Kupangitsa Misonkhano Yathu Kukhala Yosangalatsa
1 Utumiki Wathu Waufumu wa October 1985 unali ndi nkhani yakuti ‘Kusonyeza Kukula Kwauzimu mwa Kutenga Mbali Pamisonkhano.’ Kodi mwatsatira malingaliro amene anaperekedwa? Ngati mwatero, mwina mayankho anu pamisonkhano akumakhala olunjika ndi opindulitsa kwambiri inu ndi ena. Tsopano, tikufuna kunena mfundo ya kupangitsa misonkhano yathu kukhala yosangalatsa ndi kutchulanso mapindu amene tingapeze mwa kukonzekera.
2 Tiyeni tiyerekezere motere. Ngati munali kukonzekera kukaona maiko a Baibulo, chidwi chanu chikanakula kwambiri ngati munayamba mwaŵerenga chidziŵitso chonena za maiko amenewo ndi mbiri yawo imene yasimbidwa m’Baibulo ndi m’mabuku aumboni onga la Insight. Ngati munali wosakonzekera pasadakhale, simukanachita chidwi kwenikweni kuona malo osangalatsa amene anatchulidwa. Nzofanananso ndi kupezeka pamisonkhano yampingo. Mwa kupeza nthaŵi yoŵerenga zimene zikakambidwa kumisonkhano, timakulitsa chikhumbo chathu chofuna kudya mwauzimu ndipo timakhala ofunitsitsa kwambiri kukatengapo mbali yoyankha.
3 Zinthu zofuna nthaŵi yathu zikumawonjezekabe chaka chilichonse. Kodi timapeza bwanji nthaŵi yofunikira kuti tiphunzire? Tiyenera ‘kuwombola nthaŵi’ (NW) pa zinthu zosafunika kwenikweni. (Aef. 5:16) Unyinji wa Mboni za Yehova zimapezeka pamisonkhano yonse isanu ya mlungu ndi mlungu, ndipo ambiri si kuti amachita zimenezo mosavutikira. Kuti tipindule kwambiri ndi nthaŵi ndi khama limene timachita kuti tikafike pamisonkhano, tifunikiranso kuwononga nthaŵi ina yokonzekera pasadakhale.
4 Poyankha, dziŵani kufunika kwa kuyankha molondola, mwachidule, ndi momveka bwino. Kukonzekera pasadakhale kudzakuthandizani. Mutangolandira kope latsopano la Nsanja ya Olonda liŵerengeni lonse. Kenako, pokonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda, chongani mawu ndi mfundo zazikulu zokha. (Chonde onani Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki tsamba 36.) Zimenezo zidzatithandiza kuyankha mwachidule ndi molunjika.
5 Patakhala ambiri ofuna kuyankha, zingakhale zosangalatsa kwenikweni. Zimenezo zingasonkhezere anthu amanyazi kutengamo mbali, akumapereka ndemanga zina zolimbikitsa. Titawagwiritsira ntchito malingaliro ameneŵa, chimwemwe chathu chingakule ndipo misonkhanoyo ingakhale yosangalatsa pamene ‘tikulengeza poyera’ (NW), chikhulupiriro chathu.—Aheb. 10:23.