Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kusonkhanitsa “Zofunika” mu Poland
    Nsanja ya Olonda—1992 | July 15
    • nayamba ‘kupereka chilango’ ndi chikoti. Ndinamenyedwa ndi kupondedwa m’mbali zonse zathupi langa kokha chifukwa chosonkhana ndi Mboni. Ndinamenyedwa kwadzawoneni kotero kuti ndinafunikira chisamaliro chamankhwala chamwamsanga ndipo ndinaperekedwa kuchipatala. Yehova anandithandiza, ndipo ndinachira. Banja langa linandinyanyala. Pamene ndinanena zimenezi kwa wansembe, anandinyodola, kumati: ‘Kodi ungabwere kudzadandaula kokha chifukwa chakumenyedwa makofi pang’ono?’”

      Mlongo wina akukumbukira kuti: “Chaka chirichonse ndinkapita ku Częstochowa kukayenda ndi mawondo padzoma la Mtanda, zimene ndinalingalira kukhala thayo la Mkatolika aliyense wowona mtima. Ndikali nazo zipsera m’mawondo anga.” Pamene anali ndi zaka 18 zakubadwa anaphunzira chowonadi ndipo anauza wansembe ndi banja lake kuti sakapitanso kutchalitchi. Anamenyedwa kwadzawoneni​—“kwadzawoneni ndithu kotero kuti ubongo wanga unavulala ndi kugwedezeka,” akusimba motero. “Koma m’chipatalamo ndinachira mokwanira kotero kuti ndinafika pa Msonkhano Wachigawo wa ‘Okonda Ufulu.’ Ndinagwetsa misozi yachimwemwe pamene ndinawona chigwirizano chowona ndi chikondi pakati pa anthu osatengeka maganizo​—zinthu zimene sindinaziwonepo ku Częstochowa. Ndiri wachimwemwe chotani nanga kuti ndawona ubwino wa Yehova ndipo ndaphunzira kumdalira.” Yehova amalimbitsa ndi kuchirikiza amene amamsenza nkhaŵa zawo.​—Salmo 55:22.

      Akopolo ambiri a Babulo Wamkulu tsopano akulabadira chiitano ‘chakutuluka mwa iye’ m’dziko limeneli Lachikatolika, monga momwenso akuchitira m’maiko ena. Ngati chiri chifuniro cha Yehova, anthu ake opanda mantha adzapitirizabe kusonkhanitsa ena owonjezereka a “zofunika” omwazikana m’Poland monse. Ndithudi, ambiri adzalabadirabe chiitano chakuti: “Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”​—Chivumbulutso 18:4; 22:17.

  • Tsatirani Njira Yopambana ya Chikondi
    Nsanja ya Olonda—1992 | July 15
    • Tsatirani Njira Yopambana ya Chikondi

      YEHOVA MULUNGU iyemwiniyo ndiye chikondi. (1 Yohane 4:8) Mwana wake, Yesu Kristu, ananena kuti tiyenera kukonda Mulungu ndi mnansi wathu. (Mateyu 22:37-40) Eya, Mulungu amayendetsa chilengedwe chonse pamaziko a mkhalidwe umenewu! Chotero kaamba ka moyo wamuyaya kulikonse, tiyenera kutsatira njira ya chikondi.

      Mulungu anasonyeza chikondi kumtundu wa Israyeli koma pambuyo pake anakana gulu limenelo chifukwa cha kusakhulupirika. Iye kenako anasonyeza mpingo wa ophunzira a Yesu kukhala gulu Lake latsopano. Motani? Mwa zisonyezero zapadera za mzimu woyera ukumawapatsa mphamvu za kulankhula m’malilime ndi kulosera. Chotero, pa Pentekoste wa 33 C.E., Ayuda ndi otembenuka 3,000 anafikira kukhala okhulupirira ndipo anasiya gulu lakale moyanja la Mulungu latsopanolo. (Machitidwe 2:1-41) Popeza kuti mphatso za mzimu pambuyo pake zinaperekedwa kupyolera mwa atumwi a Yesu, zizindikirozo zinalekeka iwo atafa. (Machitidwe 8:5-18; 19:1-6) Koma podzafika panthaŵiyo mphatsozo zinali zitatsimikizira kuti chiyanjo cha Mulungu chinali pa Israyeli wauzimu.​—Agalatiya 6:16.

      Zozizwitsa zochititsidwa ndi mphatso za mzimu zinali zopindulitsa. Komabe, kusonyeza chikondi kapena kuderera nkhaŵa ena mopanda dyera nkofunika kwambiri koposa kukhala

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena