Nyimbo 33
Musawaope!
1. Pitanibe anthu anga,
Mulalike uthenga.
Musaope adani.
Anthu onse adziwe
Kuti Mwana wanga Yesu,
Wagwetsadi mdaniyo,
Posachedwa adzam’manga,
Sadzavutitsa anthu.
(KOLASI)
Musaope anthu anga,
Kaya akuopseni.
Ndidzakusamalirani
Monga mwana wa m’diso.
2. Kaya adani n’ngambiri,
Kaya amwetulire
Mwanjira yachinyengo,
Pokusocheretsani.
Musaope anthu anga,
Kaya akuzunzeni,
Ndidzakusamalirani
Mpaka ndiwagonjetsa.
(KOLASI)
Musaope anthu anga,
Kaya akuopseni.
Ndidzakusamalirani
Monga mwana wa m’diso.
3. Sindingakuiwaleni
Ndine Mtetezi wanu.
Ngakhale akupheni,
Ndidzagonjetsa imfa.
Musaope opha thupi
Sangawononge moyo.
Inde, khulupirikani
Mudzalandira mphoto.
(KOLASI)
Musaope anthu anga,
Kaya akuopseni.
Ndidzakusamalirani
Monga mwana wa m’diso.
(Onaninso Deut. 32:10; Neh. 4:14; Sal. 59:1; 83:2, 3.)