Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kulambira Makolo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Sal. 146:3, 4: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wamunthu . . . mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”

      Asayansi ndi madokotala a opareshoni sanapeze umboni uliwonse wa mbali ya anthu yozindikira, ya moyo imene imapulumuka pamene thupi lifa.

      Wonaninso tsamba 153-155, pamutu wakuti “Imfa.”

      Kodi mukanakonda kuti ana anu ndi adzukulu anu akusonyezeni ulemu ndi chikondi pamene mudakali amoyo kapena kuti achite madzoma pamanda anu mutafa?

      Aef. 6:2, 3: “Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wanthaŵi yaitali padziko.” (Ana ophunzitsidwa m’malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo amasonyeza ulemu umene umabweretsa chisangalalo kumitima ya makolo awo adakali ndi moyo.)

      Miy. 23:22: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.”

      1 Tim. 5:4: “Ngati wamasiye wina alinawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuŵabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.”

      Pamene obwebweta anena kuti amapereka mauthenga ochokera kwa akufa, kodi kwenikweni amenewa amachokera kuti?

      Yes. 8:19: “Pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ung’udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?” (Kodi Mulungu akanatichenjeza motsutsana ndi machitamachita otere ngati akutichititsadi kulankhulana ndi okondedwa athu?)

      Mac. 16:16: “Pamene tinali kumka kukapemphera, anakumana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye wake zambiri pa kubwebweta.”

      Wonaninso tsamba 190-193, pamutu wakuti “Kulambira Mizimu.”

      Kodi nkwayani kumene kulambira kwathu kuyenera kulunjikitsidwako?

      Luka 4:8, NW: “Yesu anati kwa iye: ‘Kwalembedwa, “Ndiye Ambuye Mulungu wako uyenera kumlambira, ndipo ndi kwa iye yekha uyenera kuperekako utumiki wopatulika.”’”

      Yoh. 4:23, 24: “Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mu mzimu ndi m’chowonadi.”

      Kodi nchiyembekezo chotani chimene chiripo kaamba ka mtsogolo cha kugwirizanitsa ziŵalo zabanja, kuphatikizapo awo amene anafa?

      Yoh. 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene anachita zoipa kukuuka kwa kuŵeruza.”

  • Kulambira Mizimu
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kulambira Mizimu

      Tanthauzo: Chikhulupiriro chakuti mbali ya mzimu ya anthu imapulumuka imfa yathupi laumunthu ndipo ingakhoze kulankhulana ndi amoyo, kaŵirikaŵiri kupyolera mwa munthu amene amatumikira monga wobwebweta. Anthu ena amakhulupirira kuti zinthu zonse zakuthupi ndi zochitika zonse za chilengedwe ziri ndi mizimu yokhalamo. Kupenduza ndiko kugwiritsiridwa ntchito kwa mphamvu imene imavomerezedwa kukhala yochokera kwa mizimu yoipa. Mipangidwe yonse ya kukhulupirira mizimu imatsutsidwa mwamphamvu m’Baibulo.

      Kodi kulidi kotheka kwa munthu kulankhulana ndi “mzimu” wa wokondedwa wakufa?

      Mlal. 9:5, 6, 10: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano. Chirichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena