Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 1/1 tsamba 22-24
  • Kodi Mumayamikiradi Madalitso a Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayamikiradi Madalitso a Yehova?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wopatsa Woposa Onse
  • Madalitso Amene Amatilemeretsa
  • Kuyembekezera Yehova Moleza Mtima
  • Funani Madalitso Ake
  • ‘Kubzala ndi Misozi ndi Kututa ndi Mfuu Yachikondwerero’
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Madalitso a Yehova Amatilemeretsa
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Ubwino Woyenda Mwangwiro
    Nsanja ya Olonda—2006
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 1/1 tsamba 22-24

Kodi Mumayamikiradi Madalitso a Yehova?

KENICHI, mwamuna wina wa zaka zapakati, analoŵa m’sitolo yamankhwala nkugula mankhwala a chifuŵa. Atamwa mankhwalawo, thupi lake silinagwirizane nawo, ndiye linayamba kuyabwa ndipo thupi lonse linatuluka matuza a madzi. Nzosadabwitsa kuti Kenichi anayamba kukayikira kuti mwina wogulitsa mankhwalayo sanamvetsetse bwino zimene iyeyo anali kufuna.

Ena angamaganize za Yehova Mulungu mofanana ndi mmene Kenichi anaonera wogulitsa mankhwala uja. Amakayikira kuti Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, amatikondadi aliyense payekha. Ngakhale amazindikira kuti Mulungu ngwabwino, iwo samakhulupirira kuti amatisamala aliyense payekha. Amaganiza zimenezo makamaka pamene zinthu sizikuwayendera bwino kapena pamene kumvera kwawo mapulinsipulo a Baibulo kwawapangitsa kukumana ndi mavuto aakulu. Chifukwa chosazindikira, amaona mavuto awowo monga kuyabwa kwa thupi ndi matuza amene anatuluka pathupi la Kenichi mosayembekezera, ngati kuti mwa njira ina umenewo uli mlandu wa Mulungu.​—Miyambo 19:3.

Sitingayerekezere Yehova ndi anthu opanda ungwiro. Maluso ndi nzeru za anthu nzochepa. Amalephera kuzindikira zimene ena amasoŵadi, monga uja anagulitsa Kenichi mankhwala. Koma si choncho ndi Yehova, palibe chimene samaona. Nthaŵi zonse Yehova amatithandiza koma sitimazindikira zinthuzo kapena kuziyamikira, chifukwa timakonda kudandaula ndi zimene tilibe koma nkumanyalanyaza madalitso omwe tili nawo. M’malo mofulumira kuimba mlandu Yehova pa mavuto alionse amene timakumana nawo, tiyeni tiziyesa kuzindikira madalitso ochokera kwa Yehova omwe tili nawo.

Malinga ndi Webster’s Ninth New Collegiate Dictionary, “dalitso” lingafotokozedwe kuti “chinthu chosangalatsa, kapena chopatsa mtendere.” Kodi mumazindikira kuti ndi mmenedi madalitso a Yehova alili?

Wopatsa Woposa Onse

Pamene mkazi amati mwamuna wake ngwodziŵa kupatsa, amatanthauza kuti iye amapatsa apabanja lakewo zosoŵa zawo mokwanira, kuwapatsa chakudya chokwanira, malo ogona, ndi zovala kuti banjalo lizisangalala ndi kukhala pamtendere. Nanga Yehova ngwopambana motani monga Wopatsa zinthu? Taliyang’anani bwino pulaneti lathuli, Dziko Lapansi, mudzi wa anthu. Linalenjekedwa kutali ndi dzuŵa pamtunda wa makilomita 150,000,000, wangokhala mtunda woyenera wopangitsa kutentha ndi kuzizira koyenera kochititsa kuti dziko lapansi likhale ndi zamoyo. Kupendeka kwa dziko lathuli pamadigirii 23.5 anakulinganiza bwino kwambiri. Iko kumapangitsa nyengo zosiyanasiyana zimene zimapangitsa anthu kututa zakudya zambiri. Chifukwa cha zimenezo, dziko lapansi limadyetsa anthu oposa mabiliyoni asanu. Ndithudi Yehova alidi Wopatsa wabwino kwambiri!

Ndiponso, Baibulo limatitsimikiza kuti Yehova amatisamala zedi aliyense payekha ndipo amatifunira mtendere. Tangoganizani, pa nyenyezi zonse zofika m’mabiliyoni, Yehova amadziŵa iliyonse ndi dzina lake, ndipo palibe ngakhale mpheta imodzi yomwe ingagwe pansi iye osadziŵa. (Yesaya 40:26; Mateyu 10:29-31) Ndiye kuti ayenera kusamala kwambiri anthu amene amamkonda ndiponso amene anawagula ndi mwazi wamtengo wapatali wa Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu! (Machitidwe 20:28) Munthu wanzeru uja ananena zoona pamene anati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”​—Miyambo 10:22.

Madalitso Amene Amatilemeretsa

Tili ndi kanthu kena kamtengo wapatali zedi kamene tiyenera kukayamikira kwenikweni. Kameneko ndiye kati? Baibulo limakatchula pamene limati: “Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golidi ndi siliva zikwi zikwi.” (Salmo 119:72; Miyambo 8:10) Golidi wabwino kwambiri angakhale wamtengo wapamwamba, koma chilamulo cha Yehova nchokoma kuposapo. Kudziŵa molongosoka chilamulo chake limodzi ndi nzeru ndi kuzindikira zimene Yehova amapatsa anthu ofunafuna choonadi moona mtima, tiyenera kuziona kukhala zinthu zamtengo wapatali. Zimatithandiza kudzitetezera, kupirira m’mikhalidwe yovuta, kukhoza kuthetsa mavuto, ndiyeno nkukhala okhutira ndi achimwemwe.

Zimenezi nzoona ngakhale kwa ana aang’ono. Talingalirani mmene mtsikana wamng’ono anathetsera mavuto ake mwa kumvera chilamulo cha Yehova. Mtsikanayo, Akemi, amakhala cha ku Tokyo. Atate wake ndi amayi ake anagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo pomphunzitsa, ndipo mwa mawu ndi zitsanzo iwo anathandiza mwana wawo wamkaziyo kuphunzira kukonda Yehova ndi mnansi wake. Pokhala ataoneratu mavuto omwe ati adzakumane nawo kusukulu, iwo anayesa kumkonzekeretsa mwa njira yabwino kwambiri. Komabe, pamene Akemi anayamba sukulu yapulaimale, anzake a m’kalasi ankamuona ngati “wosiyana” chifukwa ankapemphera asanayambe kudya chakudya ndipo momvera chikumbumtima chake ankapeŵa zinthu zotsutsidwa m’malemba. Pambuyo pakanthaŵi anadzakhala choseŵeretsa cha kagulu ka ovutitsa anzawo omwe anali kumtsekereza panjira ataŵeruka kusukulu ndi kumuomba makofu, kumpotokola mikono yake, ndi kumamnyodola.

Kamwanako, ka Akemi, sikanali kubwezera, kapena kuwaopa omzunzawo. M’malo mwake, anayesa kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira. Chifukwa cha khalidwe lake labwino ndi kulimba mtima, anzake ambiri apasukulu anayamba kumlemekeza. Anzakewo anafotokozera mphunzitsi wawo za nkhaniyo, ndipo kuyambira tsiku limenelo, Akemi sanavutitsidwenso kusukulu.

Kodi nchiyani chinamthandiza Akemi kupirira mkhalidwe wovuta umenewo? Chidziŵitso cholongosoka, kuzindikira, ndi nzeru yochokera kwa Yehova imene makolo ake anamphunzitsa. Anadziŵa bwino za kupirira kwa Yesu, ndipo chimenecho chinamthandiza kutsatira chitsanzo chake. Baibulo linamthandiza kuzindikira kuti anthu ena amachita zoipa chifukwa chosadziŵa, ndipo linamlimbikitsa kumada zoipa zimene anthu omvutawo ankachita koma osada anthuwo iyayi.​—Luka 23:34; Aroma 12:9, 17-21.

Nzoonadi, palibe makolo omwe angakonde kuona mwana wawo akunyodoledwa ndi kuchitidwa nkhanza. Komabe, tangoyerekezerani mmene makolo a Akemi anasangalalira pamene anamva zonse zimene zinachitika! Ana oterowo ndithudi ali dalitso lochokera kwa Yehova.​—Salmo 127:3; 1 Petro 1:6, 7.

Kuyembekezera Yehova Moleza Mtima

Komabe, musanalandire madalitso a Yehova, nthaŵi zina muyenera kuyembekezera nthaŵi yake. Yehova amadziŵa za inu ndipo amakupatsani chosoŵa chilichonse pamene chingakupindulitseni kwambiri. (Salmo 145:16; Mlaliki 3:1; Yakobo 1:17) Mwina mumakonda zipatso, koma mungamuone bwanji munthu amene mwamchezera amene wakupatsani chipatso chimene sichinafike poti nkudyedwa? Kaya likhale apulo, lalanje, kapena kenakake, mungakonde kuti chipatsocho chikhale chakucha, chili chozuna. Mofananamo, Yehova amakupatsani zimene mumasoŵa panthaŵi yoyenera​—osati mwamsanga ndipo osati mochedwetsa.

Kumbukirani chokumana nacho cha Yosefe. Anaponyedwa m’ndende ku Igupto, osati chifukwa choti anachimwa iyayi. Mkaidi mnzake, woperekera chikho Farao, ankayembekezera kumasulidwa ndipo analonjeza kuti akauza Farao za Yosefe. Koma atamasulidwa anangoiŵaliratu za Yosefe. Kunaoneka ngati kuti Yosefe anatayidwa. Komabe, patatha zaka ziŵiri zathunthu, anadzamasulidwa m’ndende ndipo potsirizira pake anaikidwa kukhala wolamulira wachiŵiri mu Igupto. M’malo motaya mtima, Yosefe anayembekezera Yehova. Chifukwa cha zimenezo, anadalitsidwa mwa kumgwiritsira ntchito kupulumutsa miyoyo ya Aisrayeli ndi Aigupto omwe.​—Genesis 39:1–41:57.

Masashi anali mkulu mumpingo kumpoto kwa Japan. Iyeyo sanali m’ndende, koma anafunikira kuyembekezera Yehova. Chifukwa? Kuyambira pamene Sukulu Yophunzitsa Utumiki, sukulu yophunzitsa atumiki achikristu oyeneretsedwa, inayamba ku Japan, iyeyo anakhumba kwambiri kuloŵa sukuluyo. Anapemphera ndi mtima wonse kuti alandire mwaŵi umenewo. Mpainiya mnzake anaitanidwa, koma Masashi, ngakhale kuti anali wofunitsitsa, sanaitanidwe. Anakhumudwa kwabasi.

Komabe, anachitapo kanthu kuti alamulire maganizo ake. Anaphunzira Baibulo ndi mabuku ofalitsidwa ndi Watch Tower Society, onena za nkhani zonga kudzichepetsa ndi kulamulira maganizo ako. Anayamba kuganiza bwino ndipo anakhala wokhutira pautumiki wake. Kenako, anaitanidwa kukaloŵa sukuluyo panthaŵi yomwe sanali kuyembekezera.

Pokhala atakulitsa mikhalidwe yonga kuleza mtima ndi kudzichepetsa, anapindula nayo sukuluyo. Pambuyo pake, Masashi anapatsidwa ntchito yotumikira abale ake monga woyang’anira woyendayenda. Inde, Yehova anadziŵa zimene Masashi anasoŵa ndipo anampatsa zimenezo ndendende pamene zikanampindulitsa kwambiri.

Funani Madalitso Ake

Choncho, Yehova sali ngati wogulitsa mankhwala uja. Ngakhale kuti tingalephere kuzindikira kuti Yehova amatisamala ndipo amatidera nkhaŵa, amatisonyeza chifundo chake mwa njira zosiyanasiyana​—panthaŵi yabwino ndi mwa njira imene chifundocho chimatipindulitsa kwambiri. Choncho funafunanibe madalitso ake. Kumbukirani kuti muli kale ndi zinthu zambiri zoyenera kuyamikira. Mwadalitsidwa ndi zinthu zofunika kuti mupitirize kukhala moyo padziko lapansi. Mwapatsidwa chidziŵitso chonena za Yehova ndi chonena za njira zake zangwiro. Mwapatsidwa kuzindikira. Ndipo mwapeza kuzindikira. Zonsezo zimakupatsani mtendere ndi chimwemwe.

Kuti muone madalitso ena ambiri a Yehova, ziphunziranibe Baibulo nthaŵi zonse. Mpempheni Yehova kukuthandizani kumvetsetsa ndi kugwiritsira ntchito ziphunzitso zonga ngale zopezeka m’Mawu ake ouziridwa. Zidzakulemeretsanidi, kotero kuti simudzasoŵa kanthu. Inde, zimenezo zidzakupangitsani kukhala wachimwemwe ndi wokhutira tsopano lino ndiponso kukhala ndi moyo wabwino kwambiri m’dziko latsopano likudzalo.​—Yohane 10:10; 1 Timoteo 4:8, 9.

[Chithunzi patsamba 23]

Madalitso a Yehova ngamtengo wapamwamba kuposa golidi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena