Ndandanda ya Mlungu wa October 24
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 24
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 14 ndime 17-21 ndi bokosi patsamba 149 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Miyambo 17-21 (Mph. 10)
Na. 1: Miyambo 17:21–18:13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Nkhondo ndi Kusowa kwa Chakudya Kuli Mbali ya “Chizindikiro”?—rs tsa. 262 ndime 1 mpaka tsa. 263 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Anthu Amene Amatamanda Chilengedwe Koma Osati Mlengi Amasonyeza Kuti Ndi Otani?—Aroma 1:20 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Tchulani mabuku ogawira m’mwezi wa November, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri za mmene tingagawirire mabukuwa.
Mph. 25: “Kodi Mukuchita Zonse Zimene Mungathe Kuti Muphunzire Zambiri Kwa Yehova?” Mafunso ndi mayankho. Funsani mwachidule m’bale amene anaphunzitsidwa zinthu zina mwapadera ndi gulu la Yehova.
Nyimbo Na. 9 ndi Pemphero