Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira May 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 15: “Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 1.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Fotokozani chifukwa chake kuli kwanzeru kulingalira zinthu bwino pamene tikufuna kukwatira kapena kukwatiŵa ndiponso kubereka ana.
Mph. 20: “Kodi Kuchotsa Anthu mu Mpingo Kumasonyeza Chikondi?” Ikambidwe ndi mkulu waluso. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito malemba oyenera kuti muthandize onse kuzindikira chifukwa chake n’kofunika kusamala pochita zinthu ndi achibale ochotsedwa mu mpingo. Gogomezerani kuti kuchotsa anthu mumpingo ndi njiradi ya chikondi cha Mulungu. Sonyezani kufunika kotsatira malangizo ameneŵa.
Nyimbo Na. 115 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 20
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri za ulaliki zosonyeza momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya May 15 ndi Galamukani! ya June 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu akanena mawu otsekereza kukambirana naye, akuti “Ndili wotanganitsidwa.”—Onani buku la Kukambitsirana, pamasamba 19-20.
Mph. 10: Zosoŵa za Pampingo.
Mph. 20: “Kuyamikira ‘Nyumba ya Mulungu.’” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndipo pendani mbali za mu Bulosha Loonetsa Malo a Nthambi ya Malaŵi. Kumbutsani anthu onse pampingopo kuti pokacheza ku Beteli azivala bwino ndiponso moyenera. Khomani bulosha limodzi la nthambiyi pa bolodi lanu la chidziŵitso kwa mwezi umodzi.
Nyimbo Na. 169 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 27
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a May. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, wofalitsa wachikulire asonyeze momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya June 1 ndipo wachinyamata asonyeze momwe tingagaŵire Galamukani! ya June 8. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse nenani momwe tingagwiritsire ntchito lemba mu ulalikiwo mosavuta.
Mph. 15: “Kodi Mpingo Wanu Uli ndi Gawo Lalikulu?” Nkhani komanso kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. (Mipingo imene ili ndi gawo lochepa ingapende nkhani ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 1999 yakuti, “Gwiritsani Ntchito Nthaŵi Yanu Moyenera.”) Tchulani kukula kwa gawo la mpingowo ndiponso limene linafoledwa chaka chathachi. Fotokozani momwe malingaliro a m’nkhaniyi angagwirire ntchito pa mpingopo. Pendani zimene akukonza zokalalikira posachedwapa ku gawo limene salalikirako pafupipafupi.
Mph. 18: “Kodi Mukugwiritsa Ntchito Bulosha la Mulungu Amafunanji Kuyambitsira Maphunziro?” (Onse akhale ndi mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 pokambirana nkhani imeneyi.) Yambani mwa kupempha wofalitsa amene wakonzekera bwino achite chitsanzo cha momwe tingayambitsire phunziro pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mu ndime 3. Ndiyeno, tchulani mfundo zikuluzikulu za m’buloshali, ndipo fotokozani chifukwa chake lili labwino kwambiri kuyambitsira maphunziro. Sonyezani kufunika kopenda maulaliki a mu mphatika ya January 2002. Funsani omvetsera kutchula maulaliki amene aona kuti ndi abwino kwambiri. Malizani mwa kubwereza chitsanzo cha ulaliki chimene mwachita kale chija.
Nyimbo Na. 93 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 3
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Bokosi la Mafunso. Konzani zoti ofalitsa amene anachita upainiya wothandiza kapena wokhazikika mu March, April, kapena May asimbe madalitso amene anapeza.
Mph. 15: Momwe Buku la Kukambitsirana Limagwiritsira Ntchito Mabaibulo Ena. Nkhani yachidule ndiponso kukambirana ndi omvetsera. Ŵerengani ndime yachiŵiri patsamba 8 m’buku la Kukambitsirana, ndipo fotokozani momwe tingachitire kuti tizigwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wathu ndiponso chifukwa chake tifunika kuchita zimenezi. Tchulani chidule cha matembenuzidwe a Mabaibulo a patsamba 6, ndipo fotokozani chifukwa chake timagwira mawu m’Mabaibulo ena. Kambiranani malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1997, patsamba 16, ndime 2, ndiponso patsamba 20, ndime 15. Mogwiritsa ntchito mitu ya m’buku la Kukambitsirana yakuti “Kuloŵa Mmalo Kwautumwi,” “Zifanizo,” ndi “Utatu,” pemphani omvetsera kunena momwe Mabaibulo ena angakhalire othandiza pophunzitsa choonadi.
Mph. 15: “Chikhulupiriro Chathu Chimatilimbikitsa Kuchita Ntchito Zabwino.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime yachiŵiri, funsani mwachidule Mboni yachangu. Pemphani wofalitsayo kunena momwe kulalikira kumasonyezera chikhulupiriro chake ndiponso momwe kumalimbitsira chikhulupiriro chake.
Nyimbo Na. 56 ndi pemphero lomaliza.