Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Kodi Ndidzachite Zotani Pamoyo Wanga? (Gawo 1)
Achinyamata akamakula amayenera kusankha zinthu zofunika kwambiri pa moyo wawo. Kuti muwathandize, gwiritsani ntchito mafunso otsatirawa pamene mukukambirana mutu 38 m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. (1) Kodi lemba la Miyambo 4:26 lingathandize bwanji achinyamata kusankha zinthu zokhudza tsogolo lawo mwanzeru? (tsamba 311) (2) Kodi n’chiyani chimene chingathandize wachinyamata kukhala ndi moyo wosangalala? (tsamba 312 ndi 313) (3) Kodi ndi utumiki wosiyanasiyana uti umene achinyamata angachite? (tsamba 313 ndi 315) (4) Kodi ndi utumiki uti umene umakusangalatsani komanso umene mungakwanitse? (Onani zithunzi zimene zili patsamba 316 ndi 317) (5) Kodi achinyamata angadziikire zolinga zotani (a) pa nkhani ya utumiki (b) pa nkhani yophunzira Baibulo paokha ndiponso (c) mumpingo? (tsamba 314) (6) Kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse? (Werengani Malaki 3:10.) (7) Kodi achinyamata angakonzekere bwanji tsogolo lawo? (tsamba 315 ndi 316) (8) Kodi Roberto ananena chiyani chimene chingathandize achinyamata kusankha zinthu mwanzeru? (tsamba 316 ndi 317)—Werengani Miyambo 20:18.
Achinyamata ndi ofunika kwambiri m’gulu la Yehova. Choncho, mlungu wamawa tidzakambirana zimene zingawathandize kuti apite patsogolo mwauzimu. Mukakonzekere kudzayankha mafunso amene tidzakambirane pa Msonkhano wa Utumiki mlungu wamawa.