Kusonkhanitsa “Zofunika” mu Poland
POLAND amanenedwa kukhala dziko Lachikatolika. Malinga ndi ziŵerengero za boma, 93 peresenti ya anthu onse nga Tchalitchi cha Katolika. Komabe, masinthidwe aposachedwa andale zadziko ndi makhalidwe a anthu ochitika kumeneko akhala ndi chiyambukiro chachikulu pa anthu ndi moyo wawo wachipembedzo. Kufufuza kumasonyeza kuti pafupifupi 50 peresenti yokha ya omwe anafunsidwa amadziyesa kukhala olondola Chikatolika.
Mu May 1989, Mboni za Yehova zinavomerezedwa mwalamulo kukhala kagulu kachipembedzo m’Poland. Chiyambire nthaŵiyo, pafupifupi atsopano 11,000 agwirizana nawo monga ofalitsa mbiri yabwino ya Ufumu. Tsopano ofalitsa Ufumu oposa 106,000 amapanga mipingo yoposa 1,300, ndipo anthu okwanira 200,422 anafika paphwando la 1991 la Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Motero, kusonkhanitsidwa konenedweratu kwa ‘zofunika za amitundu’ kukuchitika m’Poland. (Hagai 2:7) Posachedwapa, misonkhano ya mitundu yonse yotchuka ya Mboni za Yehova inachitikira m’Poland. Koma kupenda ena a matauni aang’ono m’malo akumidzi kudzasonyeza kwenikweni mmene ntchito yosonkhanitsayo ikuyendera m’dzikolo.
Apainiya Alambula Njira
Sztum nditauni la anthu pafupifupi 10,000 lokhala pafupi ndi pamene Mtsinje wa Vistula umatsirira m’Nyanja ya Baltic. Kwazaka zambiri tauni limeneli lalingaliridwa kukhala gawo lovuta kuchitiramo ntchito yolalikira. Mu 1987 munali kokha ofalitsa asanu ndi atatu m’deralo. Komabe, zinthu zinayamba kusintha pamene apainiya, kapena olengeza Ufumu anthaŵi yonse, anafika. Pamsonkhano wachisanu, wochitidwira m’nyumba ya kanema, anthu okondwerera okwanira 100 anafika! Mpingo unapangidwa pambuyo pa zaka ziŵiri zakuyesayesa kolimba. Tsopano ofalitsa okwanira 90 ali ndi Nyumba yawo Yaufumu, ndipo anthu 150 amafika pamisonkhano yawo nthaŵi zonse.
Monga chodziŵadziŵa, chitsutso chamwamsanga chinachokera ku Tchalitchi cha Katolika. Mvirigo woyesedwa “katswiri” anakamba nkhani zonyoza Mboni, akumaziimba mlandu wophunzitsa ziphunzitso zonyenga. Koma monga momwe zimakhalira kaŵirikaŵiri, zimenezo zinamtembenukira. Maulaliki ake anangopangitsa anthu kufufuza zenizeni. Ambiri a iwo aphunzira chowonadi ndipo tsopano ali apainiya anthaŵi yonse! Iwo amati: ‘Pamene tinkaphunzira chowonadi, tinaganiza kuti aliyense wofuna kukhala Mboni anayenera kukhala ngati mphunzitsi wake, zimene zinatanthauza kukhala mpainiya.’ Choncho mzimu waupaniya ngwofunga mumpingo wonse.
Chotero, pafupifupi maphunziro Abaibulo apanyumba 180 akuchitidwa m’deralo. Mwakugwiritsira ntchito bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, ena aphunzitsidwa ngakhale kuŵerenga. Panthaŵi imodzimodziyo, aphunzira chowonadi. Maphunziro Abaibulo anthaŵi zonse amphindi khumi amachitidwa ndi kagulu ka akaidi m’ndende yakomweko pamene atulukira kunja kukasesa makwalala. Mmodzi wa iwo anatetezera Mboni pamene mkazi wina wodutsa chapafupipo anayamba kulalatira mlongoyo. Mkaidiyo anathamangira kwa mlongo, namlanda bukhu la Kukhala ndi Moyo Kosatha m’dzanja lake, nalitukula, nafunsa mkazi wachipongweyo kuti: “Kodi udziŵa kuŵerenga? Chalembedwa apa nchiyani? Ungathe kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi! Kodi unamvapo nkhani yotereyi? Uchitiranji mwano Mulungu ndi olambira ake?”
Nkhani Yofala
Kruszwica, lomwe kale linali likulu la Poland malinga ndi nthano, liri phata Lachikatolika. Ngakhale pofika pakati pake pa 1990, munali Mboni zoŵerengeka zokha mwa nzika zake 9,300. Koma dalitso la Yehova lolemera linali pa zoyesayesa za olengeza Ufumu.
Powona chinyengo cha atsogoleri awo auzimu, anthu ambirimbiri—makamaka achichepere—anatembenukira kwa Mboni kaamba ka mayankho. Mosataya nthaŵi, maphunziro Abaibulo 20 anakhazikitsidwa. Wansembe wa deralo anapereka maulaliki oneneza Mboni za Yehova, koma zimenezi sizinalefule anthu owona mtima kufika pamisonkhano yawo. Mboni zinakhala mutu wankhani wokambirana m’masitolo ndi m’mapaki ndipo ngakhale m’tchalitchi momwe. Pambuyo pa theka la chaka, timagulu tatikulu tiŵiri taphunziro labukhu tinapangidwa. Tsopano ku Kruszwica kuli mpingo wokangalika wa olambira a Yehova pafupifupi 35. Iwo akuchititsa maphunziro Abaibulo apanyumba 75 ndipo ngotanganitsidwa kubweretsa “zofunika” zomwe panthaŵi ina zinali muukapolo wa chipembedzo chonyenga.
Pakati pa ameneŵa panali Bogdan wazaka zakubadwa 23, chiŵalo cha banja lodzipereka ku Chikatolika. Iye akukumbukira kuti: “Ndinali kumwa, kusuta, ndipo ndinali wachisembwere. Ndinadziŵika monga wachipanki ndi wachipolowe, ndipo aliyense anawonekera kukhala wosadera nkhaŵa. Komabe, pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo, amayi anandiwopsa kuti akamwa poizoni. Pokhala wosakhoza kupirira chitsenderezocho, ndinalekeratu kugwirizana ndi Mboni. Pambuyo pake, mwachithandizo chachikondi cha apainiya apadera, ndinakhoza kuwonjoka kuzizoloŵezi zonse zoipa. Popeza kuti ndinabatizidwa pa Msonkhano Wachigawo wa 1991 wa ‘Okonda Ufulu,’ ndasankha uminisitala wanthaŵi yonse kukhala chonulirapo changa m’moyo ndipo ndakhala ndikuchita upainiya wothandiza chiyambire nthaŵiyo.”
Sławomir wazaka zakubadwa makumi aŵiri mphambu chimodzi anali muukapolo wa kukhulupirira mizimu ndi kulambira Satana, zimene anasiya atazindikira kuti Baibulo limatsutsa zizoloŵezi zotero. “Koma Satana anandiumirira,” iye akutero. “Usiku wina rekodi puleya inayamba kuimba popanda kuitsegula, ndipo ndinamva nyimbo zauchiŵanda, ngakhale kuti ndinali nditachotsa m’nyumba zinthu zonse zophatikizapo kulambira Mdyerekezi. Ndinapemphera kwa Yehova, ndipo anandithandiza kupezanso nyonga yauzimu. Katswiri wanthenda zamaganizo amene ndinkapitako mochichizidwa ndi makolo anga anazindikira kuwongokera kwakukulu kwa mkhalidwe wanga nanena kuti ndinachira. Iyeyo analemba patchati changa kuti: ‘Anachiritsidwa ndi Mboni za Yehova.’”
Kukana Mzimu Waudziko
Kum’mwera koma chakumadzulo kwa Kruszwica kuli Środa Śląska. “Zofunika” zikuwonekeranso m’tauni limeneli la anthu 9,000. Zaka zinayi zapitazo, kunali mlongo wathu wauzimu mmodzi yekha komweko. Komabe, tsopano, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chawonjezereka kufika pa 47. Ambiri a Mbonizo panthaŵi ina anali ogwidwa mumsampha wa kukhulupirira mizimu, kumwerekera ndi anamgoneka, ndi chisembwere. Iwo amaganiza kuti kwakukulukulu zimenezi zinali chifukwa cha njala yauzimu yopezeka m’tchalitchi chimene chiri chokhoza kutemberera anthu mwauzimu basi, osati kuŵathandiza. Mboni zikupereka mpumulo weniweni kwa anthuwo.
Achichepere mumpingo apanga sukulu kukhala gawo lawo kaamba ka ntchito yolalikira. “Kaŵirikaŵiri anzanga apasukulu amandiuza kuti: ‘Ukuwononga ubwana wako,’” akusimba tero Kasia wazaka zakubadwa 18. “Komatu ine ndapeŵa mavuto ambiri, ndipo moyo wanga wakhala watanthauzo. Ndimachititsa maphunziro Abaibulo angapo kusukulu ndipo sindimanyalanyaza homuweki kapena phunziro laumwini. Asungwana amene amanena kuti ‘ndikuwononga ubwana wanga’ akhala kale anakubala, akumalimbana ndi mtolo wa mavuto.”
Mabukhu a Watch Tower akhala otchuka kwambiri m’sukulu zakonko. Mwachitsanzo, mphunzitsi wina wa Chipolishi anauza ana ake a sukulu kutsanzira chinenero chosavuta cha magazini athu a Galamukani! monga chitsanzo polemba nkhani zawo. Mpainiya wothandiza Ewa amapeza brosha la School and Jehovah’s Witnesses kukhala lothandiza kwambiri. “Ndimakonda kwambiri bukhu limeneli. Aphunzitsi anga ngozoloŵerana nalo bwino lomwe. Sindinakhalepo ndi vuto lirilonse popempha chilolezo chosabwera kusukulu kotero kuti ndipite kumisonkhano yaikulu.” Kaimidwe kotero mwa achichepere kamakondweretsa mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.
Apandu Okakala Asinthidwa
Kum’maŵa kwa Środa Śląska kuli Strzelce Opolskie, kumene kuli ndende ziŵiri. Imodzi ndindende yotchinjirizidwa kwambiri ya apandu osaweruzika. Mboni zimapita kumalo okhaulitsira ameneŵa mokhazikika kupereka chowonadi kwa andende, amene ambiri a iwo analinso muukapolo wa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga.—Chivumbulutso 18:1-5.
Mbonizo zimaphunzira Baibulo ndi akaidi alionse paokha ndi timagulu ta akaidi, amene ena a iwo abatizidwa. Ngakhale kuti ayenera kumaliza chilango chawo m’ndendemo, akulalikira mbiri yabwino mokangalika kwa akaidi anzawo. Mkaidi wina wokonzekera ubatizo anapanga masinthidwe aakulu kwambiri kotero kuti akuluakulu a ndende anamlola kupita kunyumba kamodzi pamlungu. Ena alembera mabanja awo makalata osonyeza kufunitsitsa kwawo kutuluka m’ndende, osati monga apandu, koma monga Mboni za Yehova.
Ofisala wamkulu wa imodzi ya ndendezo anadandaula kuti ansembe Achikatolika ankabwera koma sanapindulepo kalikonse. Anafunsa Mbonizo kuti: “Kodi chimakukhozetsani nchiyani kusintha ndi kukonzanso anthu aŵa?” Kalata yochokera kwa mkaidi wina kupita kubanja lake ikuyankha kuti: “M’ndende muno, Mboni za Yehova zandiuza za lonjezo labwino kwambiri la Mulungu lonena za boma latsopano, Ufumu wa Yehova, umene posachedwapa udzalamulira dziko lapansi. Kunoko ndakhala ndi nthaŵi yopenda moyo wanga wapapitapo mwakugwiritsira ntchito Baibulo. Popeza ndapeza kuti uli ndi zotulukapo zowopsa, ndiri ndi chikhumbo chachikulu chakukhala munthu waufulu ndi kukhala nzika ya Ufumu wa Mulungu. Tsopano ndine Mboni yobatizidwa ya Yehova.”
M’ndende ina, ambiri akutumikira chilango cha zaka 25 chifukwa cha kuchita mbanda. Phunziro Labaibulo lokhazikika likuchitidwa ndi amuna 12. Mmodzi wa iwo anapatulira moyo wake kwa Yehova ndipo anabatizidwa, ndipo pali ena amene akukonzekera kutenga masitepe ameneŵa. Poyamikira zotulukapo zabwino za kaphunzitsidwe kogwiritsiridwa ntchito ndi Mboni za Yehova, ofisala wamkulu wa ndendeyo anati: “Sindiri chabe ndi akaidi 12. Ndiri nawo 600. Chonde ndithandizeni kuwakonzanso. Ndidzakupatsani zirizonse zimene mufuna, koma chonde linganizani programuyo. Asamalireni!”
Abale anachitadi zimenezo. Analinganiza programu Yabaibulo yofotokoza chifuno cha moyo, chiyembekezo cha mtsogolo, ndi kufunika kwa kuleka zizoloŵezi zoipa. Anasimbanso zokumana nazo za yemwe kale anali mkaidi amene anadzakhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndiyeno mkupita kwa nthaŵi anaikidwa monga mkulu mumpingo. Mbonizo zinatchulanso mfundo zazikulu zotengedwa m’mbiri za moyo wa mbala yoba diamondi ndi yogwiritsira ntchito anamgoneka zimene zinaphunzira chowonadi.a Akaidi 20 ofikapo anapeza programuyo kukhala yokondweretsa kwambiri nafunsa mafunso ambiri, ena anapempha ndi phunziro Labaibulo lomwe.
Chikhulupiriro ndi Chipiriro Ziyesedwa
Lubaczów nditauni laling’ono la anthu 12,000 lokhala pafupi ndi malire a Ukraine. Ntchito yolalikira kumeneko inayamba kuwonjezereka mu 1988 pamene apainiya anasamukirako kukathandiza ofalitsa 12 akomweko. Tsopano kuli ofalitsa Ufumu okangalika 72, ndipo anthu 150 anafika paphwando la 1991 la Chikumbutso m’Nyumba Yaufumu yomangidwa chatsopano.
Mu June 1991, Papa John Paul II anayendera Lubaczów. Koma zimenezo sizinakwaniritse kalikonse kukulitsa chikhulupiriro mwa anthu. Ambiri a iwo ngokanthidwa ndi zikaikiro ndi mafunso onena za chifuno cha moyo ndi chiyembekezo cha mtsogolo. Pamene sakhoza kupeza mayankho okhutiritsa kwa atsogoleri achipembedzo, amatembenukira kwa Mboni za Yehova. Ngakhale kuti poyamba anthuwo angavutike ndi chikumbumtima chifukwa chosiya chipembedzo chawo, chowonadi cha Baibulo chimene amaphunzira chimaŵathandiza kuwona kuti apanga chosankha cholondola.
Chitsanzo chabwino ndicho chokumana nacho cha Honorata, amene tsopano ali mpainiya wokhazikika. Pafupifupi chaka chimodzi chapitacho, anafunsa wansembe panthaŵi yakuulula machimo kumuuza dzina la Mulungu. “Mulungu ndiye chikondi—limenelo ndilo dzina lake laulemerero koposa,” anayankha motero wansembeyo. Patapita kanthaŵi, anawonjezera kuti: “Uli ngati chitini cha madzi oyera ngati krustalo mmene munthu wina wadonthetsera inki. Ziyambukiro ziri zosakhoza kusintha.” Motero mkaziyo anapeza yankho. “Pamenepo ndinasankha kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova,” akutero Honorata. “Ndiponso zimenezo nzosasinthika.”
Pafupifupi aliyense amene anaphunzira chowonadi ku Lubaczów anafunikira kupirira chitsutso champhamvu, ngakhale chankhanza. Koma zimenezo sizinawalefule kulandira chowonadi cha Baibulo ndi kutenga kaimidwe kawo kumbali ya Yehova.
Elżbieta akusimba kuti: “Poyamba makolo anga anandimenya tiri kunyumba. Ndiyeno banja langa linadzaloŵa mwaukali m’Nyumba Yaufumu. . . . Ananditengera kunyumba nayamba ‘kupereka chilango’ ndi chikoti. Ndinamenyedwa ndi kupondedwa m’mbali zonse zathupi langa kokha chifukwa chosonkhana ndi Mboni. Ndinamenyedwa kwadzawoneni kotero kuti ndinafunikira chisamaliro chamankhwala chamwamsanga ndipo ndinaperekedwa kuchipatala. Yehova anandithandiza, ndipo ndinachira. Banja langa linandinyanyala. Pamene ndinanena zimenezi kwa wansembe, anandinyodola, kumati: ‘Kodi ungabwere kudzadandaula kokha chifukwa chakumenyedwa makofi pang’ono?’”
Mlongo wina akukumbukira kuti: “Chaka chirichonse ndinkapita ku Częstochowa kukayenda ndi mawondo padzoma la Mtanda, zimene ndinalingalira kukhala thayo la Mkatolika aliyense wowona mtima. Ndikali nazo zipsera m’mawondo anga.” Pamene anali ndi zaka 18 zakubadwa anaphunzira chowonadi ndipo anauza wansembe ndi banja lake kuti sakapitanso kutchalitchi. Anamenyedwa kwadzawoneni—“kwadzawoneni ndithu kotero kuti ubongo wanga unavulala ndi kugwedezeka,” akusimba motero. “Koma m’chipatalamo ndinachira mokwanira kotero kuti ndinafika pa Msonkhano Wachigawo wa ‘Okonda Ufulu.’ Ndinagwetsa misozi yachimwemwe pamene ndinawona chigwirizano chowona ndi chikondi pakati pa anthu osatengeka maganizo—zinthu zimene sindinaziwonepo ku Częstochowa. Ndiri wachimwemwe chotani nanga kuti ndawona ubwino wa Yehova ndipo ndaphunzira kumdalira.” Yehova amalimbitsa ndi kuchirikiza amene amamsenza nkhaŵa zawo.—Salmo 55:22.
Akopolo ambiri a Babulo Wamkulu tsopano akulabadira chiitano ‘chakutuluka mwa iye’ m’dziko limeneli Lachikatolika, monga momwenso akuchitira m’maiko ena. Ngati chiri chifuniro cha Yehova, anthu ake opanda mantha adzapitirizabe kusonkhanitsa ena owonjezereka a “zofunika” omwazikana m’Poland monse. Ndithudi, ambiri adzalabadirabe chiitano chakuti: “Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 18:4; 22:17.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani Galamukani! (Wachingelezi) wa October 8, 1983, tsamba 16-19, ndi November 22, 1987, tsamba 21-3.
[Mapu patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
POLAND
Sztum
Kruszwica
Poznan
Warsaw
Środa Śląska
Częstochowa
Strzelce Opolskie
Lubaczów
[Chithunzi patsamba 26]
Kulalikira uthenga Waufumu m’Kruszwica, Poland