Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my nkhani 10
  • Chigumula Chachikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chigumula Chachikulu
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Madzi Alisesa Dziko
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Anthu 8 Anapulumuka
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nowa Akhoma Chingalawa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Chingalawa cha Nowa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my nkhani 10

NKHANI 10

Chigumula Chachikulu

KUNJA kwa chingalawa, anthu anachitabe zochita zao monga kale. Iwo sanakhulupirirebe kuti Chigumula chikadza. Iwo angakhale ataseka koposa kale. Koma posapita nthawi analeka kuseka.

Mwadzidzidzi mvula inayamba kubvumba. Inakhuthuka kumwamba monga m’mene mumakhuthulira madzi m’ndowa. Nowa anali atanena zoona! Koma kunali kochedwa tsopano kwa ali yense kulowa m’chingalawa. Khomo linali litatsekedwa zolimba ndi Yehova.

Posapita nthawi madambo onse anamizidwa, Madzi anakhala ngati mitsinje yaikulu. Anakhwekhweretsa mitengo nagubuduza zimiyala, ndi kupanga phokoso lalikulu. Anthu anaopa. Anakwera m’zitunda. O, analaka-lakatu ngati akanamvetsera Nowa ndi kulowa m’chingalawa pamene khomo linali lowatsegukira! Koma tsopano kunali kochedwa.

Madzi anali kumakwera-kwera. Kwa mausana 40 ndi mausiku 40 madzi anakhuthuka kumwamba. Anakwera m’mbali mwa mapiri, ndipo posakhalitsa mapiri atali koposa anamizidwa. Chotero monga momwe ananenera Mulungu, anthu ndi zinyama zomwe kunja kwa chingalawa anafa. Koma ali yense m’kati anali bwino lomwe.

Nowa ndi ana ake anachita ntchito yabwino kukhoma chingalawa. Madzi anachinyamula, ndipo chinayandama pamwamba pa madzi. Tsiku lina, italeka mvula’yo, dzuwa linayamba kuwala. Ha, ndi kaonekedwe kokongola chotani! Panali chinyanja chimodzi konse-konse. Chokha chimene chikanatha kuonedwa chinali chingalawa choyandama’cho.

Zimphona zija zinali zitapita tsopano. Sizinapezeke’nso kuti zibvulaze anthu. Zonse zinali zitafa, limodzi ndi amai ao ndi anthu ena onse oipa. Koma kodi n’chiani chinachitikira atate ao?

Atate a zimphona’zo sanali anthu kweni-kweni ngati ife. Iwo anali angelo amene anadza kudzakhala ngati anthu pa dziko. Tsono chitadza Chigumula, sanafere kumodzi ndi anthu ena onse. Iwo sanagwiritsire’nso ntchito mafupi aumunthu amene anapanga’wo, nabwerera kumwamba monga angelo. Koma sanaloledwe’nso kukhala mbali ya banja la angelo a Mulungu. Chotero anakhala angelo a Satana. M’Baibulo akuchedwa ziwanda.

Tsopano Mulungu anachititsa mphepo kuomba, ndipo madzi’wo anayamba kuphwa. Pambuyo pa miyezi isanu chingalawa’cho chinatera pa phiri. Masiku ena ambiri anapitapo, okhala m’katimo ankatha kuyang’ana panja ndi kuona nsonga za mapiri. Madziwo anali kutsika-tsika.

Kenako Nowa anatulutsa khungubwi m’chingalawa. Ankauluka kwa kanthawi kumka cha uko n’kubwerera’nso, chifukwa cha kusapeza malo abwino oterapo. Anatero nthawi zonse ndipo pobwerera pali ponse, ankakhala pa chingalawa.

Nowa anafuna kudziwa ngati madzi anali ataphwa pa dziko, chotero kenako anatulutsa nkhunda. Koma nkhunda’yo inabwerera’nso chifukwa sinapeze malo okhala. Nowa anaitumiza kachiwiri, ndipo inadza ndi tsamba la mtengo wa azitona kukamwa. Chotero Nowa anadziwa kuti madzi anali ataphwa. Nowa anatumiza nkhunda kachitatu, potsiriza inapeza malo ouma okhala.

Mulungu tsopano analankhula ndi Nowa. Anati: ‘Tuluka m’chingalawa. Tuluka nalo banja lako lonse ndi zinyama.’ Iwo anali atakhala m’chingalawa’cho koposa chaka chimodzi. Chotero tingayerekezere m’mene analiri achimwemwe kutuluka ndi kukhala ali moyo!

Genesis 7:10-24; 8:1-17; 1 Petro 3:19, 20.

Mafunso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena