Maphunziro a Baibulo Amene Amapanga Ophunzira
1 “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” anafunsa choncho mdindo wa ku Aitiopiya, Filipo ‘atalalikira kwa iye Yesu.’ (Mac. 8:27-39) Mdindoyo anali atayamba kale kukonda malembo ouziridwa a Mulungu, ndipo atalandira chithandizo chauzimu kwa Filipo, anakonzeka kukhala wophunzira. Koma si anthu onse amene amaganiza kuti afunikiradi kusanthula okha Malemba.
2 Tikuyamikira gulu la Yehova kuti latipatsa zofalitsa zambiri kuti zilimbikitse anthu kusanthula uthenga wa m’Baibulo wonena za tsiku lathu. Chidziŵitso chimene chili m’zofalitsa zimenezi chidzakondweretsa anthu oona mtima amene angakhale ophunzira koma amene sadziŵa zambiri za Baibulo. Zofalitsa zabwino zimenezi zakonzedwa kuti zisonkhezere anthu kufuna kuŵerenga Baibulo.
3 Pofuna kuyamba phunziro la Baibulo, kungakhale kothandiza kupendanso malingaliro abwino ofalitsidwa mu mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, onena za mmene phunziro lobala zipatso lingachitidwire ndi buku la Chidziŵitso. Mukali m’kati mwaphunziro, muzimpenda wophunzirayo kuti muone mmene akuchitira, kuti mudziŵe mbali zimene mufunikira kumphunzitsa bwino. Limbikitsani wophunzirayo kumakonzekera maphunziro ake pasadakhale, kuyang’aniratu malemba. Akamayankha m’mawu akeake kudzatanthauza kuti akuchimvetsetsa bwino choonadi. Kaŵirikaŵiri omwe amaphunzira msanga ndiwo aja amene amaŵerenga zofalitsa zina za Sosaite ndi kupezeka pamisonkhano yampingo nthaŵi zonse. Mlimbikitseni kumauza ena mwa mwaŵi zimene akuphunzira. Msonyezeni mwachikondi zimene afunikira kuchita kuti apite patsogolo mwauzimu. Tisamangochititsabe maphunziro ndi anthu a mitima iŵiri. Ophunzira ayenera kukhala ofunitsitsa kuphunzira, kuchilandira choonadi, ndi kupitirizabe mpaka adzipatulire ndi kubatizidwa.
4 M’mabanja ena mumatsogozedwa maphunziro angapo, popeza kuti a pabanja ena amaphunzitsidwa payekhapayekha. Komabe, kuphunzirira pamodzi monga banja kumakhala bwino kwambiri, pakuti kumathandiza banjalo kugwirizana mwauzimu.
5 Lamulo la Yesu nlakuti tipite tikaphunzitse anthu. (Mat. 28:19) Kuti titero, tiyenera kuchititsa maphunziro a Baibulo amene amathandiza ophunzira kuphunzira bwino mpaka kufika ponena kuti, “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?”