzi ndi atumiki a Yehova amene aphunzitsidwa bwino kungatithandizenso kuti tiziphunzitsa mogwira mtima.

Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi sukulu iti imene ineyo ndingalowe?’

Atumiki a Yehova amaona kuti ndi mwayi kuphunzira m’sukulu zofunikazi. Tikukhulupirira kuti maphunziro amenewa akuthandizani kuyandikira kwambiri Mulungu. Akuthandizaninso kumutumikira bwino makamaka pa ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino.

SUKULU ZOPHUNZITSA ATUMIKI A MULUNGU

Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Cholinga: Kuphunzitsa ofalitsa kuti azilalikira ndiponso kuphunzitsa mogwira mtima uthenga wabwino.

Nthawi: Siitha.

Malo: Pa Nyumba ya Ufumu.

Oyenera Kulowa: Onse amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse omwe amavomereza zimene Baibulo limaphunzitsa komanso amayesetsa kutsatira mfundo za m’Malemba.

Kulembetsa: Woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi amene amalemba anthu.

Mlongo Sharon yemwe akudwala matenda amene anapha ziwalo zake anati: “Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yandiphunzitsa kufufuza zinthu ndiponso kuzifotokoza motsatirika. Yandithandizanso kuti ndisamangoganizira za ine ndekha koma kuganizira za mmene ndingathandizire ena kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.”

M’bale Arnie yemwe wakhala woyang’anira woyendayenda kwa nthawi yaitali anati: “Ndili mnyamata ndinali wachibwibwi ndipo sindinkayang’ana anthu ndikamalankhula nawo. Koma sukuluyi yandithandiza kuti ndisamadzikayikire. Kudzera m’sukuluyi, Yehova wandithandiza kudziwa kupuma bwino polankhula ndiponso kuika maganizo pa zimene ndikuchita. Ndimasangalala kwambiri kuti panopa ndimatha kutamanda Mulungu mu mpingo ndiponso mu utumiki.”

Sukulu ya Otumikira pa Beteli Atsopano

Cholinga: Kuthandiza amene angofika kumene pa Beteli kuti azichita bwino utumiki wawo.

Nthawi: Mphindi 45 mlungu uliwonse kwa milungu 16.

Malo: Ku Beteli.

Oyenera Kulowa: Munthu amene akutumikira pa Beteli nthawi zonse kapena amene wavomerezedwa kutumikira kwa chaka chimodzi kapena zingapo pa Beteli.

Kulembetsa: Anthu onse atsopano pa Beteli amalowa sukuluyi.

M’bale Demetrius amene analowa sukuluyi m’ma 1980 anati: “Sukuluyi inandithandiza kuti ndiziphunzira bwino Baibulo ndiponso kuti ndikhale wokonzeka kutumikira nthawi yaitali pa Beteli. Alangizi ake, maphunziro ake ndiponso malangizo amene tinkapatsidwa zinandithandiza kuona kuti Yehova amandikonda ndiponso amafuna kuti ndizichita bwino utumiki wa pa Beteli.”

Mlongo Kaitlyn anati: “Sukuluyi inandithandiza kudziwa kuti chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Yandithandizanso kuti ndiziyamikira kwambiri Yehova, nyumba yake ndiponso gulu lake.”

Sukulu ya Utumiki wa Ufumu

Cholinga: Kuphunzitsa oyang’anira oyendayenda, akulu ndiponso nthawi zina atumiki othandiza kuti azichita bwino utumiki wawo. (Mac. 20:28) Amathandizidwa kudziwa zinthu zatsopano komanso mmene angathandizire abale ndi alongo malinga ndi mmene zinthu zikusinthira m’dzikoli. Imachitika pakapita zaka zingapo ndipo Bungwe Lolamulira ndi limene limakonza kuti ichitike.

Nthawi: Oyang’anira oyendayenda amaphunzira masiku awiri kapena awiri ndi hafu. Akulu amaphunzira tsiku limodzi ndi hafu ndipo atumiki othandiza amaphunzira tsiku limodzi.

Malo: Pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Nyumba ya Msonkhano.

Oyenera Kulowa: Oyang’anira oyendayenda, akulu kapena atumiki othandiza.

Kulembetsa: Woyang’anira dera amauza akulu ndi atumiki othandiza za sukuluyi ndipo ofesi ya nthambi ndi imene imauza oyang’anira oyendayenda.

M’bale Quinn (amene ali m’munsiyu) anati: “Ngakhale kuti amaphunzira zinthu zambiri nthawi yochepa, sukuluyi imalimbikitsa akulu ndiponso kuwathandiza kukhalabe achimwemwe komanso ‘kupitiriza kuchita chamuna’ potumikira Yehova. Akulu atsopano ndiponso amene atumikira nthawi yaitali amaphunzira mmene angawetere nkhosa komanso kukhala ndi ‘maganizo amodzi.’”

M’bale Michael anati: “Sukuluyi imatithandiza kuchita zinthu mosapitirira malire, imatichenjeza za zinthu zoopsa ndiponso imatidziwitsa mmene tingasamalirire nkhosa. Kunena zoona, Yehova amatithandiza mokoma mtima.”

Sukulu ya Utumiki Waupainiya

Cholinga: Kuthandiza apainiya kuti ‘akwaniritse mbali zonse za utumiki wawo.’—2 Tim. 4:5.

Nthawi: Milungu iwiri.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha koma nthawi zambiri imachitikira ku Nyumba ya Ufumu.

Oyenera Kulowa: Amene achita upainiya wokhazikika kwa chaka chimodzi kapena kuposerapo.a

Kulembetsa: Apainiya oyenerera amadziwitsidwa ndi woyang’anira dera.

Mlongo Lily (yemwe ali kumanjayu) anati: “Sukulu imeneyi yandithandiza kuti ndizithana ndi mavuto mu utumiki komanso pa moyo wanga. Panopa, ndasintha mmene ndimaphunzirira Baibulo ndiponso mmene ndimaphunzitsira ena. Ndine wokonzeka kuthandiza ena, kuchita zinthu mogwirizana ndi akulu ndiponso kuthandiza mpingo wonse kuti ukule.”

Brenda amene walowa sukuluyi kawiri anati: “Sukulu imeneyi yandithandiza kuti ndizikonda kwambiri choonadi, kulimbitsa chikumbumtima changa ndiponso kuti ndizikonda kuthandiza ena. Kunena zoona, Yehova ndi wabwino.”

a Ngati apainiya ndi ochepa m’deralo, apainiya ena amene analowa sukuluyi zaka 5 zapitazo angaitanidwenso.

Sukulu ya Akulu

Cholinga: Kuthandiza akulu kuti azigwira bwino ntchito yawo mu mpingo komanso azikonda kwambiri Yehova.

Nthawi: Masiku asanu.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha. Koma nthawi zambiri imachitikira pa Nyumba ya Ufumu kapena Nyumba ya Msonkhano.

Oyenera Kulowa: Akulu

Kulembetsa: Ofesi ya nthambi ndi imene imadziwitsa akuluwo.

Tamvani zimene ananena akulu amene analowa kalasi ya nambala 92 ku United States.

“Sukuluyi yandithandiza kwambiri chifukwa yandilimbikitsa kudzifufuza komanso kuona mmene ndingasamalirire nkhosa za Yehova.”

“Panopa ndine wokonzeka kulimbikitsa aliyense pofotokoza mfundo zikuluzikulu za m’Malemba.”

“Mfundo zimene ndaphunzirazi zindithandiza moyo wanga wonse.”

Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda ndi Akazi Awo

Cholinga: Kuthandiza oyang’anira madera ndi oyang’anira zigawo kuti azigwira bwino ntchito zawo akamatumikira mipingo ndiponso kuti ‘azichita khama polankhula ndi kuphunzitsa.’—1 Tim. 5:17; 1 Pet. 5:2, 3.

Nthawi: Miyezi iwiri.

Malo: Imasankha ndi ofesi ya nthambi.

Oyenera Kulowa: M’bale yemwe ndi woyang’anira dera kapena woyang’anira chigawo.

Kulembetsa: Ofesi ya nthambi ndi imene imaitana oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo.

M’bale Joel, amene analowa kalasi yoyamba mu 1999, anati: “Tinathandizidwa kumvetsa zimene Yesu akuchita potsogolera gulu. Tinaona kuti m’pofunika kulimbikitsa abale amene timawatumikira ndiponso kulimbikitsa mgwirizano mu mpingo. Sukuluyi inatithandiza kudziwa kuti ngakhale kuti oyang’anira oyendayenda amafunika kupereka malangizo ndiponso kukonza zinthu zina, cholinga chawo chachikulu ndi kuthandiza abale kuona kuti Yehova amawakonda.”

Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira

Cholinga: Kukonzekeretsa abale osakwatira amene ndi akulu ndi atumiki othandiza kuti athe kusamalira maudindo ena m’gulu. Abale ambiri akamaliza amatumizidwa kumadera amene kukufunika thandizo m’dziko lawo. Ena amatumizidwa kudziko lina ngati angakwanitse. Ena amakhala apainiya apadera akanthawi m’madera akumidzi kumene ofalitsa ndi ochepa kapena kulibiretu.

Nthawi: Miyezi iwiri.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha ndipo nthawi zambiri imachitikira m’Nyumba ya Ufumu kapena m’Nyumba ya Msonkhano.

Oyenera Kulowa: Abale osakwatira a zaka za pakati pa 23 ndi 62 amene ali ndi thanzi labwino ndiponso amene akufunitsitsa kutumikira kumene kukufunika thandizo. (Maliko 10:29, 30) Akhale oti achita upainiya kwa zaka zosachepera ziwiri komanso atumikira mosalekeza pa udindo monga mtumiki wothandiza kapena mkulu kwa nthawi yosachepera zaka ziwiri.

Kulembetsa: Pamakhala msonkhano wa ofuna kupita kusukuluyi pa nthawi ya msonkhano wadera. Malangizo ena amaperekedwa pa msonkhano umenewu.

Rick amene analowa kalasi ya nambala 23 ku United States anati: “Pamene ndinali kuphunzira zambiri m’sukuluyi, mzimu wa Yehova unandithandiza kusintha zinthu zina mumtima mwanga.Yehova akakupatsa udindo amakuthandiza kuti ukwanitse. Ndinaona kuti ndikamaganizira kwambiri za chifuniro cha Yehova osati za ineyo, iye amandilimbitsa.”

Andreas amene akutumikira ku Germany anati: “Ndathandizidwa kudziwa kuti zimene zikuchitika m’gulu la Mulungu n’zodabwitsa kwambiri. Sukuluyi inandikonzekeretsa mautumiki ena akutsogolo. Zitsanzo zambiri za m’Baibulo zinandithandiza kudziwa mfundo yakuti kutumikira abale anga komanso Yehova kumabweretsa chimwemwe chenicheni.”

Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja

Cholinga: Kuphunzitsa Akhristu apabanja maphunziro apadera kuti athe kugwiritsidwa ntchito kwambiri ndi Yehova ndiponso gulu lake. Ambiri mwa anthu amene amaliza maphunzirowa amatumizidwa kumene kukufunikira thandizo m’dziko lawo. Ena amatumizidwa kudziko lina. Amatha kutumikira monga apainiya apadera akanthawi m’madera akumidzi kumene kuli ofalitsa ochepa kapena kulibiretu.

Nthawi: Miyezi iwiri.

Malo: Izichitika padziko lonse koma m’mayiko osankhidwa. Nthawi zambiri, izichitikira pa Nyumba ya Ufumu kapena Nyumba ya Msonkhano.

Oyenera Kulowa: Akhristu apabanja a zaka za pakati pa 25 ndi 50 amene ali ndi thanzi labwino, amene angathe kukatumikira kumene kukufunika thandizo ndiponso ali ndi mtima wonena kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Akhale oti akwanitsa zaka ziwiri ali m’banja ndiponso achita utumiki wa nthawi zonse mosalekeza kwa nthawi yosachepera zaka ziwiri. Mwamuna ayenera kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza kwa zaka zosachepera ziwiri mosalekeza.

Kulembetsa: Pamakhala msonkhano wa ofuna kulowa sukuluyi pa msonkhano wachigawo ndipo malangizo ena amaperekedwa pa nthawiyo. Ngati izi sizichitika pa msonkhano wachigawo m’dziko lanu koma mukufuna mutalowa, mungalembere ofesi ya nthambi kuti mumve zambiri.

Eric ndi Corina (amene ali kumanjawa) analowa kalasi yoyamba mu 2011. Iwo anati: “Moyo wa abale ndi alongo amene aphunzira sukuluyi kwa milungu 8 umasintha kwambiri. Panopa sitifuna zambiri pa moyo ndipo cholinga chathu ndi kugwiritsa ntchito nthawi yathu mwanzeru.”

Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo

Cholinga: Kuphunzitsa Akhristu kuti akhale amishonale m’madera amene kuli anthu ambirimbiri, akhale oyang’anira oyendayenda kapena atumikire pa Beteli. Cholinga chawo chimakhala kuthandiza kuti zinthu ziziyenda bwino mu utumiki komanso panthambi.

Nthawi: Miyezi isanu.

Malo: Ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, ku New York m’dziko la United States.

Oyenera Kulowa: Akhristu okwatirana amene ali kale mu utumiki wa nthawi zonse wapadera monga amishonale amene sanapiteko, apainiya apadera, oyang’anira oyendayenda kapena otumikira pa Beteli. Akhale oti achita utumikiwu limodzi kwa zaka zitatu mosalekeza. Akhale oti amatha kulankhula, kuwerenga ndiponso kulemba Chingelezi bwinobwino.

Kulembetsa: Komiti ya Nthambi ndi imene imauza anthu kuti afunsire ngati angakonde.

Lade ndi Monique a ku United States analowa sukuluyi ndipo akutumikira ku Africa. Lade anati: “Sukuluyi inatikonzekeretsa kupita kulikonse n’kumakagwira ntchito mwakhama limodzi ndi abale athu okondedwa.”

Monique anati: “Ndikamatsatira zimene ndaphunzira m’Mawu a Mulungu ndimasangalala kwambiri ndi utumiki wanga. Zimenezi zimanditsimikizira kuti Yehova amandikonda kwambiri.”

Sukulu ya Abale a m’Komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo

Cholinga: Kuphunzitsa abale a m’Komiti ya Nthambi kuti azitha kugwira bwino ntchito yawo yotsogolera mabanja a Beteli, kusamalira ntchito ya utumiki yokhudza mipingo komanso kuyang’anira madera ndiponso zigawo. Amaphunziranso zokhudza kumasulira, kusindikiza ndiponso kutumiza mabuku.

Nthawi: Miyezi iwiri.

Malo: Ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, ku New York m’dziko la United States.

Oyenera Kulowa: M’bale afunika kukhala m’Komiti ya Nthambi, m’Komiti ya Dziko kapena woti adzaikidwa pa udindowu.

Kulembetsa: Bungwe Lolamulira ndi limene limaitana abalewa ndi akazi awo.

Lowell ndi Cara analowa kalasi ya nambala 25 ndipo akutumikira ku Nigeria. Lowell anati: “Ndinakumbutsidwa kuti kaya ndili wotanganidwa bwanji, kaya ndapatsidwa ntchito yotani, chinthu chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Sukuluyi yandithandizanso kudziwa kuti pochita zinthu ndi anthu tizitengera mmene Yehova amakondera atumiki ake.”

Cara anati: “Mfundo imodzi imene sindidzaiwala ndi yakuti ngati sindingathe kufotokoza mfundo m’njira yosavuta ndiye kuti ndifunika kuiphunzira bwino ndisanakaphunzitse ena.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena