Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/99 tsamba 3-6
  • Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2000

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2000
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Timitu
  • Malangizo
  • NDANDANDA
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 10/99 tsamba 3-6

Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2000

Malangizo

Mu 2000, otsatiraŵa ndiwo adzakhale makonzedwe pochititsa Sukulu ya Utumiki Wateokalase.

MABUKU OPHUNZIRA: Revised Nyanja (Union) Version [bi53], Nsanja ya Olonda [w-CN], Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki [sg-CN], Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN], ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo [my-CN], adzakhala magwero a nkhani zimene zidzagaŵiridwa.

Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje. Palibe chifukwa choperekera chithunzithunzi cha zimene zili pa pologalamu. Pamene woyang’anira sukulu aitanira mbali iliyonse, iye ndiye adzatchula nkhani imene idzakambidwa. Ndiyeno n’kupitiriza motere:

NKHANI NA. 1: Mphindi 15. Imeneyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira, ndipo idzatengedwa mu Nsanja ya Olonda kapena mu Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki. Ngati yatengedwa mu Nsanja ya Olonda, iyenera kukambidwa monga nkhani yachilangizo ya mphindi 15 yopanda mafunso openda; ngati yatengedwa mu Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki ikambidwe ngati nkhani yachilangizo ya mphindi 10 mpaka 12, kenako mphindi 3 mpaka 5 za mafunso openda, kugwiritsira ntchito mafunso osindikizidwa m’bukulo. Cholinga chake sichiyenera kukhala cha kungokamba nkhaniyo koma kusamalira kwambiri za phindu lenileni la chidziŵitso chimene chikufotokozedwa, mukumagogomezera mfundo zomwe zidzakhala zothandiza kwambiri mpingowo. Gwiritsirani ntchito mutu wosonyezedwa.

Abale opatsidwa nkhani imeneyi ayenera kukhala osamala kusunga nthaŵi. Ngati muti muwapatse uphungu wamseri, pasilipi lawo la uphungu wakulankhula mungalembepobe mfundo zoyenera.

MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 6. Nkhaniyi iyenera kukambidwa ndi mkulu kapena mtumiki wotumikira amene adzagwiritsira ntchito mfundozo pa zofunika za kumaloko. Mutu wa nkhani n’ngwosafunikira kwenikweni. Siyenera kukhala chidule wamba cha kuŵerenga kwa mlunguwo. Choyamba perekani chithunzi chachidule cha machaputala onse a mlunguwo pa masekondi 30 mpaka 60. Komabe, cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvetsera kuzindikira chifukwa chake ndi mmene chidziŵitsocho chilili chaphindu kwa ife. Ndiyeno woyang’anira sukulu adzauza ophunzirawo kupita kumakalasi awo osiyanasiyana.

NKHANI NA. 2: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya kuŵerenga Baibulo kwa mbali yogaŵiridwa kochitidwa ndi mbale. Nkhaniyi idzakambidwa m’sukulu yaikulu limodzinso ndi m’timagulu tinato. Kaŵirikaŵiri mbali zoŵerenga zimakhala zazifupi mololeza wophunzira kukamba mawu oyamba ndi omaliza achidule opereka chidziŵitso pankhaniyo. Zingaphatikizepo mbiri yakale, tanthauzo la ulosi kapena la chiphunzitso, ndi mmene mapulinsipulo angagwirire ntchito. Mavesi onse ogaŵiridwa ayenera kuŵerengedwa mosalekeza. Komabe, pamene mavesiwo saali ondondozana, wophunzira angatchule vesi lopitirizira kuŵerengako.

NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhaniyi idzapatsidwa kwa mlongo. Idzatengedwa m’buku la “Kukambitsirana za m’Malemba.” Chochitikacho chingakhale umboni wamwamwayi, ulendo wobwereza, kapena phunziro la Baibulo la panyumba, ndipo otenga mbaliwo angakhale pansi kapena kuimirira. Woyang’anira sukulu adzafuna makamaka kuona mmene wophunzirayo adzafotokozera mutu wogaŵiridwawo ndi kuthandiza mwininyumba kusinkhasinkha malemba. Wophunzira wopatsidwa nkhani imeneyi ayenera kudziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi, koma mukhoza kugwiritsira ntchito wothandiza winanso. Chimene chiyenera kusamalidwa kwambiri, si mkhalidwe wa chochitikacho, koma kugwiritsira ntchito Baibulo kogwira mtima.

NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Mutu wa nkhani imeneyi udzatengedwa mu “Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo” kapena m’buku la “Kukambitsirana za m’Malemba.” Pamene yatengedwa mu “Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo,” wophunzirayo ayenera kufufuza Malemba amene alembedwa m’nkhaniyo n’cholinga choti amvetsetse cholinga chenicheni cha nkhani ya Baibuloyo. Kenako, afotokozere mutu wogaŵiridwawo ndi kusankha malemba oyenerera kuwagwiritsa ntchito. Malemba owonjezera amene akugwirizana ndi nkhaniyo angaphatikizidwe. Cholinga chosankhira nkhani ya Baibulo ndicho kuonetsa chomwe chingaphunziridwe pa chochitikacho. Kukhulupirika, kulimba mtima, kudzichepetsa, ndi kusadzikonda zimapereka zitsanzo zabwino zofunika kutsatidwa; machitachita achinyengo ngakhalenso zikhoterero zosafunika zili machenjezo aakulu kwa Akristu oti asiye machitachita oipa. Pamene nkhaniyi yatengedwa m’buku la “Kukambitsirana za m’Malemba” mutu wogaŵiridwawo ndiwo udzagwiritsidwa ntchito, ndipo wophunzirayo ayenera kuyesayesa kugwiritsa ntchito malemba moyenera. Mbale kapena mlongo angagaŵiridwe Nkhani Na. 4. Pamene ipatsidwa kwa mbale, nthaŵi zonse iyenera kukambidwa monga nkhani zina zonse. Pamene ipatsidwa kwa mlongo, iyenera kuperekedwa mofanana ndi Nkhani Na. 3. Komanso, nthaŵi zonse pamene mutu wa Nkhani Na. 4 watsogozedwa ndi chizindikiro ichi #, iyenera kukambidwa makamaka ndi mbale.

*NDANDANDA YOWONJEZERA YA KUŴERENGA BAIBULO: Imeneyo taiika m’mabulaketi, pambuyo pa nambala ya nyimbo ya mlungu uliwonse. Mwa kutsatira ndandanda imeneyi, mukumaŵerenga masamba ngati khumi pamlungu, mungaŵerenge Baibulo lonse m’zaka zitatu. Ndandanda ya kuŵerenga yowonjezera imeneyi siili maziko a nkhani za pologalamu ya sukulu kapena kubwereramo kolemba.

CHIDZIŴITSO: Za chidziŵitso china ndi malangizo onena za uphungu, kusunga nthaŵi, kubwereramo kolemba, ndi kukonzekera nkhani, onani patsamba 3 la Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996.

NDANDANDA

Jan. 3 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 4-6

Nyimbo Na. 9 [*Yeremiya 49-52]

Na. 1: Yamikirani Madalitso a Yehova (w98-CN 1/1 mas. 22-4)

Na. 2: Deuteronomo 6:4-19

Na. 3: Kutaya Mimba—N’chifukwa Chiyani Kuli Koletsedwa? (rs-CN mas. 210-12)

Na. 4: my-CN Nkhani 1-Mutu: # Mulungu Ayamba Kupanga Zinthu

Jan. 10 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 7-10

Nyimbo Na. 49 [*Maliro 1-5]

Na. 1: Tamandani Mulungu Woona (w98-CN 1/1 mas. 30-1)

Na. 2: Deuteronomo 8:1-18

Na. 3: Adamu ndi Hava, Anthu Enieni a M’mbiri? (rs-CN mas. 25-6)

Na. 4: my-CN Nkhani 2-Mutu: Munda Wokongola

Jan. 17 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 11-14

Nyimbo Na. 132 [*Ezekieli 1-9]

Na. 1: Chifukwa Chake Tiyenera Kukonzekeratu Tsogolo la Okondedwa? (w98-CN 1/15 mas. 19-22)

Na. 2: Deuteronomo 11:1-12

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kulambira Makolo kuli Kwachabe? (rs-CN mas. 188-9 ndime 6)

Na. 4: my-CN Nkhani 3-Mutu: Mwamuna ndi Mkazi Oyamba

Jan. 24 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 15-19

Nyimbo Na. 162 [*Ezekieli 10-16]

Na. 1: Mphamvu Yosanduliza ndi Kugwirizanitsa ya Choonadi (w98-CN 1/15 mas. 29-31)

Na. 2: Deuteronomo 19:11-21

Na. 3: Chifukwa Chake Kulambira Makolo Kumakhumudwitsa Yehova Mulungu (rs-CN mas. 189-90)

Na. 4: my-CN Nkhani 4-Mutu: # Chifukwa Chake Anataya Malo Awo

Jan. 31 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 20-23

Nyimbo Na. 13 [*Ezekieli 17-21]

Na. 1: Kaonedwe ka Malemba ka Chitamando ndi Kusyasyalika (w98-CN 2/1 mas. 29-31)

Na. 2: Deuteronomo 20:10-20

Na. 3: Kodi Okana Kristu N’ndani? (rs-CN mas. 414-5)

Na. 4: my-CN Nkhani 5-Mutu: Moyo Wovuta Uyamba

Feb. 7 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 24-27

Nyimbo Na. 222 [*Ezekieli 22-27]

Na. 1: Maziko a Chiyembekezo Choona cha Zinthu Zabwino (w98-CN 2/1 mas. 4-6)

Na. 2: Deuteronomo 25:5-16

Na. 3: Kuzindikira Ampatuko (rs-CN mas. 299-301)

Na. 4: my-CN Nkhani 6-Mutu: # Mwana Wabwino ndi Woipa

Feb. 14 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 28-30

Nyimbo Na. 180 [*Ezekieli 28-33]

Na. 1: Kulitsani Mzimu Woyamikira (w98-CN 2/15 mas. 4-7)

Na. 2: Deuteronomo 28:1-14

Na. 3: Kodi Maganizo Athu pa Ampatuko Ayenera Kukhala Otani? (rs-CN mas. 301-2)

Na. 4: my-CN Nkhani 7-Mutu: # Munthu Wolimba Mtima

Feb. 21 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 31-34

Nyimbo Na. 46 [*Ezekieli 34-39]

Na. 1: sg-CN mas. 29-31 ndime 1-7

Na. 2: Deuteronomo 32:35-43

Na. 3: Kristu Sanamange Tchalitchi pa Petro (rs-CN mas. 196-8, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 8-Mutu: Zimphona Padziko

Feb. 28 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 1-5

Nyimbo Na. 40 [*Ezekieli 40-45]

Na. 1: sg-CN mas. 31-3 ndime 8-15

Na. 2: Yoswa 2:8-16

Na. 3: Kodi N’chiyani Chimene Chinali Mfungulo Yogwiritsidwa Ntchito ndi Petro? (rs-CN mas. 198-9)

Na. 4: my-CN Nkhani 9-Mutu: Nowa Akhoma Chingalawa

Mar. 6 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 6-9

Nyimbo Na. 164 [*Ezekieli 46-Danieli 2]

Na. 1: Makolo Tetezerani Ana Anu! (w98-CN 2/15 mas. 8-11)

Na. 2: Yoswa 7:1, 10-19

Na. 3: “Oloŵa Mmalo a Atumwi” Si Akristu Enieni (rs-CN mas. 200-3)

Na. 4: my-CN Nkhani 10-Mutu: # Chigumula Chachikulu

Mar. 13 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 10-13

Nyimbo Na. 138 [*Danieli 3-7]

Na. 1: Chimene Baibulo Limanena pa za Chikoka (w98-CN 2/15 mas. 23-7)

Na. 2: Yoswa 11:6-15

Na. 3: Kodi Armagedo Idzamenyedwera Kuti? (rs-CN mas. 37-9, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 11-Mutu: # Utawaleza Woyamba

Mar. 20 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 14-17

Nyimbo Na. 10 [*Danieli 8-Hoseya 2]

Na.1: Amuna Okhulupirika “Akumva Zomwezi Tizimva Ife” (w98-CN 3/1 mas. 26-9)

Na. 2: Yoswa 15:1-12

Na. 3: Kodi Ndani Ndiponso N’chiyani Chimene Chidzawonongedwa pa Armagedo? (rs-CN mas. 39-40, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 12-Mutu: Anthu Amanga Chinsanja

Mar. 27 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 18-20

Nyimbo Na. 105 [*Hoseya 3-14]

Na. 1: Kukumbukira Masiku Omaliza a Yesu Padziko (w98-CN 3/15 mas. 3-9)

Na. 2: Yoswa 18:1-10

Na. 3: Kodi Ndani Adzapulumuka Armagedo? (rs-CN tsa. 40)

Na. 4: my-CN Nkhani 13-Mutu: Abrahamu—Bwenzi la Mulungu

Apr. 3 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 21-24

Nyimbo Na. 144 [*Yoweli 1-Amosi 7]

Na. 1: sg-CN mas. 33-5 ndime 1-9

Na. 2: Yoswa 21:43–22:8

Na. 3: Armagedo—Si Kuswedwa kwa Chikondi cha Mulungu (rs-CN tsa. 41, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 14-Mutu: # Mulungu Ayesa Abrahamu

Apr. 10 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 1-4

Nyimbo Na. 43 [*Amosi 8-Mika 5]

Na. 1: sg-CN mas. 36-8 ndime 10-17

Na. 2: Oweruza 3:1-11

Na. 3: N’kosatheka Kukhala M’mkhalidwe Wauchete pa Armagedo (rs-CN tsa. 41, kamutu kachiŵiri)

Na. 4: my-CN Nkhani 15-Mutu: Mkazi wa Loti Anacheuka

Apr. 17 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 5-7

Nyimbo Na. 193 [*Mika 6-Zefaniya 1]

Na. 1: Phunziranipo pa Malangizo a Yesu kwa 70 Aja (w98-CN 3/1 mas. 30-1)

Na. 2: Oweruza 5:24-31

Na. 3: Kodi N’chisonkhezero Chayani Chimene Chikukankhira Amitundu ku Nkhondo ya Armagedo? (rs-CN mas. 41-2)

Na. 4: my-CN Nkhani 16-Mutu: Isake Apeza Mkazi Wabwino

Apr. 24 Kubwereramo Kolemba. Malizani Deuteronomo 4-Oweruza 7

Nyimbo Na. 91 [*Zefaniya 2-Zekariya 7]

May 1 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 8-10

Nyimbo Na. 38 [*Zekariya 8-Malaki 4]

Na. 1: Lemekezani Anthu Ena (w98-CN 4/1 mas. 28-31)

Na. 2: Oweruza 9:7-21

Na. 3: Kuzindikira Babulo wa m’Chivumbulutso (rs-CN 47-8)

Na. 4: my-CN Nkhani 17-Mutu: Amapasa Amene Anali Osiyana

May 8 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 11-14

Nyimbo Na. 82 [*Mateyu 1-8]

Na. 1: Barnaba, “Mwana wa Chitonthozo” (w98-CN 4/15 mas. 20-3)

Na. 2: Oweruza 13:2-10, 24

Na. 3: Kodi Babulo Wakale Anadziŵika ndi Chiyani? (rs-CN mas. 48-9)

Na. 4: my-CN Nkhani 18-Mutu: # Yakobo Amka ku Harana

May 15 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 15-18

Nyimbo Na. 26 [*Mateyu 9-14]

Na. 1: Chisungiko Padziko Lonse Kopanda Magulu Ankhondo (w98-CN 4/15 mas. 28-30)

Na. 2: Oweruza 17:1-13

Na. 3: Chifukwa Chake Zipembedzo Zodzinenera Kukhala Zachikristu Zili Mbali ya Babulo Wamkulu (rs-CN tsa. 51, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 19-Mutu: Yakobo Ali ndi Banja Lalikulu

May 22 Kuŵerenga Baibulo: Oweruza 19-21

Nyimbo Na. 42 [*Mateyu 15-21]

Na. 1: sg-CN mas. 39-41 ndime 1-11

Na. 2: Oweruza 19:11-21

Na. 3: Chifukwa Chake Kuli Kofunika Kutuluka m’Babulo Wamkulu (rs-CN tsa. 51)

Na. 4: my-CN Nkhani 20-Mutu: Dina Aloŵa M’vuto

May 29 Kuŵerenga Baibulo: Rute 1-4

Nyimbo Na. 120 [*Mateyu 22-26]

Na. 1: sg-CN mas. 41-3 ndime 12-18

Na. 2: Rute 3:1-13

Na. 3: Chimene Ubatizo Uli ndi Chifukwa Chake Okhulupirira Amabatizidwa (rs-CN tsa. 364, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 21-Mutu: Abale a Yosefe Amuda

June 5 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 1-3

Nyimbo Na. 191 [*Mateyu 27-Marko 4]

Na. 1: sg-CN mas. 44-6 ndime 1-8

Na. 2: 1 Samueli 1:9-20

Na. 3: Ubatizo Wachikristu—Osati mwa Kuwaza Madzi, Osati wa Makanda (rs-CN mas. 364-5)

Na. 4: my-CN Nkhani 22-Mutu: Yosefe Aikidwa M’ndende

June 12 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 4-7

Nyimbo Na. 85 [*Marko 5-9]

Na. 1: Kodi Yehova Ndani? (w98-CN 5/1 mas. 5-7)

Na. 2: 1 Samueli 4:9-18

Na. 3: Ubatizo Wam’madzi Sukhululukira Machimo (rs-CN tsa. 365)

Na. 4: my-CN Nkhani 23-Mutu: Maloto a Farao

June 19 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 8-11

Nyimbo Na. 160 [*Marko 10-14]

Na. 1: Kukhulupirika Kufupidwa (w98-CN 5/1 mas. 30-1)

Na. 2: 1 Samueli 8:4-20

Na. 3: Kodi Ndani Amene Amabatizidwa ndi Mzimu Woyera? (rs-CN tsa. 366, kamutu koyamba)

Na. 4: my-CN Nkhani 24-Mutu: Yosefe Ayesa Abale Ake

June 26 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 12-14

Nyimbo Na. 172 [*Marko 15-Luka 3]

Na. 1: Kodi Chuma Chingakupatseni Chimwemwe? (w98-CN 5/15 mas. 4-6)

Na. 2: 1 Samueli 14:1-14

Na. 3: Ubatizo wa Moto Wosiyana ndi Ubatizo wa Mzimu Woyera (rs-CN mas. 367-8)

Na. 4: my-CN Nkhani 25-Mutu: Banja Lisamukira ku Igupto

July 3 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 15-17

Nyimbo Na. 8 [*Luka 4-8]

Na. 1: Yunike ndi Loisi—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo Chabwino (w98-CN 5/15 mas. 7-9)

Na. 2: 1 Samueli 16:4-13

Na. 3: Zifukwa Zophunzirira Baibulo (rs-CN mas. 52-53)

Na. 4: my-CN Nkhani 26-Mutu: # Yobu Akhulupirira Mulungu

July 10 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 18-20

Nyimbo Na. 156 [*Luka 9-12]

Na.1: Fikani Pamtima ndi Luso la Kukopa (w98-CN 5/15 mas. 21-3)

Na. 2: 1 Samueli 19:1-13

Na. 3: Umboni wa M’buku la Yesaya Wakuti Baibulo ndi Louziridwa (rs-CN mas. 54-5)

Na. 4: my-CN Nkhani 27-Mutu: Mfumu Yoipa Ilamulira Igupto

July 17 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 21-24

Nyimbo Na. 33 [*Luka 13-19]

Na. 1: Kwaniritsani Udindo Wanu Wosamalira Banja (w98-CN 6/1 mas. 20-3)

Na. 2: 1 Samueli 24:2-15

Na. 3: Kukwaniritsidwa kwa Maulosi Onena Za Yesu Kumatsimikizira Kuuziridwa kwa Baibulo (rs-CN mas. 55-6)

Na. 4: my-CN Nkhani 28-Mutu: Mmene Mose Anapulumutsidwira

July 24 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 25-27

Nyimbo Na. 60 [*Luka 20-24]

Na. 1: Chilungamo Chenicheni—Liti Ndipo Motani? (w98-CN 6/15 mas. 26-9)

Na. 2: 1 Samueli 25:23-33

Na. 3: Baibulo Limagwirizana ndi Sayansi (rs-CN mas. 56-7)

Na. 4: my-CN Nkhani 29-Mutu: Chifukwa Chake Mose Akuthawa

July 31 Kuŵerenga Baibulo: 1 Samueli 28-31

Nyimbo Na. 170 [*Yohane 1-6]

Na. 1: sg-CN mas. 46-9 ndime 9-20

Na. 2: 1 Samueli 31:1-13

Na. 3: Kuyankha Zitsutso za Kukhulupirira Baibulo (rs-CN mas. 58-59)

Na. 4: my-CN Nkhani 30-Mutu: # Chitsamba Choyaka Moto

Aug. 7 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 1-4

Nyimbo Na. 22 [*Yohane 7-11]

Na. 1: sg-CN mas. 49-51 ndime 1-8

Na. 2: 2 Samueli 2:1-11

Na. 3: Baibulo ndi Lopindulitsa M’tsiku Lathu (rs-CN tsa. 60)

Na. 4: my-CN Nkhani 31-Mutu: Mose ndi Aroni Aona Farao

Aug. 14 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 5-8

Nyimbo Na. 174 [*Yohane 12-18]

Na. 1: “Yesetsani” (w98-CN 6/15 mas. 30-1)

Na. 2: 2 Samueli 7:4-16

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Sasangalalira Tsiku Lakubadwa (rs-CN mas. 361-2)

Na. 4: my-CN Nkhani 32-Mutu: # Miriri 10

Aug. 21 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 9-12

Nyimbo Na. 107 [*Yohane 19-Machitidwe 4]

Na. 1: Khalani Mnansi Wabwino (w98-CN 7/1 mas. 30-1)

Na. 2: 2 Samueli 11:2-15

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Amasala Mwazi? (rs-CN tsa. 313)

Na. 4: my-CN Nkhani 33-Mutu: # Kuoloka Nyanja Yofiira

Aug. 28 Kubwereramo Kolemba. Malizani Oweruza 8-2 Samueli 12

Nyimbo Na. 177 [*Machitidwe 5-10]

Sept. 4 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 13-15

Nyimbo Na. 183 [*Machitidwe 11-16]

Na. 1: Thandizani Ana Anu Kukhala ndi Chiyambi Chabwino M’moyo (w98-CN 7/15 mas. 4-6)

Na. 2: 2 Samueli 13:20-33

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Amakana Kupoperedwa Mwazi? (rs-CN mas. 315-6)

Na. 4: my-CN Nkhani 34-Mutu: Mtundu Watsopano wa Chakudya

Sept. 11 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 16-18

Nyimbo Na. 129 [*Machitidwe 17-22]

Na. 1: Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro (w98-CN 7/15 mas. 20-4)

Na. 2: 2 Samueli 16:5-14

Na. 3: Kuyankha Chitsutso pa Kaonedwe ka Baibulo ka Mwazi (rs-CN mas. 317-9)

Na. 4: my-CN Nkhani 35-Mutu: # Yehova Apereka Malamulo Ake

Sept. 18 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 19-21

Nyimbo Na. 19 [*Machitidwe 23-Aroma 1]

Na. 1: Kodi Chikumbumtima Chanu Mungachikhulupirire? (w98-CN 9/1 mas. 4-7)

Na. 2: 2 Samueli 20:1, 2, 14-22

Na. 3: Kodi “Kubadwanso Mwatsopano” Kumatanthauza Chiyani? (rs-CN mas. 157-8)

Na. 4: my-CN Nkhani 36-Mutu: Mwana wa Ng’ombe wa Golidi

Sept. 25 Kuŵerenga Baibulo: 2 Samueli 22-24

Nyimbo Na. 98 [*Aroma 2-9]

Na. 1: sg-CN mas. 51-4 ndime 9-18

Na. 2: 2 Samueli 23:8-17

Na. 3: Chipulumutso Sichidalira pa “Kubadwanso Mwatsopano” (rs-CN tsa. 159)

Na. 4: my-CN Nkhani 37-Mutu: # Chihema Cholambirira

Oct. 2 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 1-2

Nyimbo Na. 36 [*Aroma 10-1 Akorinto 3]

Na. 1: sg-CN mas. 54-6 ndime 1-8

Na. 2: 1 Mafumu 2:1-11

Na. 3: “Kubadwanso Mwatsopano”—Kukonza Malingaliro Olakwika (rs-CN mas. 160-1)

Na. 4: my-CN Nkhani 38-Mutu: Azondi 12

Oct. 9 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 3-6

Nyimbo Na. 106 [*1 Akorinto 4-13]

Na. 1: Ikani Zinthu Zofunika Pamalo Oyamba (w98-CN 9/1 mas. 19-21)

Na. 2: 1 Mafumu 4:21-34

Na. 3: Kuululira kwa Ansembe: N’chifukwa Chiyani Sikuli kwa m’Malemba? (rs-CN mas. 218-9)

Na. 4: Kuulula Machimo a kwa Mulungu ndi a kwa Munthu (rs-CN mas. 220-1, kamutu kachiŵiri tsa. 220, ndi koyamba tsa. 221)

Oct. 16 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 7-8

Nyimbo Na. 76 [*1 Akorinto 14-2 Akorinto 7]

Na. 1: Kuchitira Umboni Pamaso pa Zinduna (w98-CN 9/1 mas. 30-1)

Na. 2: 1 Mafumu 7:1-14

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Machimo Aakulu Ayenera Kuululidwa kwa Akulu? (rs-CN mas. 221-2)

Na. 4: # N’chifukwa Chiyani Kuli Kwanzeru Kukhulupirira Chilengedwe? (rs-CN mas. 74-6)

Oct. 23 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 9-11

Nyimbo Na. 97 [*2 Akorinto 8-Agalatiya 4]

Na. 1: Kaonedwe Kachikristu ka Malowolo (w98-CN 9/15 mas. 24-7)

Na. 2: 1 Mafumu 11:1-13

Na. 3: Kumvetsetsa Cholembedwa cha Baibulo Ponena za Chilengedwe (rs-CN mas. 76-8)

Na. 4: N’chifukwa Chiyani Kulambira Mtanda Sikugwirizana ndi Malemba? (rs-CN mas. 305-6, ndime 3)

Oct. 30 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 12-14

Nyimbo Na. 113 [*Agalatiya 5-Afilipi 2]

Na. 1: Kodi Mulungu Ali Weniweni Kwa Inu? (w98-CN 9/15 mas. 21-3)

Na. 2: 1 Mafumu 13:1-10

Na. 3: N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa? (rs-CN mas. 151-2, kamutu koyamba)

Na. 4: Kodi Akufa Ali Kuti Ndipo Kodi Mkhalidwe Wawo ndi Wotani? (rs-CN mas. 152-3)

Nov. 6 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 15-17

Nyimbo Na. 123 [*Afilipi 3-1 Atesalonika 5]

Na. 1: Pitanibe Patsogolo Mwauzimu! (w98-CN 10/1 mas. 28-31)

Na. 2: 1 Mafumu 15:9-24

Na. 3: Kodi N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizichita Nawo Miyambo ya Makolo ya Maliro? (rs-CN mas. 155-6)

Na. 4: Kutsutsa Malingaliro Olakwika Ponena za Imfa (rs-CN mas.156-7)

Nov. 13 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 18-20

Nyimbo Na. 159 [*2 Atesalonika 1-2 Timoteo 3]

Na. 1: Thetsani Mavuto Mwamtendere (w98-CN 11/1 mas. 4-7)

Na. 2: 1 Mafumu 20:1, 13-22

Na. 3: Maloto: Ouziridwa ndi Osauziridwa (rs-CN mas. 246-7)

Na. 4: Mankhwala Osokoneza Bongo: Pamene Aletsedwa kwa Akristu (rs-CN mas. 248-9)

Nov. 20 Kuŵerenga Baibulo: 1 Mafumu 21-22

Nyimbo Na. 179 [*2 Timoteo 4-Ahebri 7]

Na. 1: sg-CN mas. 56-8 ndime 9-16

Na. 2: 1 Mafumu 22:29-40

Na. 3: Chifukwa Chake Akristu Amapeŵa Chamba (rs-CN mas. 250-1, kamutu koyamba)

Na. 4: # N’chifukwa Chiyani Akristu Amapeŵa Fodya? (rs-CN mas. 251-3, kamutu kachiŵiri)

Nov. 27 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 1-3

Nyimbo Na. 148 [*Ahebri 8-Yakobo 2]

Na. 1: sg-CN mas. 58-61 ndime 1-12

Na. 2: 2 Mafumu 2:15-25

Na. 3: Maboma Sadzalepheretsa Chifuno cha Mulungu Chokhudza Dziko Lapansi (rs-CN mas. 131-2)

Na. 4: Kodi Yehova Adzawononga Dziko Lapansi ndi Moto? (rs-CN mas. 132-4)

Dec. 4 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 4-6

Nyimbo Na. 109 [*Yakobo 3-2 Petro 3]

Na. 1: Chenjerani ndi Chisimoni (w98-CN 11/15 tsa. 28)

Na. 2: 2 Mafumu 5:20-27

Na. 3: Ziwalo za Yerusalemu Watsopano Sizidzabwereranso Padziko Lapansi Oipa Atawonongedwa (rs-CN tsa. 134)

Na. 4: Kodi Chifuno cha Mulungu Choyambirira Kaamba ka Dziko Lapansi Chinasintha? (rs-CN tsa. 135)

Dec. 11 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 7-9

Nyimbo Na. 117 [*1 Yohane 1-Chivumbulutso 1]

Na. 1: Malamulo a Baibulo Ofunika Kutsatidwa Pokongoza Kapena Kukongola Ndalama (w98-CN 11/15 mas. 24-7)

Na. 2: 2 Mafumu 7:1, 2, 6, 7, 16-20

Na. 3: Kodi Tingalimbikitse Motani Anthu Odwala? (rs-CN tsa. 79)

Na. 4: Mmene Tingalimbikitsire Anthu Oferedwa? (rs-CN tsa. 80)

Dec. 18 Kuŵerenga Baibulo: 2 Mafumu 10-12

Nyimbo Na. 181 [*Chivumbulutso 2-12]

Na. 1: Nkhani Yake Yeniyeni Yonena za Kubadwa Kwa Yesu (w98-CN 12/15 mas. 5-9)

Na. 2: 2 Mafumu 11:1-3, 9-16

Na. 3: Chilimbikitso kwa Ozunzidwa Chifukwa cha Kuchita Chifuniro cha Mulungu (rs-CN mas. 80-1)

Na. 4: # Kodi Mungalimbikitse Motani Otaya Mtima Chifukwa cha Chisalungamo? (rs-CN tsa. 81)

Dec. 25 Kubwereramo Kolemba. Malizani 2 Samueli 13-2 Mafumu 12

Nyimbo Na. 217 [*Chivumbulutso 13-22]

S-38-CN Mal, Moz & Zam 10/99

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena