Nyimbo 217
Kupeza Ubwenzi wa Yehova
1. Ndani adzakhala bwenzi la Yehova?
Ndani adzakhala muhema wanu kosatha?
Iye wosawopa Wopanda tchimoyo,
Inde, woyera mtima nachita mowonadi.
Ubwenzi wanu Ya, mupatsa kwa yani?
Ndani adzakhala nanu muphiri loyera?
Iye wosamalira malankhulidwe ake kwa wina.
(Korasi)
2. Ndani adzakhala nanu O Mulungu?
Ndani angakhalitsetu monga bwenzi lanu?
Iye wowonayo, Ngakhale muvuto,
Ayenda molungama, nachita chowonadi.
Tikhumba ubwenzi wanutu Yehova.
Mawu anu atidziŵitsa zofuna zanu.
Tikonze njira zathu ndipo mukhalebe bwenzi lathu.
(Korasi)
3. Tifuna kukhala ndi inu Yehova.
Mtendere wanu uposa chidziŵitso chonse.
Mwa Ambuye Yesu, Munabwezeretsa
Kulambirako. Makamu akulambirani.
Wammwambamwambanu Tidzatchinjiriza
Ubwenzi wanu ndi kukhala wopanda banga.
Monga ogwirizana tidzaima paphiri lanulo.
(KORASI)
Tikhale mabwenzi Anu Ya kosatha.