Nyimbo 37
Kupanga Dzina Labwino ndi Mulungu
1. Tifunitsitsa
Chiyanjo cha M’lungu.
Timafunadi
Kumkondweretsabe.
Dzina labwinodi,
Monga tadziŵira,
Tingalipange,
Tiyenera.
2. Mwamawu athu
Tingapeze dzina.
Tikulipanga,
Poti tilifuna.
Tikamka kwa M’lungu,
Tidzapeza dzina
Labwinodi ndi
Madalitso.
3. Tipanga dzina
Momvera Mulungu.
Pokhala moyo,
Izi nzofunika.
Tikatetezera
Mawu Ake ndithu
Adzakhaladi
Bwenzi lathu.
4. Nthaŵi nzoipa,
Tichitepo kanthu,
Kupanga dzina
Ndi Ya, M’lungu wathu.
Tichite zabwino,
Tiyende m’kuŵala
Tifalitse
za Ufumuwo.