Ndandanda ya Mlungu wa September 24
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 24
Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 12 ndime 14-20 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Danieli 1-3 (Mph. 10)
Na. 1: Danieli 2:17-30 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Angelo Amachita Zinthu Mwadongosolo?—rs tsa. 139 ndime 2 mpaka tsa. 140 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Tingapewe Bwanji Kumvetsa Chisoni Mzimu wa Yehova?—Aef. 4:30 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 30: “Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Kodi Ndidzachite Zotani Pamoyo Wanga? (Gawo 2)” Mafunso ndi mayankho. M’mawu oyamba, osapitirira mphindi imodzi, nenani mwachidule zimene tinakambirana mlungu watha pa Gawo 1 la nkhaniyi. Pomaliza nkhaniyi, yamikirani achinyamata chifukwa choyesetsa ‘kukumbukira’ Yehova pa unyamata wawo. (Mlal. 12:1) Alimbikitseni kuti apitirize kugwiritsira ntchito moyo wawo potumikira Yehova.
Nyimbo Na. 91 ndi Pemphero