Ndandanda ya Mlungu wa October 15
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 15
Nyimbo Na. 29 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 13 ndime 17-24 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Danieli 10-12 (Mph. 10)
Na. 1: Danieli 11:15-27 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Akhristu Sabwezera Ena Akawachitira Zoipa?—Aroma 12:18-21 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Atumiki Okhulupirika a Mulungu Akupezeka M’Matchalitchi Osiyanasiyana Achikhristu?—rs tsa. 142 ndime 3-5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Ngati Wina Wanena Kuti ‘Sindikufuna Kukambirana za M’Baibulo.’ Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 16, ndime 1 mpaka tsamba 18 ndime 1. Kambiranani zina mwa mfundo zimene zili m’bukuli komanso mfundo zina zimene zakhala zothandiza m’gawo la mpingo wanu. Chitani zitsanzo ziwiri zachidule.
Mph. 20: “Muzigwiritsa Ntchito Timapepala Pofalitsa Uthenga Wabwino.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime yachisanu, fotokozani mwachidule zimene zili m’timapepala timene tidzagawire mwezi wa November ndipo muchite chitsanzo. Mukamakambirana ndime 7, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito timapepala polalikira mwamwayi.
Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero