Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/15 tsamba 22
  • Msonkhano Wapachaka—October 3, 1992

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano Wapachaka—October 3, 1992
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Msonkhano Wapachaka—October 3, 1992
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Msonkhano Wapachaka—October 5, 1991
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Msonkhano Wapachaka—October 5, 1991
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Msonkhano wa Pachaka
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/15 tsamba 22

Msonkhano Wapachaka​—October 3, 1992

MSONKHANO WAPACHAKA wa ziŵalo za Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitidwa pa October 3, 1992, pa Nyumba Yamsonkhano ya Mboni za Yehova, 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, New Jersey. Msonkhano woyambirira wa ziŵalo zokha udzakhalako pa 9:30 a.m, wotsatiridwa ndi msonkhano wapachaka wa onse pa 10:00 a.m.

Ziŵalo za bungwe la Corporation ziyenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano zakusintha kulikonse kwa makeyala awo olandirira makalata kumene kungakhale kutachitika mkati mwa chaka chapitacho kotero kuti zikalata zanthaŵi zonse zoperekera chidziŵitso ndi zikalata zoponyera mavoti zikawafikire mwamsanga pambuyo pa August 1.

Zikalata zoponyera mavoti, zomwe zidzatumizidwa kwa ziŵalo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wapachaka, ziyenera kubwezedwa kotero kuti zifikire Ofesi ya Mlembi wa Sosaite osati pambuyo pa August 15. Chiŵalo chirichonse chiyenera kulemba ndi kubweza mwamsanga chikalata chake choponyera voti, akumanena kuti kaya adzafika iye mwini pamsonkhanopo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pachikalata choponyera voti chirichonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pamfundo imeneyi, popeza kuti ndicho chimene chidzagwiritsiridwa ntchito kudziŵira amene adzafikapo iwo eni.

Tikuyembekezera kuti programu yonse, kuphatikizapo msonkhano wokambitsirana ntchito ndi malipoti, zidzamalizidwa podzafika 1:00 p.m. kapena mwamsanga pambuyo pake. Sipadzakhala programu yamasana. Chifukwa chakuchepa kwa malo, ofikapo adzaloledwa kokha ngati ali ndi tikiti. Palibe makonzedwe amene adzapangidwa a kulunzanitsa msonkhano wapachakawu ndi malo ena mwa nsambo za telefoni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena