Kuona Mmene Ntchito Yamwamsanga Yopanga Ophunzira Ikupitira Patsogolo
1 Yesu asanachoke padziko lapansi analamula otsatira ake “kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” Izi zinatanthauza ndaŵala yolalikira ndi kuphunzitsa kwabasi ndi kufikitsa ntchito yawo padziko lonse lokhalidwa ndi anthu. (Mat. 28:19, 20, NW; Mac. 1:8) Kodi anaona ntchito imeneyi ngati chikatundu chosatheka kunyamula? Mtumwi Yohane sanaione motero. Atatha zaka 65 akupanga ophunzira, iye analemba kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yoh. 5:3.
2 Nkhani za m’Malemba zosimba ntchito ya Akristu oyambirirawo zimasonyeza kuti anali kugwira mwachangu ntchito yawo ya kupanga ophunzira a Yesu Kristu. (2 Tim. 4:1, 2) Osati ankangochita ntchitoyo monga mwa ntchito basi, koma kuti ankakhumba mwachikondi kutamanda Mulungu ndi kuuzako ena za chiyembekezo cha chipulumutso. (Mac. 13:47-49) Popeza kuti onse amene ankakhala ophunzira, nawonso ankapanga ophunzira ena, mpingo wachikristu unakula mwamsanga m’zaka za zana loyamba.—Mac. 5:14; 6:7; 16:5.
3 Ntchito Yopanga Ophunzira Ikukangaza: Ntchito yaikulu kwambiri yopanga ophunzira imene sinachitikepo ndi kalelonse ikuchitidwa m’zaka zino za zana la 20! Mmene tikunenamu, anthu mamiliyoni ambiri alandira uthenga wabwino nkuukhulupirira. (Luka 8:15) Popeza kuti nthaŵi ya dongosolo lazinthu lilipoli ikutha mofulumira, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watipatsa ziŵiya zimene zingatheketse anthu oona mtima kuphunzira choonadi mwamsanga.—Mat. 24:45.
4 Mu 1995 tinalandira buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, ndiyeno mu 1996 linadza brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, tsamba 14, ponena za buku la Chidziŵitso inati: “Buku limeneli la masamba 192 lingaphunziridwe m’nthaŵi yofupikirapo, ndipo mwa kuliphunzira, aja ‘ofuna moyo wosatha’ ayenera kukhala okhoza kudziŵa zambiri zowatheketsa kudzipatulira kwa Yehova ndi kubatizidwa.”—Mac. 13:48.
5 Mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, yakuti “Mmene Tingapangire Ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso,” inatiikira cholinga ichi: “Zingakhale zotheka kwa inu kuphunzira mitu yochuluka umodzi pa ola lililonse laphunziro kapena kuposa pamenepo, zikumadalira pa mikhalidwe ndi luso la wophunzirayo, popanda kuthamanga ndi phunzirolo. Ophunzira adzapita patsogolo bwino pamene mphunzitsi ndi wophunzira yemwe asunga lonjezo lawo la phunziro mlungu uliwonse.” Nkhaniyo inapitiriza kuti: “Tiganiza kuti podzafika nthaŵi imene munthu akumaliza phunziro la buku la Chidziŵitso, kuona mtima kwake ndi kuya kwa chikondwerero m’kutumikira Mulungu kudzaoneka.” Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996, linafotokoza kuti: “Tikuyembekezera kuti m’nthaŵi yaifupi, mphunzitsi wabwino adzakhoza kuthandiza wophunzira wabwino woona mtima kupeza chidziŵitso chokwanira kuti apange chosankha chanzeru cha kutumikira Yehova.”
6 Buku la Chidziŵitso Libala Zipatso: Patsiku limene mtsikana wina anabatizidwa, anasimba mmene anamvera pophunzira buku la Chidziŵitso. Kwa nthaŵi yaitali ankaphunzira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Pamene buku la Chidziŵitso linatuluka, mlongo yemwe anali kuphunzira nayeyo anangoyamba nayenso buku latsopanolo. Mwamsanga wophunzirayo anaona kuti limeneli lidzampangitsa kufuna kusankha chochita, ndipo linamsonkhezera kupita patsogolo mwamsanga kuyambira pamenepo. Mtsikanayo, yemwe ndi mlongo wathu tsopano, anati: “Buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha linandithandiza kukonda Yehova, koma buku la Chidziŵitso landithandiza kusankha kumtumikira.”
7 Taonani mmene mkazi wina anaphunzirira choonadi msanga. Ataphunzira maulendo aŵiri, anakakhala nawo pamsonkhano pa Nyumba ya Ufumu panthaŵi imene woyang’anira dera anali kuchezetsa. Mlungu womwewo, paphunziro lake lachitatu, anamuuza woyang’anira derayo kuti anadzipatulira kwa Yehova ndipo ankafuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Mkaziyo anaonana ndi akulu, ndipo anamvomereza kukhala wofalitsa, ndipo mlungu wotsatira anayamba kuloŵa mu utumiki wakumunda. Anayamba kulimbikira kuphunzira Baibulo moti anapempha tchuti kuntchito kuti aziphunzira kaŵiri kapena katatu pamlungu ndi kutinso aziwononga nthaŵi yambiri mu utumiki. Nthaŵi zina ankaphunzira mitu iŵiri kapena itatu nthaŵi imodzi. Mkaziyo anayamba kugwiritsira ntchito zimene anali kuphunzira, anatsiriza buku la Chidziŵitso patatha milungu inayi, ndipo anapita patsogolo mpaka kubatizidwa!
8 Mwamuna wa mlongo wina amadzitcha yekha kuti anali “wosakhulupiriradi.” Tsiku lina, mbale wina anampempha kuphunzira naye Baibulo m’buku la Chidziŵitso, atamuuza mwamunayo kuti angasiye kuphunzira pambuyo pa phunziro loyamba kapena nthaŵi ina iliyonse. Mwamunayo anavomereza kuti ayese, ngakhale kuti kusukulu sankakhoza bwino, ndipo ngakhale kuti anali asanaphunzirepo buku lililonse lachipembedzo kwa zaka zoposa 20. Kodi anati bwanji ataphunzira buku la Chidziŵitso? Anati: “Zinali zosangalatsa kuona kuti buku limeneli lothandizira kuphunzira Baibulo linalembedwa mofeŵa chonchi. Nkhani zake zinafotokozedwa mosavuta ndipo momveka bwino, moti pasanapite nthaŵi, ndinkadikira ndi chidwi phunziro lathu lotsatira. Mphunzitsi wanga ankatsatira mwaluso njira zopangira ophunzira zimene Sosaite inafotokoza, ndipo mzimu wa Yehova unandithandiza moti ndinabatizidwa patatha miyezi inayi. Ndingaterodi kuti tikamakonda kupanga ophunzira, tikamapitirizabe kufunafuna anthu amitima yabwino mu utumiki wakumunda, tikumagwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso ndi mabuku ena othandizira kuphunzira Baibulo omwe Sosaite imapereka, ndipo koposa zonse, tikamapempha Yehova kutitsogoza, tingakhale ndi mwayi wapadera wakuthandiza kupanga ophunzira.” Komabe, zokumana nazo zimene tangotchulazi sizimachitikachitika. Ophunzira athu ambiri samabwera m’choonadi mwamsanga chonchi.
9 Ophunzira Amapita Patsogolo Mosiyanasiyana: Tiyenera kudziŵa kuti maluso a aphunzitsi ndi ophunzira Mawu a Mulungu amasiyana kwambiri. Munthu angakule mwauzimu msangamsanga kapena pang’onopang’ono. Ophunzira ena amapita patsogolo msanga pamiyezi yoŵerengeka kuposa ena. Kukula kwa munthu mwauzimu kumayenderananso ndi mmene anaphunzirira sukulu, mmene amayamikirira zinthu zauzimu, ndi mmene amakondera Yehova. Sikuti aliyense amene timaphunzira naye ‘amafunitsitsa ndi mtima wonse’ kuphunzira Malemba tsiku ndi tsiku, monga ankachitira Abereya akale omwe anakhala okhulupirira.—Mac. 17:11, 12.
10 Nchifukwa chake mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa May 1998, yakuti, “Maphunziro a Baibulo Enanso Akufunika,” inapereka langizo loyenera ili lakuti: “Inde, si ophunzira Baibulo onse amene amapita patsogolo pamlingo wofanana. Ena sakonda kwambiri zauzimu monga amachitira ena ndiponso ena safulumira kugwira zinthu zimene akuphunzira. Ena ali otanganidwa kwambiri ndipo sakhoza kukhala ndi nthaŵi yofunikira kuti amalize mutu wonse mlungu uliwonse. Chotero, kwa ena pangafunikire kuchita phunzirolo kangapo kuti amalize mitu ina ndi miyezi inanso kuti amalize buku lonse.”
11 Opanga Ophunzira Amayang’ana Mbali Zonse: Tiyeneranso kulingalira za liŵiro la phunzirolo malinga ndi mikhalidwe ya wophunzirayo ndi kukhoza kwake. Popeza kuti timalimbikitsidwa kumayamba phunziro ndi brosha lakuti Mulungu Amafunanji, pangapite miyezi iŵiri kapena itatu tisanaloŵe m’buku la Chidziŵitso. Titati tigwiritsire ntchito malingaliro onse amene anafotokozedwa m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, pangapite miyezi ina kuyambira pa isanu ndi umodzi mpaka isanu ndi inayi kuti munthu atsirize buku la Chidziŵitso. Ena amene anayamba phunziro ndi buku la Chidziŵitso anasamukira m’brosha lakuti Mulungu Amafunanji, kuti athandize wophunzirayo kuphunzira choonadi cha Baibulo msanga. Kenako nkudzapitiriza ndi buku la Chidziŵitso. Ngati tinayamba phunziro ndi buku la Chidziŵitso nkuyenda bwino, zingakhale bwinonso kuphunzira brosha lakuti Mulungu Amafunanji titatsiriza bukulo, kuti tipendenso zoyambirira za choonadi cha Mawu a Mulungu. Mulimonsemo, sitikufuna kumlepheretsa wophunzira kumvetsetsa bwino chifukwa chongoti tifulumire. Wophunzira aliyense amafunikira kumanga maziko olimba okhazikapo chikhulupiriro chake chatsopano cha Mawu a Mulungu.
12 Poganizira za pamene tafikapa malinga ndi nthaŵi, tifunika kufulumira kwambiri kuposa ndi kale lonse kuwathandiza ena kuphunzira choonadi. Kuwonjezera pa kupemphera kosaleka kuti tiyambe maphunziro a Baibulo atsopano, tiyeni tizipempherera amene tikuphunzira nawo. Ndiyeno tidzakondwera pomabatiza ophunzira ambiri “masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mat. 28:20.