Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/97 tsamba 3-4
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 9/97 tsamba 3-4

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu September: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. October: Makope a Nsanja ya Olonda kapena a Galamukani! Kuyambira chakumapeto kwa mweziwu, tidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. November: Tidzapitiriza kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. Mipingo imene iti itsirize kufola gawo lawo mwa kufikira eni nyumba ndi kope la Uthenga wa Ufumu Na. 35 panyumba iliyonse, ingagaŵire buku la Chidziŵitso. December: New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina amene iye wamsankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa September 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani kumpingo mutatha kuchita zimenezo.

◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo operekedwa pamasamba 21-3 a Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, onena za wochotsedwa aliyense kapena munthu wodzilekanitsa amene angakonde kubwezeretsedwa.

◼ Amene akugwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikripishoni onse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! atsopano ndi kulembetsanso akale kuphatikizapo masabusikripishoni awoawo, kupyolera mumpingo.

◼ Sosaite siimadzazira munthu aliyense zofunsira mabuku za wofalitsa. Woyang’anira wotsogoza ayenera kuona kuti mwezi uliwonse pazikhala chilengezo asanatumize ku Sosaite chofunsira mabuku a mpingo cha mwezi ndi mwezi, kuti onse ofuna kupeza mabuku awoawo auziretu mbale wosunga mabuku. Chonde kumbukirani kuti ndi mabuku ati amene afunikira oda yapadera.

◼ Pooda mabuku, mipingo iyenera kukumbukira kuti ma CD-ROM a Sosaite amagwiritsiridwa ntchito ndi ofalitsa okha, popeza ali ndi chidziŵitso china chimene sichili cha anthu ena onse.

◼ “Bokosi la Mafunso” mu Utumiki Wathu Waufumu wa May 1997 linalangiza kuti wofalitsa wamwamuna azisamala pamene akugwira ntchito ndi wofalitsa wamkazi mu utumiki. Pali zifukwa zabwino kuti onse azichita mwanzeru pankhani imeneyi. Zimenezi sizikutanthauza kuti oyang’anira oyendayenda kapena abale ena sangagwire ntchito ndi alongo mu utumiki wakumunda. Komatu lingaliro limene linaperekedwa linali lakuti sikwanzeru kuti mbale azipezeka nthaŵi zonse ali ndi munthu mmodzimodziyo wamkazi, yemwe si wachibale wake.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Kodi Nchiyani Chimene Mboni za Yehova Zimakhulupirira? (Trakiti Na. 14)—Chingelezi

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akufa Okondedwa?(Trakiti Na. 16)—Chicheŵa, Chingelezi

Chifukwa Chimene Mungakhulupirire Baibulo (Trakiti Na. 13) —Chicheŵa, Chitonga

Kodi Dzikoli Lidzapulumuka? (Trakiti Na. 19)—Chicheŵa

◼ Makaseti Omvetsera Omwe Alipo:

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chingelezi

◼ Zofalitsa za Akhungu Zomwe Zilipo:

Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?—Chingelezi

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha— Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena