Nyimbo 27
Musawaope!
1. Pitanibe anthu anga,
Ndi mbiri ya Ufumu.
Musawope adani.
Uzani abwinowo
Kuti Mfumu, Yesu Kristu,
Waponyatu m’daniyo,
Satana adzamangidwa,
Mikhole kumasudwa.
(Korasi)
2. Nkana adani anu ndi
Amphamvu ndi ambiri,
Nkana amwetulire,
Kuwanyenga opusa,
Musawope anthu anga;
Limba musakomoke;
Ndidzasunga anthu anga,
Ndi kuwamasulatu.
(Korasi)
3. Sindidzaiŵala inu,
Ndine mphamvu ndi linga.
Nkana mufe pankhondo,
Imfa ndidzagonjetsa.
Musawope anthu anga;
Nkana akuthupseni
Ndidzasunga inu nonse
Monga mwana wadiso.
(KORASI)
Musawope opha thupi.
Moyo sangawononge.
Khala wokhulupirika;
Kufikira mapeto.