Nyimbo 113
Ndife Mboni za Yehova!
1. Anthu amapangadi
Milungu ya mitengo.
Iye ndi Mulungu
Wamphamvuyonse.
Milungu sikhozatu
Kuwona zamtsogolo.
Afunatu mboni mwachabe,
Milunguyo sithandiza.
(Korasi)
2. ‘Ndinu mboni Zangadi,
Musawope milungu.
Ndinetu Yehova,
Mfumu ndi Mbuye.
Ine ndipulumutsa.
Palibe M’lungu wina.
Lengezanibe dzina langa;
Muli inu mboni zanga.’
(Korasi)
3. Kulengeza dzinalo,
Lichotsedwe chitonzo.
Chenjeza onyoza
Dzina la M’lungu.
Kuti a khulukira,
Anthu onse olapa.
Kulalikira kubweretsa
Chiyembekezo chamoyo.
(KORASI)
Mbonife za Yehova;
Tilankhula molimba.
Wathu ndi M’lungu waulosi;
Amanena zowona.