Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 1
1 Yehova Mulungu analamula Adamu ndi Hava kubereka ana. (Gen. 1:28) Ndipo izi m’kupita kwa nthaŵi zikanapangitsa kuti padziko lonse pakhale anthu. Kodi Akristu akufunika kutsatira lamulo limeneli m’masiku otsiriza ano? Lamulo la pa Genesis 1:28 analipereka dziko lili ndi anthu aŵiri okha. Choncho, sikoyenera kuganiza kuti Akristu akufunika kutsatira lamulo limeneli m’masiku otsiriza ano. Tiyeni tione zifukwa zake.
2 Solomo analemba kuti: “Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphoto yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chimphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake.” (Sal. 127:3-5) Mu Israyeli kubereka ana amakuona monga chizindikiro cha madalitso a Yehova. (Sal. 128:3, 4) Koma, tidziŵe kuti Solomo analemba zimene iye anachita pa Salmo 127, m’nthaŵi imene Israyeli anali ndi moyo wabwino kwambiri. (1 Maf. 4:20, 25) Komabe nthaŵi zina m’mbiri ya Israyeli, kubereka ana kunali kosasangalatsa.—Maliro 2:11, 20; 4:10.
3 Kodi Akristu oyambirira anali kuiona motani nkhani ya kubereka ana? Zikanakhala kuti Akristu anali kudzachulukana mwa kubereka ana, si bwenzi Yesu atalimbikitsa ophunzira ake “kulandira” kusakwatira “chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba.” (Mat. 19:10-12) Si bwenzi mtumwi Paulo atalemba kuti: “Iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosam’kwatitsa achita koposa.” (1 Akor. 7:38) Ngakhale kuti Israyeli wakuthupi anachulukana mwa kubereka ana, Israyeli wauzimu anali kudzakula mwa kupanga ophunzira.—Mat. 28:19, 20; Mac. 1:8.
4 Ngakhale kuti kukwatira kapena kukwatiwa ndi chosankha cha munthu, Paulo ananena kuti: “Ungakhale ukwatira, sunachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m’thupi, ndipo ndikulekani.” (1 Akor. 7:28) Mawu akuti “chisautso m’thupi” pa lembali, Baibulo la New World Translation limatilozera pa Genesis 3:16, pamene timaŵerenga kuti: “Kwa mkaziyo ndipo [Yehova] anati, ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” Kuphatikiza pa mavuto amene angakhalepo m’banja, “chisautso m’thupi” chimene anthu okwatira kapena okwatiwa adzapeze chimaphatikizaponso mavuto a pobereka. Ngakhale kuti Paulo sanaletse kukwatira ndiponso kubereka ana, anaona kuti ndi udindo wake kuchenjeza Akristu anzake kuti zimenezi zimabweretsa mavuto ndi zododometsa zimene zingawalepheretse kutumikira Yehova.
5 Kodi Akristu lerolino ayenera kuona motani kubereka ana? Zimenezi tidzakamba mu nkhani yakuti, “Kubereka Ana Mwanzeru—Udindo Wachikristu—Gawo 2.”