Anachita Chifuniro cha Yehova
Eliya Atamanda Mulungu Woona
MUNTHUYO ankamsaka ngati nyama ku Israyeli. Ndithudi, iye akanaphedwa nthaŵi yomweyo mfumu ikanampeza. Kodi munthu ankasakidwayo anali yani? Mneneri wa Yehova Eliya.
Mfumu Ahabu ndi mkazi wake wachikunja, Yezebeli, anachititsa kulambira Baala kufala mu Israyeli. Chifukwa cha zimenezo, Yehova anadzetsa chirala m’dzikomo, chimenechi chinali chaka chachinayi cha chiralacho. Yezebeli atapsa mtima anatsimikiza kupha aneneri a Yehova, koma Ahabu anafuna makamaka Eliya. Anali Eliya yemwe anauza Ahabu zaka zitatu zapitazo kuti: “Ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.” (1 Mafumu 17:1) Ndipo chirala chimene chinatsatiracho chinapitirizabe.
Mu mkhalidwe woopsa umenewu, Yehova anauza Eliya kuti: “Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.” Ngakhale kuti anali kudziika pangozi yaikulu, Eliya anamvera lamulo la Yehova.—1 Mafumu 18:1, 2.
Adani Aŵiri Akumana
Ahabu atangomuona Eliya anamfunsa kuti, “Kodi ndiwe uja umvuta Israyeliyo?” Eliya anayankha molimba mtima kuti, “Sindimavuta Israyeli ine ayi, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.” Kenako Eliya analamula kuti Aisrayeli onse akakumane ku Phiri la Karimeli, kuphatikizapo “aneneri a Baala mazana anayi mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anayi.” Ndiyeno Eliya anawalankhula anthuwo nati: “Mukayikakayika kufikira liti?a Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo.”—1 Mafumu 18:17-21.
Anthuwo anangoti duu. Mwinamwake anazindikira tchimo lawo la kulephera kudzipereka kotheratu kwa Yehova. (Eksodo 20:4, 5) Kapena mwina chikumbumtima chawo chinali chakufa kwakuti sanadzione kuti anachimwa pakugaŵa kudzipereka kwawo kuti kwinaku azilambira Yehova kwinakunso Baala. Mulimonse mmene zinalili, koma Eliya anawalangiza anthuwo kuti abweretse ng’ombe ziŵiri—imodzi ya aneneri a Baala inayo yake. Ng’ombe zonsezo zinali zoti azipereke nsembe, koma osasonkhapo moto. Eliya anati: “Muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu.”—1 Mafumu 18:23, 24.
Yehova Atamandidwa
Aneneri a Baala anayamba ‘kuvinavina kuguwa adalimanga.’ Mmaŵa wonse anali kumangofuula kuti: “Baala, timvereni ife.” Koma Baala sanayankhe. (1 Mafumu 18:26) Kenako Eliya anayamba kuwanyodola kuti: “Kwezani mawu, popeza ndiye mulungu.” (1 Mafumu 18:27) Ndiyeno aneneri a Baalawo anayamba kudzitematema ndi mipeni ndi nthungo—zimene anthu akunja ankachita kaŵirikaŵiri kuti milungu yawo iwamvere chisoni.b—1 Mafumu 18:28.
Tsopano kunali cha kumasana, ndipo olambira Baala [anachitabe ngati aneneri, NW],—m’nkhani ino, mawu amenewo akutanthauza kuchita zinthu ngati wamisala ndi monyanyuka. Dzuŵa litapendeka, potsirizira Eliya anauza anthu onsewo kuti “Senderani kwa ine.” Onsewo ankangopenyerera dwii pamene Eliya anali kumanganso guwa la nsembe la Yehova, nakumba dzenje mozungulira, naduladula ng’ombe ija nthulinthuli, naika paguwapo pamodzi ndi nkhuni zowotchera. Atatha zimenezo, ng’ombeyo, guwalo, ndi nkhunizo anazinyoŵetseratu ndi madzi, ndipo dzenjelo analidzaza madzi (mosakayikira anali madzi a m’nyanja omwe anatunga m’nyanja ya Mediterranean). Kenako Eliya anapemphera kwa Yehova, kuti: “Lero kudziŵike kuti inu ndinu Mulungu wa Israyeli, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mawu anu ndachita zonsezi. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziŵe kuti inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti inu mwabwezanso mitima yawo.”—1 Mafumu 18:29-37.
Mwadzidzidzi, moto unatsika kumwamba “nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera.” Anthu omwe anali kupenyererawo anaŵeramira pansi nthaŵi yomweyo nkumati: “Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.” Ndiyeno Eliya analamula kuti aneneri a Baala agwidwe ndipo anapita nawo kuchigwa cha Kisoni, kumene anakawaphera.—1 Mafumu 18:38-40.
Zimene Tingaphunzirepo
Eliya anasonyeza zimene zingaoneke ngati kulimba mtima koposa kwa munthu wanyama. Komabe, wolemba Baibulo Yakobo akutitsimikizira kuti “Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife.” (Yakobo 5:17) Si kuti iye analibiretu mantha ndi nkhaŵa iyayi. Mwachitsanzo, pamene Yezebeli analumbira kumbwezera chilango chifukwa chakupha aneneri a Baala, Eliya anathaŵa kenako anafuulira Yehova mwapemphero kuti: “Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova.”—1 Mafumu 19:4.
Yehova sanamchotsere Eliya moyo wake mwa kumlola kufa. Koma anamthandiza mwachifundo. (1 Mafumu 19:5-8) Lerolino atumiki a Mulungu angakhale nchidaliro chakuti Yehova adzawachitira zofananazo pamene iwo ali mumkhalidwe wodetsa nkhaŵa kwambiri, mwina chifukwa chotsutsidwa. Ndithudi, ngati angapemphere kwa Yehova kuti awathandize, adzawapatsa “ukulu woposa wamphamvu,” kotero kuti ngakhale ali “osautsika,” sakhala “opsinjika.” Choncho adzawathandiza kupirira monga mmene anathandizira Eliya.—2 Akorinto 4:7, 8.
[Mawu a M’munsi]
a Akatswiri ena azamaphunziro amati mwina Eliya ankatanthauza kuvina kwamwambo kwa olambira Baala. Mawu amodzimodziwo akuti ‘kuvinavina’ agwiritsiridwa ntchito pa 1 Mafumu 18:26 pofotokoza kuvina kwa aneneri a Baala.
b Ena amati kudzichekacheka kunali ngati kudzipereka nsembe. Zonse ziŵirizo zinkatanthauza kuti kudzivulaza kapena kukhetsa mwazi kungapangitse munthuyo kuyanjidwa ndi mulungu wake.