Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/98 tsamba 5-6
  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 8/98 tsamba 5-6

Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa May 4 kufikira August 24, 1998. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Njira yopita ku ubatizo wachikristu imayamba mwa kuloŵetsa chidziŵitso cholongosoka chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu m’mitima mwathu. [kl-CN tsa. 173 ndime 7]

2. Kumwaza phulusa la mtembo wootchedwa nkosagwirizana ndi Malemba. [w96-CN 9/15 tsa. 30 ndime 6–tsa. 31 ndime 1]

3. Changu chopambanitsa pofuna kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu sichimakhala chifukwa chabwino chochitira zinthu mopanda nzeru, chifundo, ndiponso mosasamala pochita ndi ena. (1 Akor. 13:2, 3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 10/15 tsa. 31 ndime 5.]

4. Tingapeze moyo monga malipiro a kutumikira Yehova Mulungu. [kl-CN tsa. 182 ndime 4]

5. Mawu a pa Agalatiya 5:26 amaletsa Akristu oona kuseŵera maseŵero alionse opikisana. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g95-CN 12/8 tsa. 30 ndime 9.]

6. Pamene Paulo ananena kuti “zida za nkhondo yathu sizili zathupi” pa 2 Akorinto 10:4, iye anali kugogomezera mfundo yakuti Akristu sayenera kugwiritsira ntchito zida zakuthupi, monga chinyengo, kudzitukumula, kapena zida zankhondo, pofuna kutetezera mpingo ku ziphunzitso zonyenga. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani rs-CN tsa. 369 ndime 5.]

7. Kuukitsidwira kumoyo wakumwamba kumatchedwa kuti “kuuka koyamba,” chifukwa chakuti nkumene kukuyamba ndiponso ndiko kofunika koposa. (Chiv. 20:6) [w96-CN 10/15 tsa. 6 ndime 4]

8. Yesu “anayesedwa wolungama mumzimu,” monga momwe 1 Timoteo 3:16 amanenera, mwa kufupidwa ndi moyo wauzimu ataukitsidwa; zimenezi zinasonyeza kuti Mulungu anayesadi Yesu kukhala wolungama ndiponso woyenerera utumiki wina wokwezeka kwambiri. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 1/15 tsa. 13 ndime 12.]

9. “Kuchoka” kotchulidwa pa Afilipi 1:23 mwachionekere ndi chiyembekezo cha Paulo cha kukakhala ndi Kristu atangomwalira. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 3/1 tsa. 30 ndime 5.]

10. Mu 33 C.E., ataukitsidwa ndi kukhala pamalo ake kudzanja lamanja la Mulungu, Yesu anayamba kulamulira ophunzira ake odzozedwa panthaŵiyo. (Akol. 1:13) [gt-CN mutu 132]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Kodi ndi motani mmene ena ku Korinto anali kudyera zizindikiro “kosayenera” atasonkhana kaamba ka Chikumbutso cha imfa ya Kristu? (1 Akor. 11:27) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 2/15 tsa. 19 ndime 17.]

12. Kodi Yehova adzatibwezera motani pa chilichonse chimene tadzimana kaamba ka kulambira kwake? [kl-CN tsa. 169 ndime 20]

13. Kodi nchifukwa chiyani Mkristu ayenera kukhala wofunitsitsa kupepesa ngakhale ataona kuti sanalakwe? [w96-CN 9/15 tsa. 22 ndime 4, 7]

14. Kodi nchifukwa ninji atumwi okhulupirikawo, Yakobo mbale wa Yesu wa atate wina, ndi ophunzira oposa 500 anakhulupirira kuti Yesu waukitsidwa? [gt-CN mutu 131]

15. Kodi nchifukwa ninji chisiriro chikunenedwa kuti ncholingana ndi kulambira mafano? (Akol. 3:5) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w78 4/1 tsa. 21.]

16. Kodi mtumwi Paulo anatanthauzanji pamene ananena kuti Chilamulo “chinawonjezeka chifukwa cha zolakwa”? (Agal. 3:19) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani uw-CN tsa. 146 ndime 3–4.]

17. Kodi “munthu wosayeruzika” ndani? (2 Ates. 2:3) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 1/15 tsa. 12.]

18. Kodi “chinsinsi chopatulika” chimanena za yani kwenikweni? (1 Tim. 3:16, NW) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 9/1 tsa. 12.]

19. Kodi mtumwi Paulo anatanthauzanji pamene ananena kuti akazi “adziveke okha . . . ndi manyazi”? (1 Tim. 2:9) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g90 7/8 tsa. 19 ndime 2.]

20. Kodi ndi mwa njira ziŵiri ziti zimene akulu angagogomezerere kufunika kwa uphungu wa Mulungu wa kukwatira “mwa Ambuye”? (1 Akor. 7:39) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w82 3/15 tsa. 31.]

Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Abale ayenera kuona akazi achikulire mumpingo monga ․․․․․․․ ndipo akazi aang’ono monga ․․․․․․․ mwachiyero chonse. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w73 tsa. 540.]

22. Pamene ․․․․․․․ anadzipatula kwa okhulupirira Akunja a ku Antiokeya chifukwa choopa Ayuda achikristu ochokera ku Yerusalemu, ․․․․․․․ anamdzudzula. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 11/15.]

23. Paulo anatonthoza mtima Afilipi ponena za ․․․․․․․ amene anali atadwala kwambiri. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 11/15.]

24. Ubatizo umakhala ․․․․․․․ cha utumiki wa moyo wonse kwa Mulungu monga ․․․․․․․ ndiponso mmodzi wa Mboni za Yehova. (Mat. 24:13) [kl-CN tsa. 178 ndime 17]

25. Popeza kuti nkovuta kudziona mmene ena amationera, chimene tingachite ndicho kufunsa makolo athu kapena ․․․․․․․ kuti atiuze mosabisa ponena za umunthu wathu. [fy-CN tsa. 16 ndime 7]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Mwinamwake atasonkhezeredwa ndi ( filosofi yachigiriki; kutengeka maganizo; Malemba Achihebri), ena mumpingo wa ku Korinto ankanena kuti kulibe kuuka kwa akufa. (1 Akor. 15:32) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 9/15 tsa. 25.]

27. Pa 2 Akorinto 3:18, Paulo akusonya ku chokumana nacho cha ( Mose; Yoswa; Eliya). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 9/15 tsa. 26.]

28. Pa 1 Akorinto 12:31, “njira yokoma yoposatu” ndiyo njira (ya choonadi; ya chikondi; ya moyo wodzala ndi mphatso zauzimu). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 7/15 tsa. 27 ndime 3.]

29. (Ayuda Osunga Mwambo; atsogoleri achipembedzo a m’Dziko Lachikristu; Babulo Wamkulu) ndiye “munthu wosayeruzika” wotchulidwa pa 2 Atesalonika 2:3. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 1/15 tsa. 18 ndime 11.]

30. Ngati pali zimene mukukayikira kwambiri mwa munthu amene muli naye pachibwenzi, chinthu chanzeru chimene mungachite ndicho (kulola chikondi chanu kuthetsa zikayiko zanu; kuthetsa chibwenzicho; kunyalanyaza zododometsa zazikulu ndi chiyembekezo chakuti zinthu zidzawongokera mutakwatirana). [fy-CN tsa. 24 ndime 19]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

1 Ates. 5:8; 2 Akor. 4:7; 2 Akor. 8:14; Afil. 4:6, 7; 2 Ates. 1:8, 9, 12

31. Pamene munthu aika utumiki wachikristu patsogolo m’moyo wake, iye amalandira mphamvu yochokera kwa Mulungu. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 3/1 tsa. 29 ndime 5.]

32. Kuti Akristu akhalebe okhulupirika, iwo afunikira zida zankhondo zauzimu zimenezi. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 1/15 tsa. 22.]

33. Mphatso zoperekedwa mooloŵa manja ndi Akristu achuma zingathandize kusamalira zosoŵa za awo amene ali kumalo osoŵa, pamene kuli kwakuti changu ndi chipiriro cha ovutikawo zingadzetse chimwemwe ndi chilimbikitso kwa operekawo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 12/15 tsa. 21 ndime 20.]

34. Sitiyenera kuleka kulalikira uthenga wabwino, popeza malinga nkunena kwa Baibulo, anthu onse amoyo lerolino amene adzakhalapo mpaka mapeto a dongosolo loipali ndipo amene adzaweruzidwa monga adani a kulambira koona adzawonongedwa kosatha. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 5/1 tsa. 19 ndime 4.]

35. Yehova amapereka mtendere ndi bata pakati pa mayesero aakulu kwambiri. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 11/1 tsa. 30 ndime 19-20.]

S-97-CN Zam, Mal & Moz #295b 8/98

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena