Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/99 tsamba 8
  • Njira Zofutukulira Utumiki Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Zofutukulira Utumiki Wanu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Futukulani Chuma Chanu cha Utumiki wa Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Kodi Mukufuna Kuchita Zochuluka?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 5/99 tsamba 8

Njira Zofutukulira Utumiki Wanu

1 Zaka zoposa 40 zapitazo, mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 15, 1955 munatuluka nkhani yamutu wakuti “Kodi Mukuchita Zomwe Mungathe?” Inapereka malingaliro a mmene anthu a Yehova aliyense payekha angawongolerere zoyesayesa zake za mu utumiki kuti awonjezere ntchito yawo ya Ufumu. Uphungu wabwino umenewu ukugwiranso ntchito lerolino, pamene tikupitiriza kuwongolera utumiki wathu.

2 Chimene chiyenera kusonkhezera utumiki wathu wonse ndi lamulo lalikulu lakuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:30) Timasonyeza chikondi chathu chonse pa Yehova mwa kugwiritsa ntchito mokwanira mipata yomwe tili nayo kuti tipititse patsogolo ntchito yake ya Ufumu. Pendani njira zotsatirazi zimene mungafutukulire utumiki wanu.

3 Kwaniritsani Udindo Wanu: Abale odzipatulira angayesetse kuti akhale atumiki otumikira ndipo kenako apite patsogolo ndi kukhala akulu. Nkhani za m’kope la Nsanja ya Olonda ya September 1, 1990, yamutu wakuti “Kodi Mukukalimira?” ndi yakuti “Kodi Muli Oyeneretsedwa Kutumikira?,” zinasonkhezera abale ambiri kudzipereka pamaudindo a mpingo. Funsani akulu mumpingo wanu malingaliro ena a mmene mungakalimirire ndi kukhala woyenerera.

4 Akulu ndi atumiki otumikira amene ali osakwatira akupemphedwa kulingalira mosamalitsa zofunsira kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Mungadziŵe zambiri za sukulu imeneyi mwa kuŵerenga mabuku ena pamutu wakuti “Ministerial Training School” mu Watch Tower Publications Indexes a 1986-1995, 1996, ndi 1997. Kodi mukuona kuti “khomo lalikulu ndi lochititsa [“lantchito,” NW]” lakutsegukirani? (1 Akor. 16:9a) Abale ambiri amene analoŵa pakhomo limeneli sanali kulingalira za maudindo onse autumiki amene akatsatirapo. Lerolino akusangalala kutumikira pa Beteli kapena m’gawo monga apainiya apadera, amishonale, kapena oyang’anira madera.

5 Kalimirani Utumiki wa Nthaŵi Zonse: Achinyamata omwe akutsiriza maphunziro awo akusekondale, amayi a pakhomo, ndi ena amene anapuma pantchito ayenera kulingalira mosamalitsa zochita upainiya. Pendani mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa July 1998, ndiyeno lankhulani ndi apainiya amene mikhalidwe yawo inali yofanana ndi yanuyo. Mwina mungalimbikitsidwe kufutukula utumiki wanu mwa kuchita upainiya, monga mmene iwo akuchitira. (1 Akor. 11:1) Kodi kungatheke kufutukula ntchito yanu mpaka maola 70 pamwezi motero mukumatumikira monga mpainiya wokhazikika?

6 Pakalipano abale ndi alongo oposa 17,000 kuzungulira padziko lonse akutumikira m’maofesi anthambi ndi panyumba za Beteli. Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1995 unafotokoza zomwe zimafunika kuti ufunsire utumiki umenewu. Bwanji osawerenga mphatikayo ndi kuona ngati mungayenere mwayi wapadera wa utumiki wa pa Beteli?

7 Katumikireni Kumene Kuli Kusoŵa Kokulira: Kodi mumakhala m’gawo limene limagwiridwa ntchito pafupipafupi kapena kumene kuli abale ambiri ogwira nawo ntchito? Kodi munayamba mwalingalirapo za kufutukula utumiki wanu mwa kusamukira kumene kuli kusoŵa kokulira? Mwina kusamukako kungakhale kupita ku midzi yapafupi kumene antchito akufunika. (Mat. 9:37, 38) Musachite zimenezi popanda kulingalira kaye. N’zofunika kulingalira mwapemphero. (Luka 14:28-30) Kambitsiranani mkhalidwe wanu ndi akulu ndi woyang’anira dera. Adzakamba nanu ngati kuli kwanzeru kuti musamuke pakali pano kapena kuti muyambe kukonzekera zodzatero m’tsogolo. Ngati mukufuna kulembera ku Sosaite kufunsa malingaliro a kumene mungapite, kalata yanuyo iyenera kutumizidwa pamodzi ndi kalata yosainidwa ndi Komiti Yautumiki Yampingo.

8 Wongolerani Utumiki Wanu: Ndithudi tonse tingatengemo mbali mokwanira mu utumiki mwa kuwongolera utumiki wathu wakumunda. Kodi mumachita nawo mbali zonse za ntchitoyi, monga umboni wakunyumba ndi nyumba komanso wamwamwayi ndiponso maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo? Ngati mumachititsa phunziro, kodi mungawongolere luso lanu lakuphunzitsa? N’kwanzeru kupenda mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 1996 kuti mupeze malingaliro amene mungagwiritse ntchito kuti musonkhezere wophunzira wanu kudzipatulira ndi kubatizidwa.

9 Njira zambiri za mmene tingafutukulire ndi kuwongolera utumiki wathu zikupezeka m’chaputala 9 m’buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu. Ndithudi tonsefe tiyenera kufuna kuchita zambiri zimene tingathe mu utumiki wa Mulungu. Bwanji osalingalira mosamalitsa zolinga zanu zauzimu? Chitani mmene 1 Timoteo 4:15 amanenera kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena