Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Kuyambira m’mwezi wa May mpaka mwezi wa July chaka chino, akulu onse m’Malawi muno anali pa “Sukulu ya Akulu” ya masiku anayi ndi hafu. Mosakayikira, malangizo amene akulu analandira kusukuluyi awathandiza kuweta mwachikondi nkhosa zimene Mulungu anawaikiza. (Mac. 20:28) Tikuthokoza Yehova ndiponso gulu lake pothandiza kuti sukuluyi iyende bwino m’gawo la nthambi yathu. Tikuthokozanso abale nonse chifukwa cha zopereka zanu zimene zinathandiza kuti sukuluyi iyende bwino m’dera lanu.