Yehova—Kodi Ndimnansi Wanu Kapena Bwenzi Lanu?
“JOHN, tabwera kuno ndikusonyeze bwenzi langa. Uyu ndi—pepani, kodi dzina lako ndani paja?”
Kodi munamvapo kuphophonya koteroko polankhulana? Kumapereka chitsanzo cha mmene anthu ena amagwiritsirira ntchito molakwa liwu lakuti “bwenzi.” Kwenikweni amangotanthauza “mnansi” ndipo mwina osati ngakhale zimenezo. Kungowadziŵa Abambo Chisale okhala kutsidya la msewu kumasiyana ndi kukhala bwenzi lawo.
Dikishonale ina imamasulira “mnansi” kukhala “munthu amene wina anakumanapo naye koma amene alibe naye chikondi chachikulu chaumwini.” Liwulo limasonyeza “kudziŵana pang’ono, kusayandikana kwambiri, kusayanjana kwenikweni, ndi kusakhala kwenikweni ndi malingaliro ofunirana zabwino muja zimakhalira ndi BWENZI.”
Kusakhalapo kwa chikondi chachikulu kumeneku kumasonyeza chifukwa chake sitimadera nkhaŵa kwambiri zomwe zimachitikira anansi, pamene kuli kwakuti timadziloŵetsa mofunitsitsa m’miyoyo ya mabwenzi athu. Timakondwera m’zisangalalo zawo, ndi kuchita nawo chisoni m’mavuto awo, kuchititsa mikhalidweyo kutikhudza mozama. Ndithudi, tiyenera kukhala osamala kusalola kukhudzidwa kwathu kutisokeretsa kuloŵerera m’nkhani zawo zamtseri.—1 Petro 4:15.
Ndiponso kukhala ndi chikondi chaumwini chachikulu pa mabwenzi athu kumasonyeza chifukwa chimene kaŵirikaŵiri timayesera kuwakondweretsa. Ngati mnansi wathu wawona kuti mkhalidwe wathu ngwoipa kapena ngwosayenera, kusakondwa kwakeko sikumatisonkhezera kwenikweni kusintha. Koma bwenzi lingakhale ndi chisonkhezero champhamvu ndithu, mukhale m’kavalidwe, kayendedwe, kapena kaimidwe kamaganizo.
Ubwenzi umafuna thayo lalikulu la kudalirika, chikondi, ulemu, ndi kukhulupirika, koposa mmene unansi umachitira. Kunena zowona, munthu amene amafunsira ubwenzi popanda thayo loloŵetsedwapo, amangofuna mnansi, osati bwenzi. Mabwenzi okondanadi amakhala ofunitsitsa kukwaniritsa mathayo obwera ndi chikondi chachikulu chaumwini, pozindikira kuti mathayo amenewo amaŵapatsa mwaŵi wakutsimikizira ubwenzi wawo.
Ubwenzi ndi Mulungu
Pokhala Mlengi, Yehova ndiye Atate wakumwamba wa anthu ndipo ayenera kukondedwa, kumvedwa, ndi kupatsidwa ulemu. Koma amafuna anthu kuchita zimenezi chifukwa cha chikondi chachikulu chaumwini, osati chabe chifukwa cha thayo. (Mateyu 22:37) Ndiponso amafuna kuti iwo amkonde monga Bwenzi. (Salmo 18:1) Popeza kuti ‘anayamba iye kutikonda,’ anayala maziko angwiro a ubwenzi wotero iyemwini.—1 Yohane 4:19.
Makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anali kumdziŵa Yehova. Koma funso linali lakuti: Kodi iwo akavomereza ubwenzi umene iye anafuna? Momvetsa chisoni, sanatero. Kufunitsitsa kwawo kwadyera ufulu wakudziimira pawokha mmalo mwa Mulungu kunasonyeza kuti analibe chikondi chachikulu chaumwini kwa iye. Ngakhale kuti anafunitsitsa kulandira madalitso a ubwenzi umene iye anafuna, sanali ofunitsitsa kukwaniritsa mathayo ake. Zikuwoneka kuti anangofuna kusangalala ndi zabwino ndi chisungiko cha mudzi wawo wokongola wa Paradaiso popanda kulipira lendi, titero kunena kwake.
Tonsefe, ena mokulirapo kuposa ena, tinalandira choloŵa chimenechi cha mzimu wosayamikira ndi wodziimira patokha. (Genesis 8:21) Mwachitsanzo, achichepere ena alola chikhumbo chawo chachibadwa cha kudziimira pawokha kuwachititsa kusayamikira makolo awo. Zimenezi zachititsa kusweka kwa ubwenzi wamtengo wapatali umene uyenera kukhalapo pakati pa iwo ndi makolo awo m’moyo wonse. Komabe, ngakhale kuti zimenezi nzomvetsa chisoni, kusweka kwa ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba nkowopsa koposa. Kunena zowona, kungakhale kwakupha!
Ziyeneretso za Ubwenzi
Popanda chidaliro, palibe unansi umene ungakhalitse, ukhale wa anthu kapena ndi Mulungu. Kholo Abrahamu anazindikira bwino lomwe, ndipo nchifukwa chake nthaŵi zonse anasonyeza chidaliro chonse mwa Mulungu. Ŵerengani Genesis 12:1-5 ndi 22:1-18, ndi kuwona zitsanzo zapadera ziŵiri za chidaliro chake mwa Yehova. Inde, ‘Abrahamu anakhulupirira [Yehova, NW], ndipo kudaŵerengedwa kwa iye chilungamo.’ Chifukwa chake ‘anatchedwa bwenzi la [Yehova].’—Yakobo 2:23.
Chiyeneretso china cha ubwenzi ndi Mulungu ndicho kukwaniritsa mathayo amene ubwenzi umenewu umadzetsa. Chifukwa cha kukhala kwathu anthu otsika poyerekezera ndi Yehova, mathayo ameneŵa moyenerera amaposa aja a ubwenzi waumunthu. Samangotanthauza kuti tiyenera kumkondweretsa m’zinthu zina—monga momwe tingachitire kwa bwenzi laumunthu. Amaphatikizapo kukhala kwathu ofunitsitsa kumkondweretsa m’zinthu zonse. Yesu, Mwana wa Mulungu ndi bwenzi lake lapamtima, anasonyeza zimenezi pamene ananena za Yehova kuti: ‘Ndichita ine zimene zimkondweretsa iye nthaŵi zonse.’—Yohane 8:29.
Chotero, ubwenzi ndi Yehova, kapena Mwana wake, ngwosatheka popanda mathayo ophatikizidwa; umadalira pa kukhala kwathu ndi moyo mogwirizana ndi ziyeneretso za ubwenzi zimene iwo anakhazikitsa. (Onani Salmo 15:1-5.) Yesu anasonyeza zimenezi momvekera bwino pokambitsirana ndi ophunzira ake kuti: ‘Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu.’—Yohane 15:14.
Chiyeneretso china cha ubwenzi ndicho kulankhulana komasuka ndi kosabisa. Patsiku la imfa yake, Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti: ‘Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziŵa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.’ (Yohane 15:15) Pokambitsirana malingaliro ake ndi mabwenzi ake, Yesu anali kutsatira chitsanzo cha Atate wake wakumwamba, amene Amosi 3:7 ananena za iye kuti: ‘Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.’
Kodi zimenezi sindizo zimachitika kaŵirikaŵiri pakati pa mabwenzi? Tingakhale opanda chifuno cha kufotokozera Abambo Chisale okhala kutsidya la msewuwo zokumana nazo zathu. Ndipo mosakaikira konse sitingafune kuwauza zakukhosi ndi malingaliro athu ena. Ndiiko komwe, iwo ali mnansi chabe. Koma kwa mabwenzi athu, eya, kaŵirikaŵiri timafulumira kuwauza zinthu zoterozo!
Ziridi tero ndi unansi wathu ndi Mulungu. Sitimazengereza mpang’ono pomwe kulankhula naye m’pemphero, kumuululira zosoŵa zathu, zikhumbo, ndi zakukhosi kwathu. Ndithudi, ngati kulankhulana kuli kwambali imodzi, ubwenzi umatha mwamsanga. Choncho tiyeneranso kukhala ofunitsitsa kulola Mulungu kulankhula nafe. Timachita zimenezo mwakumvetsera mosamalitsa Mawu ake olembedwa, kusinkhasinkha pa uphungu wake, ndiyeno kuugwiritsira ntchito bwino koposa monga momwe tingathere.
Kodi Ubwenzi ndi Yehova Uli Wofunika Motani kwa Inu?
Kuti muthandizidwe kuyankha funsolo, talingalirani za ubwenzi wapadera waumunthu. Ngati ndinu wachichepere, mwina mukufuna ubwenzi umene ungakuloŵetseni muukwati. Ndithudi, mumazindikira kuti kungodziŵana ndi woyembekezeredwa kukhala mnzanu wamuukwati sindiko maziko oyenerera a ukwati. Choyamba chinansicho chiyenera kufikira pakukhala ubwenzi. Ndiyeno ubwenzi umenewu ungakulitsidwe ndi kuumbidwa kukhala unansi wathithithi umene ungadzapange maziko oyenera kotheratu a ukwati wachimwemwe.
Tsopano, talingalirani. Kodi ndikuyesayesa kokulira motani kumene anthu ambiri amakuchita kuti akulitse ubwenzi wotero? Kodi ndinthaŵi ndi ndalama zochuluka motani zimene amataya poukhazikitsa ndi kuusungitsa? Kodi amataya nthaŵi yochuluka motani akuulingalira? Kodi amapanga makonzedwe aakulu motani—kapena kukhala ofunitsitsa kusintha makonzedwewo—ndi cholinga cha kuwongolera kapena kusungitsa unansiwo?
Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi zimenezi ziri motani poyerekezera ndi zoyesayesa zanga zakukulitsa ubwenzi ndi Mlengi wanga kapena kuuwongolera ndi kuulimbitsa? Kodi ndimataya nthaŵi yochuluka motani pochita zimenezo? Kodi malingaliro anga amaphatikizapo ubwenzi wanga ndi Yehova kuukulu wotani? Kodi ndikupanga makonzedwe kufika pati—kapena kukhala wofunitsitsa kusintha makonzedwewo—mokulira motani ndi cholinga cha kuwongolera ndiyeno kusungitsa unansiwo?’
Akristu achichepere ayenera kuzindikira bwino lomwe kuti maubwenzi onse aumunthu, kuphatikizapo omwe mkupita kwa nthaŵi angaŵaloŵetse muukwati, ngachiŵiri poyerekezera ndi ubwenzi umene ayenera kukhala nawo ndi Mlengi. Nchifukwa chake amafulumizidwa pa Mlaliki 12:1 kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” Ambiri akuchita zimenezi mwakutumikira poyera monga aminisitala a Mulungu, chiŵerengero chomawonjezereka nthaŵi zonse akutumikira monga alaliki anthaŵi zonse, kapena apainiya.
Mosasamala kanthu ndi kusekedwa komakulakula ndi mkhalidwe wakusapembedza woŵazinga, amachirikiza Yehova molimba mtima pamene amva zitonzo zonama ndi zinenezo zoikidwa pa iye. Kodi sizomwezo nanga zimene Yehova amayembekezera kwa mabwenzi ake? Kodi sizomwe nafenso tingayembekezere kwa mabwenzi athu? Ndipo kodi mitima yathu sikakondwera kuwona mabwenzi athu akutero mokangalika ndipo modalirika?—Yerekezerani ndi Miyambo 27:11.
Inde, ubwenzi ndi Mulungu—monganso ndi anthu—umadzetsa mathayo omwe ayenera kukwaniritsidwa ngati ubwenziwo uti ukhalitse. Munthu wosafuna kulandira mathayo ameneŵa, kapena wosakonzekera kudzipatulira kwa Mulungu ndiyeno kukulondola, mwina angangomdziŵa chabe Yehova. Komabe, afunikirabe kupeza chimwemwe chakukhala Bwenzi Lake.
[Chithunzi patsamba 25]
Abrahamu anakhulupirira Mulungu motero anadzatchedwa bwenzi la Yehova