Yesetsani Kumalalikira Madzulo
1. Mogwirizana ndi zimene katswiri wina wamaphunziro ananena, kodi mtumwi Paulo ankalalikira kunyumba ndi nyumba nthawi yanji?
1 Buku lina lachingelezi (Daily Life in Bible Times) limanena kuti mtumwi Paulo ankalalikira kunyumba ndi nyumba “kuyambira 4 koloko madzulo mpaka usiku.” Sitikudziwa ngati nthawi zonse Paulo ankalalikira nthawi imeneyi, koma zomwe tikudziwa n’zakuti Paulo anali wokonzeka “kuchita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino.” (1 Akor. 9:19-23) Kuti Paulo akwanitse kuchita zimenezi, ayenera kuti anasintha ndandanda yake kuti azilowa mu utumiki pa nthawi imene akanapeza anthu ambiri oti n’kuwalalikira.
2. N’chifukwa chiyani madzulo ndi nthawi yabwino yolalikira?
2 M’madera ambiri, ofalitsa anazolowera kulalikira kunyumba ndi nyumba m’mawa mkati mwa mlungu. Kodi mumaona kuti nthawi imeneyi ndi yogwirizana ndi anthu a m’dera lanu? Mpainiya wina ananena za gawo lake kuti: “Nthawi zambiri sindipeza anthu pakhomo m’mawa. Koma anthu ambiri amakonda kupezeka pakhomo chakumadzulo.” Chotero kulalikira madzulo kungatithandize kuuza anthu, makamaka azibambo, uthenga wabwino. Pa nthawiyi, eninyumba amakhala akupumula ndipo akhoza kutilola kucheza nawo. Ngati n’zotheka kumalalikira madzulo, akulu ayenera kukonza misonkhano yokonzekera utumiki wa madzulo.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuzindikira pamene tikulalikira madzulo?
3 Muzichita Zinthu Mozindikira: Mukamalalikira chakumadzulo, kuchita zinthu mozindikira n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, ngati mutapeza kuti mwininyumba watanganidwa ndi zinthu zina, zingakhale bwino kumuuza kuti mubwera nthawi ina. Mungachitenso bwino kumalalikira muli anthu awiriawiri kapena m’timagulu ndipo musamasiyane. Muzipewa kupita kunyumba za anthu madzulo kwambiri kuti mupewe kuwasokoneza pamene akukonza chakudya cha madzulo. (2 Akor. 6:3) Ngati dera lanu lili loopsa, muzilalikira chakumasana.—Miy. 22:3.
4. Kodi timapeza madalitso otani tikamalalikira madzulo?
4 Madalitso: Utumiki umasangalatsa kwambiri tikamalalikira pa nthawi imene anthu ambiri angapezeke panyumba. Komanso tikamalalikira anthu ambiri, timakhalanso ndi mwayi wothandiza anthu ochuluka kuti “apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Kodi mungasinthe ndandanda yanu kuti muzitha kulalikira madzulo?