Nyimbo 172
Pitirizanibe Kufunafuna Ufumu Choyamba
1. Kwa Yehova chokongola,
Ndi chomkondweretsadi,
Ndicho Ufumu wa Kristu,
Udzawongola zinthu.
Aneneri anawona
Nayembekezeradi.
Lero mtsogoleri
Yesu Amatilimbikitsa.
(Korasi)
2. Polalika Ufumuwo
Ndimwaŵi kwa ’nthu ake!
Tapatsidwatu ntchitoyo,
Tiisamaliredi.
Tikhala bwanji ndi nkhaŵa
Zofunika za maŵa?
M’lungu adzatigaŵira
Tikafuna Ufumu.
(Korasi)
3. Dongosololi lidzatha;
La M’lungu lidzayamba.
Anthu adzatama M’lungu;
Paradaiso adza.
Tifalitse za Ufumu,
Kwa anthu onga nkhosa
Kuyembekeza Yehova
Ndi Teokrase wake.
(KORASI)
Mufune Ufumu kaye
Ndi chilungamo cha Ya.
Mkwezeni iye choyamba,
Ndi kumtumikirabe.