Misonkhano Yautumiki ya September
Mlungu Woyambira September 1
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: “Ikani Zinthu Zofunika Kwambiri Patsogolo.” Mafunso ndi mayankho. Ngati mpata ulipo, kambanipo mfundo zochokera mu Galamukani! yachingelezi ya February 22 1987, masamba 8-9, pa kamutu kakuti “Setting Proper Priorities.”
Mph. 20: “Kuuzako Ena Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.” Nkhani yochokera pa ndime 1 ndiponso 6-8. Chitirani chitsanzo ndime 2-5. Gogomezerani kuti tiyenera kumakumbukira kuti cholinga chathu nchopanga ophunzira ndi kuyambitsa maphunziro.
Nyimbo Na. 107 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 8
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 20: “Maphunziro a Baibulo Amene Amapanga Ophunzira.” Nkhani ndi kukambitsirana ndi kagulu. Mkulu akuipenda nkhaniyo. Kenako akukambitsirana ndi ofalitsa aluso amene amachititsa maphunziro, nkhani yakuti “Sonkhezerani Ophunzira Kulinga ku Kudzipatulira ndi Ubatizo” (km-CN 6/96 mphatika, ndime 20-2).
Nyimbo Na. 109 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 15
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: “Kupangitsa Misonkhano Yathu Kukhala Yosangalatsa.” Nkhani yolimbikitsa yamkulu. Chitirani chitsanzo mfundo za m’ndime 4, mukumagwiritsira ntchito nkhani ya Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Buku la Mpingo la mlungu watha.
Mph. 20: Kodi Mukugwiritsira Ntchito Brosha la School? Mkulu akukambitsirana ndi makolo ndi ana ena nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1985, masamba 30-1, yachingelezi. Iwo akusimba zokumana nazo zawo namagwiritsira ntchito brosha la School.
Nyimbo Na. 112 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 22
Mph. 8: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 17: Mmene Mungayambire Kukambitsirana. Kupambana kwathu mu utumiki kumadalira pakukhoza kwathu kuwalankhulitsa anthu ena. Pamene takhoza kunena kanthu kena kamene kapangitsa ena kumvetsera, ndiye kuti talaka chimodzi cha zopinga zazikulu zimene timakumana nazo pochitira umboni. Kambitsiranani ndi omvetsera mfundo zazikulu mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 16, ndime 11-14. Sankhani ofalitsa aluso ndi okhoza bwino kuyamba makambitsirano kuti asimbe mawu oyamba amene amagwiritsira ntchito polankhula ndi anthu onga (1) munthu woyenda pamsewu, (2) woyenda naye m’basi, (3) kalaliki wa pakauntala, (4) munthu wotuluka m’sitolo nkukumana naye poimika magalimoto, (5) munthu ali khale pabenchi mupaki, ndi (6) wina wolankhula naye pafoni pochitira umboni.
Mph. 20: Pendani Lipoti la Mpingo la Chaka Chautumiki cha 1997. Woyang’anira utumiki akuyamikira mpingo pakhama lawo, makamaka mu March, April, ndi May. Akupereka malingaliro owongolera. Nafotokoza zolinga zina zoyenera kufikira za chaka chatsopano cha utumiki, kuphatikizapo kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi kuwachititsa, ndiponso upainiya wothandiza m’miyezi yokhala ndi mawikendi asanu—November, May, ndi August.
Nyimbo Na. 113 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 29
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda. Tchulani kuti mlungu wamaŵa tiyamba kuphunzira buku la Chimwemwe cha Banja pa phunziro la buku. Pokonzekera ntchito yamagazini mu October, kambitsiranani kufunika kwa “Kupenda Gawo Lanu,” “Kudziŵa Bwino Magaziniwo,” “Kukonza Mawu Anu Oyamba,” “Kusintha Malinga ndi Mwini Nyumba,” ndi “Kuthandizana,” kuchokera mu Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996, tsamba 8.
Mph. 15: Kodi Mkristu Angachitenji Pamene Aitanidwa Kukatumikira pa Bungwe Logamula Mlandu? Nkhani yamkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1997, masamba 27-9.
Mph. 15: Lemekezani Utumiki Wanu. Kukambitsirana ndi omvetsera mu buku la Uminisitala Wathu, masamba 81-3. Funsani mafunso aŵa kuti mumveketse mfundo zazikulu: (1) Kodi timapindula motani mwa kutsatira chitsanzo cha Yesu? (2) Kodi udindo wathu wolalikira ngwofunika motani? (3) Kodi nchiyani chinatisonkhezera kupatulira moyo wathu kwa Yehova? (4) Kodi munthu ayenera kukhala ndi khalidwe lotani kuti atumikire Mulungu? (5) Kodi tingaphunzirenji pa kalalikidwe ka Yesu?
Nyimbo Na. 121 ndi pemphero lomaliza.