Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/00 tsamba 8
  • “Ndingathe Bwanji, Popanda Munthu Wonditsogolera?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndingathe Bwanji, Popanda Munthu Wonditsogolera?”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Kuona Mmene Ntchito Yamwamsanga Yopanga Ophunzira Ikupitira Patsogolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Mmene Tingapangire ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 6/00 tsamba 8

“Ndingathe Bwanji, Popanda Munthu Wonditsogolera?”

1 Mlaliki Filipo atam’funsa mdindo wa ku Aitiopiya ngati anali kumvetsetsa zimene ankaŵerenga m’Mawu a Mulungu, iye anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Mofunitsitsa Filipo anamuthandiza kumvetsetsa uthenga wabwino wa Yesu, ndipo mwamunayo anabatizidwa nthaŵi yomweyo. (Mac. 8:26-38) Potero, Filipo anamvera lamulo la Kristu lakuti ayenera ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza.’—Mat. 28:19, 20.

2 Tiyenera kumvera lamulo lakuti tipange ophunzira, monga anachitira Filipo. Komabe, nthaŵi zambiri anthu amene timaphunzira nawo Baibulo, sapita patsogolo mwauzimu mofulumira monga anachitira mdindo wa ku Aitiopiya. Mwamuna amene uja, amene anali Myuda wotembenuzidwa wodziŵa bwino Malemba, anali ndi mtima wabwino ndipo chomwe chimafunika kwa iye ndicho kukhulupirira kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwayo. Kumakhala kovuta ngati anthu amene timaphunzira nawo sadziŵa Baibulo, ali osocheretsedwa ndi ziphunzitso zachipembedzo chonyenga, kapena ali othedwa nzeru ndi mavuto aakulu amene ali nawo. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tithe kutsogolera ophunzira Baibulo kudzipatulira ndi ubatizo?

3 Zindikirani Zosoŵa Zauzimu za Wophunzira Baibulo: Mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 1998 inafotokoza utali wanthaŵi imene tingatenge pophunzira ndi anthu, pogwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso. Inalangiza motere: “Tiyenera kusintha liŵiro la phunzirolo malinga ndi mikhalidwe ya wophunzirayo ndi kukhoza kwake. . . . Sitikufuna kum’lepheretsa wophunzira kumvetsetsa bwino chifukwa chongoti tifulumire. Wophunzira aliyense amafunikira kumanga maziko olimba okhazikapo chikhulupiriro chake chatsopano cha Mawu a Mulungu.” Chotero, si bwino kuthamanga pophunzira buku la Chidziŵitso n’cholinga chomaliza bukulo m’miyezi isanu ndi umodzi. Anthu ena angafunike miyezi yoposa isanu ndi umodzi kuti apite patsogolo mwakuti n’kubatizidwa. Mlungu uliwonse pochititsa phunziro, khalani ndi nthaŵi imene mungaone kuti ndi yokwanira kuti muthandize wophunzira kumvetsetsa ndi kukhulupirira zimene akuphunzira m’Mawu a Mulungu. Nthaŵi zina, zingatitengere milungu iŵiri kapena itatu kuti timalize mutu umodzi m’buku la Chidziŵitso. Izi zidzatipatsa nthaŵi yoŵerenga ndi kumasulira bwino malemba ambiri amene asonyezedwa.—Aroma 12:2.

4 Komabe, bwanji mutakhala kuti mwamaliza buku la Chidziŵitso, komabe mukuona kuti n’kofunikabe kukhomereza bwino choonadi mwa wophunzirayo kapena kuti sali wofunitsitsadi kuimira choonadi ndi kupatulira moyo wake kwa Mulungu? (1 Akor. 14:20) N’chiyaninso china chimene mungachite kuti mum’tsogolere njira yomuka nayo kumoyo wosatha?—Mat. 7:14.

5 Khutiritsani Zosoŵa Zauzimu za Wophunzira Baibuloyo: Ngati zikuchita kuonekeratu kuti wophunzirayo akupita patsogolo, ngakhale kuli kwapang’onopang’ono, ndiponso akuyamikira zinthu zimene akuphunzira, pitirizani kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito buku lina ngati mwaphunzira naye kale bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso. Izi sizingakhale zoyenera kuchita nthaŵi zonse, koma kokha ngati kuli kofunika kutero, pitirizani phunziro ndi buku la Mtendere, Kulambiridwa, kapena buku la Mawu a Mulungu. Ofalitsa ambiri ali nawo awoawo mabuku ameneŵa oti n’kugwiritsa ntchito ngati mpingo ulibe. Buku la Mawu a Mulungu ndi lokhalo limene mungafunsire ku Sosaite. Nthaŵi zonse, aziyamba kuphunzira bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso. Phunziro la Baibulo, maulendo obwereza, ndi nthaŵi imene mwathera kupitiriza phunziro ziyenera kuperekedwa lipoti, ngakhale ngati wophunzirayo atabatizidwa asanamalize buku lachiŵiri.

6 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti amene abatizidwa posachedwapa atangophunzira buku limodzi akufunika kuyambanso kuphunzira buku lachiŵiri? Ayi. Koma, ayenera kukhala amene anali ofooka kapena amene sanapite patsogolo m’choonadi, ndipo akuona kuti akufunika kuthandizidwa kuti azithadi kugwiritsa ntchito choonadi m’moyo wawo. Muyenera kuonana kaye ndi woyang’anira utumiki musanayambenso phunziro ndi munthu wobatizidwa kaleyo. Komabe, ngati mukudziŵa anthu ena amene anaphunzira buku la Chidziŵitso nthaŵi yam’mbuyomo koma sanapite patsogolo mwakuti n’kudzipatulira ndi ubatizo, mungawafikire kuti muone ngati akufunanso kupitiriza kuphunzira kwawo Baibulo.

7 Kusamalira mwachidwi munthu aliyense wokondwerera amene timaphunzira naye n’chizindikiro cha chikondi chachikristu. Cholinga chathu ndicho kuthandiza wophunzira kudziŵa choonadi chochuluka cha Mawu a Mulungu. Ndiyeno, angagwiritsitse choonadi akudziŵadi zimene akuchita ndipo angapatulire moyo wake kwa Yehova, n’kusonyeza kudzipatulira kwakeko mwa kubatizidwa.—Sal. 40:8; Aef. 3:17-19.

8 Kodi mukukumbukira zimene zinachitika mdindo wa ku Aitiopiya atabatizidwa? “Anapita njira yake wokondwera” monga wophunzira watsopano wa Yesu Kristu. (Mac. 8:39, 40) Ife pamodzi ndi onse amene tikuwatsogolera m’njira ya choonadi tipezetu chimwemwe m’kutumikira Yehova Mulungu—lero ndiponso kwanthaŵi zonse!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena