Kodi Mukuchita Zonse Zimene Mungathe Kuti Muphunzire Zambiri Kwa Yehova?
1. Kodi Yehova amaona bwanji nkhani ya maphunziro?
1 Yehova, ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ akufuna kuti ifeyo tiphunzire. (Yes. 30:20) Iye anayamba kuphunzitsa atalenga Mwana wake woyamba kubadwa. (Yoh. 8:28) Adamu atapanduka, Yehova sanasiye kuphunzitsa, koma mwachikondi anapereka malangizo kwa anthu opanda ungwiro.—Yes. 48:17, 18; 2 Tim. 3:14, 15.
2. Kodi ndi ntchito yaikulu iti yophunzitsa anthu imene ikuchitika?
2 Masiku ano, Yehova akutsogolera ntchito yaikulu kwambiri yophunzitsa anthu padziko lonse imene sinachitikepo ndi kale lonse. Mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera, mophiphiritsira anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse akukhamukira ku “phiri la nyumba ya Yehova.” (Yes. 2:2) N’chifukwa chiyani akukhamukira kumeneko? Iwo akufuna kuti akalangizidwe njira za Mulungu kapena kuti kuphunzitsidwa ndi Yehova. (Yes. 2:3) M’chaka chautumiki cha 2010, Mboni za Yehova zinatha maola 1.6 biliyoni zikulalikira ndi kuphunzitsa anthu choonadi cha m’Baibulo. Kuwonjezera pamenepo, mlungu uliwonse mipingo yoposa 105,000 imalandira malangizo auzimu padziko lonse lapansi. Ndipo mabuku Achikhristu othandiza pophunzira Baibulo amafalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru m’zinenero zoposa 500.
3. Kodi inuyo mwapindula bwanji ndi maphunziro ochokera kwa Yehova?
3 Pindulani Mokwanira: Tapindulatu kwambiri ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu. Taphunzira kuti Mulungu ali ndi dzina ndiponso amatisamalira. (Sal. 83:18; 1 Pet. 5:6, 7) Tapeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pa moyo monga akuti: N’chifukwa chiyani anthu amavutika ndi kufa? Kodi ndingatani kuti ndikhaledi wosangalala? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Yehova watipatsanso malangizo otithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino ndipo amatithandiza ‘kukhala ndi moyo wopambana.’—Yos. 1:8.
4. Kodi atumiki a Mulungu ali ndi mwayi wamaphunziro ati, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuphunzira zambiri kwa Yehova?
4 Kuwonjezera pamenepa, Yehova amaperekanso maphunziro ena apadera kuti athandize atumiki ake ochuluka n’cholinga choti achite zambiri pamene akumutumikira. Patsamba 4 mpaka 6 pali mautumiki osiyanasiyana amene ena angachite. Ngakhale kuti mmene zinthu zili pa moyo wathu sitingathe kuchita nawo maphunziro amene atchulidwa pamenepa, kodi tikuchita zonse zimene tingathe kuti tipindule ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu amenewa? Kodi tikulimbikitsa achinyamata, amene nthawi zambiri aziphunzitsi awo kusukulu ndiponso anthu ena amawalimbikitsa kukachita maphunziro a ku yunivesite, kuti akhale ndi zolinga zauzimu n’kupeza maphunziro apamwamba kwambiri ochokera kwa Mulungu? Kuchita zonse zimene tingathe kuti tiphunzire zambiri kwa Yehova kudzatithandiza kukhala ndi moyo wosangalala panopo ndiponso moyo wosatha m’tsogolo.—Sal. 119:105; Yoh. 17:3.
Ena mwa Maphunziro Amene Tingapeze m’Gulu la Yehova
Sukulu Yophunzitsa Kuwerenga ndi Kulemba
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa anthu kudziwa kuwerenga ndi kulemba kuti aziwerenga ndi kuphunzira Baibulo paokha ndiponso kuphunzitsa ena choonadi.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Malinga ndi mmene zinthu zilili kumaloko.
• Malo Ophunzirira: Pa Nyumba ya Ufumu ya m’deralo.
• Ndani Angalembetse?: Ofalitsa onse ndiponso anthu achidwi.
• Mungalembetse Bwanji?: Akulu pa mpingo amakonza sukulu yophunzitsa kuwerenga ndi kulemba ngati pakufunikira kutero ndipo amalimbikitsa onse amene akufuna kuti aphunzire.
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa ofalitsa kuti azilalikira ndiponso kuphunzitsa mogwira mtima uthenga wabwino.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Siitha.
• Malo Ophunzirira: Pa Nyumba ya Ufumu ya m’deralo.
• Ndani Angalembetse?: Ofalitsa onse ndiponso ena amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse, amene amavomereza zimene Baibulo limaphunzitsa komanso amene amachita zinthu mogwirizana ndi moyo wachikhristu.
• Mungalembetse Bwanji?: Funsani Woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Sukulu ya Chinenero Chakunja
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa ofalitsa mmene angalalikirire uthenga wabwino m’chinenero china.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Miyezi inayi kapena isanu. Nthawi zambiri makalasi amachitika Loweruka m’mawa kwa ola limodzi kapena awiri.
• Malo Ophunzirira: Nthawi zambiri kumakhala ku Nyumba ya Ufumu yapafupi ndi kumaloko.
• Ndani Angalembetse?: Ofalitsa amene ali ndi mbiri yabwino amene akufuna kumalalikira m’chinenero chakunja.
• Mungalembetse Bwanji?: Sukuluyi imakonzedwa ndi ofesi ya nthambi pakafunikira kutero.
Kumanga Nyumba ya Ufumu
• Cholinga Chake: Kumanga ndi kukonzanso Nyumba za Ufumu. Imeneyi si sukulu, koma kudzera mu ntchito imeneyi anthu ogwira ntchito yodzipereka amaphunzitsidwa maluso osiyanasiyana kuti azithandiza pa ntchito zomangamanga.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Zimadalira ndi munthu aliyense wogwira ntchito yodziperekayi.
• Malo Ophunzirira: Kulikonse m’dera limene Magulu Omanga Nyumba za Ufumu agawiridwa. Ogwira ntchito yodzipereka ena angapemphedwe kukathandiza pa ntchito yopereka thandizo kwa anthu amene akumana ndi masoka achilengedwe kumadera akutali.
• Ziyeneretso: Abale ndi alongo ayenera kukhala obatizidwa ndipo ayenera kuvomerezedwa ndi bungwe la akulu. Angakhale oti ali kale ndi luso linalake kapena ayi.
• Mungalembetse Bwanji?: Lembani Fomu Yofunsirapo Ntchito Yodzipereka Yomanga Nyumba za Ufumu (S-82) ndipo mungaipeze kwa akulu pa mpingo.
Sukulu ya Utumiki Waupainiya
• Cholinga Chake: Kuthandiza apainiya kuti ‘akwaniritse mbali zonse za utumiki wawo.’—2 Tim. 4:5.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Milungu iwiri.
• Malo Ophunzirira: Ofesi ya nthambi ndi imene imakonza malo ophunzirira ndipo nthawi zambiri kumakhala ku Nyumba ya Ufumu yapafupi ndi kumaloko.
• Ziyeneretso: Abale ndi alongo amene akhala akuchita upainiya wokhazikika kwa pafupifupi chaka chimodzi.
• Mungalembetse Bwanji?: Apainiya amene akuyenerera kale ndi amene amalowa m’sukuluyi ndipo amadziwitsidwa ndi mlembi wa mpingo.
Sukulu ya Otumikira pa Beteli Atsopano
• Cholinga Chake: Sukulu imeneyi cholinga chake ndi kuthandiza amene angofika kumene pa Beteli kuti azisangalala pamene akuchita utumiki wa pa Beteli.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Ola limodzi mlungu uliwonse kwa milungu 16.
• Malo Ophunzirira: Ku Beteli.
• Ziyeneretso: Ayenera kukhala m’bale kapena mlongo amene akutumikira m’banja la Beteli nthawi zonse kapena amene akugwira ntchito yodzipereka kwa nthawi yaitali (kwa chaka chimodzi kapena kuposa).
• Mungalembetse Bwanji?: Abale ndi alongo amene anavomerezedwa kutumikira pa Beteli amakhala akuyenerera kale kulowa m’sukuluyi.
Sukulu ya Utumiki wa Ufumu
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa akulu ndi atumiki othandiza kuti azichita udindo wawo woyang’anira ndi kuyendetsa zinthu mwadongosolo. (Mac. 20:28) Sukulu imeneyi imachitika mogwirizana ndi zimene Bungwe Lolamulira lakonza, pakapita zaka zowerengeka kuchokera pamene sukulu ina ngati yomweyi inachitika.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: M’zaka zaposachedwapa yakhala ikuchitika kwa tsiku limodzi ndi hafu kwa akulu ndipo tsiku limodzi kwa atumiki othandiza.
• Malo Ophunzirira: Nthawi zambiri imachitikira pa Nyumba ya Ufumu ya pafupi ndi deralo kapena ku Malo a Msonkhano.
• Ziyeneretso: Munthu ayenera kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza.
• Mungalembetse Bwanji?: Akulu ndi atumiki othandiza amene akuyenerera amaitanidwa ndi woyang’anira dera.
Sukulu ya Akulua
• Cholinga Chake: Kuthandiza akulu kuti azichita udindo wawo mwadongosolo.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Masiku asanu.
• Malo Ophunzirira: Ofesi ya nthambi ndi imene imakonza ndipo nthawi zambiri pamakhala pa Nyumba ya Ufumu yapafupi ndi deralo kapena pa Malo a Msonkhano.
• Ziyeneretso: Munthu ayenera kukhala mkulu.
• Mungalembetse Bwanji?: Akulu amene akuyenerera amaitanidwa ndi ofesi ya nthambi.
Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda ndi Akazi Awob
• Cholinga Chake: Kuthandiza oyang’anira madera ndi oyang’anira zigawo kuti azigwira ntchito zawo mogwira mtima akamatumikira mipingo, ‘azichita khama kulankhula ndi kuphunzitsa’ ndiponso kuweta amene akuwayang’anira.—1 Tim. 5:17; 1 Pet. 5:2, 3.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Miyezi iwiri.
• Malo Ophunzirira: Ofesi ya nthambi ndi imene imakonza.
• Ziyeneretso: Munthu ayenera kukhala woyang’anira dera kapena woyang’anira chigawo.
• Mungalembetse Bwanji?: Oyang’anira Oyendayenda ndi akazi awo amene akuyenerera amaitanidwa ndi ofesi ya nthambi.
Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatirac
• Cholinga Chake: Kukonzekeretsa abale osakwatira amene ndi akulu ndi atumiki othandiza kukwaniritsa maudindo owonjezera. Abale ambiri amene amaliza maphunzirowa amatumizidwa kumadera amene kukufunika thandizo m’dziko lawo. Abale owerengeka angatumizidwe kudziko lina ngati angadzipereke.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Miyezi iwiri.
• Malo Ophunzirira: Ofesi ya nthambi ndi imene imakonza ndipo nthawi zambiri pamakhala pa Malo a Msonkhano kapena Nyumba ya Ufumu.
• Ziyeneretso: Ayenera kukhala abale osakwatira a zaka zapakati pa 23 ndi 62, amene ali ndi thanzi labwino ndiponso amene akufunitsitsa kupititsa patsogolo zolinga za Ufumu komanso kutumikira abale awo kumene kukufunikira thandizo. (Maliko 10:29, 30) Akhale oti atumikira pa udindo monga mtumiki wothandiza kapena mkulu kwa nthawi yosachepera zaka ziwiri mosalekeza.
• Mungalembetse Bwanji?: Ngati sukuluyi ilipo m’gawo la nthambi yanu, pamakhala msonkhano wa ofuna kupita ku sukuluyi pa nthawi ya msonkhano wadera. Malangizo ena amaperekedwa pa msonkhano umenewu.
Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanjad
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa Akhristu amene ali pabanja maphunziro apadera kuti athe kugwiritsidwa ntchito kwambiri ndi Yehova ndiponso gulu lake. Ambiri mwa anthu amene amaliza maphunzirowa amatumizidwa kumene kukufunikira thandizo m’dziko lawo. Owerengeka angatumizidwe kukatumikira m’dziko lina ngati atadzipereka.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Miyezi iwiri.
• Malo Ophunzirira: Makalasi oyambirira akuchitikira ku Watchtower Educational Center ku Patterson, New York, ku America. Kenako sukuluyi idzayamba kuchitikiranso m’madera amene ofesi ya nthambi idzasankhe ndipo nthawi zambiri pazidzakhala pa Malo a Msonkhano kapena pa Nyumba ya Ufumu.
• Ziyeneretso: Okwatirana a zaka zapakati pa 25 ndi 50, amene ali ndi thanzi labwino, amene angathe kukatumikira kumene kukufunika thandizo ndiponso ali ndi mtima wa, “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Kuwonjezera pamenepa, akhale oti akwanitsa zaka ziwiri ali pabanja ndiponso akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa nthawi yosachepera zaka ziwiri mosalekeza.
• Mungalembetse Bwanji?: Ngati sukuluyi ilipo m’gawo la nthambi yanu, pamakhala msonkhano wa ofuna kupita kusukuluyi pa nthawi ya tsiku la msonkhano wapadera. Malangizo ena amaperekedwa pa msonkhano umenewu.
Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa apainiya ndi atumiki ena a nthawi zonse kuti akachite utumiki wa umishonale.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Miyezi isanu.
• Malo Ophunzirira: Ku Watchtower Educational Center, ku Patterson, New York, ku America.
• Ziyeneretso: Okwatirana amene akhala obatizidwa kwa zaka zitatu ndipo ali ndi zaka zapakati pa 21 ndi 38 pamene akufunsira koyamba kulowa m’sukuluyi. Ayenera kukhala odziwa kulankhula Chingelezi, atakwanitsa zaka ziwiri ali pabanja, akuchita utumiki wa nthawi zonse kwa nthawi yosachepera zaka ziwiri mosalekeza ndiponso ayenera kukhala ndi thanzi labwino. Abale amene akuchita upainiya m’dziko lina (kuphatikizapo amene amadziwika kuti akuchita umishonale), oyang’anira oyendayenda, abale amene akutumikira pa Beteli, amene analowapo m’Sukulu Yophunzitsa Utumiki, Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira ndiponso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja angafunsire ngati ali ndi ziyeneretsozi.
• Mungalembetse Bwanji?: Mu nthambi zosankhidwa, pamakhala msonkhano wa amene akufuna kulowa m’sukuluyi pa nthawi ya msonkhano wachigawo. Malangizo ena amaperekedwa pa msonkhano umenewu. Ngati pa msonkhano wachigawo palibe msonkhanowu koma mukufuna kulowa nawo m’sukuluyi mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya kwanuko kuti akupatseni malangizo a zimene mungachite.
Sukulu ya Abale a m’Komiti ya Nthambi ndi Akazi Awo
• Cholinga Chake: Kuphunzitsa abale amene akutumikira m’ma Komiti a Nthambi kuti azitha kugwira bwino ntchito yawo yotsogolera mabanja a Beteli, kusamalira ntchito ya utumiki yokhudza mipingo, kuyang’anira madera ndi zigawo mu gawo la nthambi yawo, kuyang’anira ntchito yomasulira, kusindikiza ndi kutumiza mabuku komanso kuyang’anira madipatimenti osiyanasiyana.—Luka 12:48b.
• Imatenga Nthawi Yaitali Bwanji?: Miyezi iwiri.
• Malo Ophunzirira: Ku Watchtower Educational Center, ku Patterson, New York, ku America.
• Ziyeneretso: Amene akutumikira mu Komiti ya Nthambi kapena Komiti ya Dziko kapena pa udindo wina ngati umenewu.
• Mungalembetse Bwanji?: Abale amene akuyenerera, limodzi ndi akazi awo amaitanidwa ndi Bungwe Lolamulira.
[Mawu a M’munsi]
a Panopo, sukulu imeneyi ikuchitika m’mayiko ochepa.
b Panopo, sukulu imeneyi ikuchitika m’mayiko ochepa.
c Panopo, sukulu imeneyi ikuchitika m’mayiko ochepa.
d Panopo, sukulu imeneyi ikuchitika m’mayiko ochepa.