Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bulosha la Mulungu Amafunanji Kuyambitsira Maphunziro?
1 Kodi mukudziŵa kuti kukambirana mokhazikika ndiponso mwadongosolo, ngakhale mwachidule, ndi munthu wachidwi nkhani za m’Baibulo zimene zili m’buku lina lililonse loyenera lothandiza kuphunzira Baibulo, ndiye kuti mukuchititsa phunziro la Baibulo? Inde, limenelo ndi phunziro la Baibulo kaya mukuchitira pa nkhonde kapena pa telefoni. Bwanji osayesetsa m’miyezi ya May ndi June kuyambitsa phunziro lotereli pogwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji?
2 Konzekerani Kuti Zikuyendereni Bwino: Pogaŵira bulosha la Mulungu Amafunanji, dziŵiranitu zimene mukufuna kukambirana ndi munthu. Ukakhala ulendo wobwereza lingalirani zimene munakambirana paulendo woyamba. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi ndime ziti mu buloshali zimene ndingagogomezere popitiriza nkhani imene tinakambirana paulendo woyamba uja ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo?’ Ngati mukulalikira kunyumba ndi nyumba pezani nkhani zosangalatsa wachinyamata, wachikulire, bambo, kapena mayi. Onani mitu yankhani m’buloshali, ndipo sankhani nkhani yosangalatsa. Mukasankha ulaliki umene mukagwiritse ntchito, uyeserereni kangapo. Kuyeserera ulaliki kumathandizanso kuti zinthu zitiyendere bwino.
3 M’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 muli “Mfundo Zimene Mungagwiritse Ntchito Pogaŵira Bulosha la Mulungu Amafunanji,” zokwana zisanu ndi zitatu. Bokosi lakuti “Njira Yolunjika” limasonyeza momwe tingagwiritsire ntchito buloshali kuyambitsira maphunziro. Mungagwiritse ntchito mfundo yoyambayo motere:
◼ “Kodi mukudziŵa kuti pamphindi zochepa chabe mutha kupeza yankho la funso lofunika kwambiri la m’Baibulo? Mwachitsanzo, kodi n’chifukwa ninji pali zipembedzo zambiri zimene zimati n’zachikristu? Kodi munafunsapo funso limeneli?” Akayankha, pitani pa phunziro 13 ndipo kambiranani ndime ziŵiri zoyambirira. Ngati nthaŵi ilipo, ŵerengani lemba limodzi kapena aŵiri ndipo kambiranani. Ndiyeno ŵerengani funso lomaliza pamwamba pa phunzirolo, n’kunena kuti: “Mbali yotsala ya phunziroli ikufotokoza zizindikiro zisanu za chipembedzo choona. Ndingathe kudzabweranso kuti tidzaonere limodzi mfundo zimenezi.”
4 Limbikirani: Gwiritsani ntchito mpata uliwonse kusonyeza anthu momwe timachitira phunziro pogwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji. Pemphani Yehova akudalitseni. (Mat. 21:22) Mukalimbikira ntchito yanu, mudzaona momwe zimasangalatsira kuthandiza munthu wina kulabadira uthenga wabwino.