Ikani Zinthu Zofunika Kwambiri Patsogolo
1 Kodi zinthu zina zofunika ndi ziti pa thanzi lathu lauzimu? Ndithudi zimenezi zikuphatikizapo phunziro laumwini, kupezeka pamisonkhano, kupemphera kosalekeza, mayanjano abwino, ndi utumiki wachikristu. Sitingakhale ndi thanzi labwino lauzimu ngati sitiika zinthu zofunika pamalo oyamba m’moyo wathu.
2 Komabe, tonsefe timalimbana ndi zikhumbo zathupi ndipo timafunikiradi kudziletsa. (Agal. 5:17) Tisadzaganize konse kuti tingapindule zambiri mwa kufunafuna zinthu zokonda tokha. (Yer. 17:9) Choncho, ngati tikufuna kutetezera mtima wathu kuti usatisocheretse, tiyenera kumadzipenda nthaŵi zonse.—Miy. 4:23; 2 Akor. 13:5.
3 Pendani Mtima Wanu: Mungadzipende mwa kudzifunsa mafunso oona mtimawa: Kodi ndimalakalaka kuŵerenga Mawu a Mulungu? (1 Pet. 2:2) Kodi ndimazindikira kufunika kwa kupezeka pamisonkhano yonse yampingo? (Aheb. 10:24, 25) Kodi ndimapemphera mosalekeza? (Aroma 12:12) Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu okonda zauzimu? (Aroma 1:11, 12) Kodi ndimauona monga udindo wanga, kulengeza uthenga wabwino? (1 Akor. 9:16) Ngati mayankho ali inde, zikusonyeza kuti mumafuna kuika zinthu zofunika kwambiri patsogolo.
4 Pendani Zochita Zanu Zatsiku ndi Tsiku: Mungawonjezere kupenda zokhumba mtima wanuzo mwa kuika zinthu zofunika pamalo oyamba ndi nthaŵi yochitira zimenezo. Zimenezo zikuphatikizapo kukonza ndandanda yoŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndi kope lililonse la Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ngakhalenso kukonzekera misonkhano. Muyenera kumapatulanso nthaŵi yophunzira ndi banja ndi kupemphera limodzi. Dziikireni malire a nthaŵi imene mumaonerera TV, ndi imene mumagwiritsira ntchito kompyuta. Tsimikizani kupezeka pamisonkhano yonse yampingo, ndipo pochita zinthu zanu zonse, ikani misonkhano pamalo oyamba. Linganizani kuti banja lonse lizitengamo mbali mu utumiki wakumunda mlungu uliwonse.
5 Mosakayikira, kuika zinthu zofunika kwambiri patsogolo m’moyo wathu kudzatipatsa chimwemwe.