Ndandanda ya Mlungu wa October 8
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 8
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 13 ndime 8-16, ndi bokosi patsamba 105 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Danieli 7-9 (Mph. 10)
Na. 1: Danieli 7:13-22 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Baibulo Limasonyeza Kuti AKhristu Oona Ndi Gulu Lochita Zinthu Mwadongosolo?—rs tsa. 141 ndime 2 mpaka tsa. 142 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yehova ndi Wokhulupirika M’njira Ziti?—Chiv. 15:4; 16:5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Ngati Wina Wanena Kuti ‘Ndine Wotanganidwa.’ Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 19, ndime 5 mpaka tsamba 20 ndime 4. Kambiranani zina mwa mfundo zimene zili m’bukuli komanso mfundo zina zimene zakhala zothandiza m’gawo la mpingo wanu. Chitani zitsanzo ziwiri zachidule.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 21:12-16 ndi Luka 21:1-4. Kambiranani zimene tikuphunzira pa nkhani zimenezi.
Mph. 10: “Yesetsani Kumalalikira Madzulo.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime yachiwiri, pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pamene ankalalikira nthawi yamadzulo.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero