Kulambira Makolo
Tanthauzo: Chizoloŵezi cha kupatsa ulemu ndi kulemekeza makolo akufa (mwa dzoma kapena mwa njira zina) chikhulupiriro chakuti akuzindikira m’dziko losawoneka ndipo angathe kuthandiza kapena kuvulaza amoyo ndipo chifukwa chake ayenera kukondweretsedwa. Sichiri chiphunzitso Chabaibulo.
Kodi makolo akufawo akuzindikira zimene amoyo amachita ndipo kodi makolo amenewa ali okhoza kuthandiza anthu amoyo?
Mlal. 9:5: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.”
Yobu 14:10, 21, NW: “Munthu amwalira, ndipo kodi ali kuti? Ana ake awona ulemu osadziŵa iye.”
Sal. 49:10, 17-19: “Awona anzeru amafa, monga awonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chawo. . . . Pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m’mbuyo. . . . Adzamuka kumbadwo wa makolo ake; sadzawona kuunika nthaŵi zonse.”
Kodi sizowona kuti chakudya choikidwa paguwa lansembe kapena pamanda chimakhalapobe chosakhudzidwa? Kodi ichi sichimasonyeza kuti akufa ali osakhoza kupindula kuchokera kwa ife?
Wonaninso mutu waukulu wakuti “Kulambira Mizimu.”
Kodi pali chifukwa cha kuwopera kuti makolo athu akufa adzativulaza?
Mlal. 9:5, 6: “Koma akufa . . . chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi ya muyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitika pansi pano.”
Kodi pali mbali yauzimu ya munthuyo imene imapulumuka imfa ya thupi?
Ezek. 18:4: “Tawonani, miyoyo yonse ndiyanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ndiponso vesi 20)
Sal. 146:3, 4: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wamunthu . . . mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”
Asayansi ndi madokotala a opareshoni sanapeze umboni uliwonse wa mbali ya anthu yozindikira, ya moyo imene imapulumuka pamene thupi lifa.
Wonaninso tsamba 153-155, pamutu wakuti “Imfa.”
Kodi mukanakonda kuti ana anu ndi adzukulu anu akusonyezeni ulemu ndi chikondi pamene mudakali amoyo kapena kuti achite madzoma pamanda anu mutafa?
Aef. 6:2, 3: “Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wanthaŵi yaitali padziko.” (Ana ophunzitsidwa m’malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo amasonyeza ulemu umene umabweretsa chisangalalo kumitima ya makolo awo adakali ndi moyo.)
Miy. 23:22: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.”
1 Tim. 5:4: “Ngati wamasiye wina alinawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuŵabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.”
Pamene obwebweta anena kuti amapereka mauthenga ochokera kwa akufa, kodi kwenikweni amenewa amachokera kuti?
Yes. 8:19: “Pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ung’udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?” (Kodi Mulungu akanatichenjeza motsutsana ndi machitamachita otere ngati akutichititsadi kulankhulana ndi okondedwa athu?)
Mac. 16:16: “Pamene tinali kumka kukapemphera, anakumana ndi ife namwali wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye wake zambiri pa kubwebweta.”
Wonaninso tsamba 190-193, pamutu wakuti “Kulambira Mizimu.”
Kodi nkwayani kumene kulambira kwathu kuyenera kulunjikitsidwako?
Luka 4:8, NW: “Yesu anati kwa iye: ‘Kwalembedwa, “Ndiye Ambuye Mulungu wako uyenera kumlambira, ndipo ndi kwa iye yekha uyenera kuperekako utumiki wopatulika.”’”
Yoh. 4:23, 24: “Ikudza nthaŵi, ndipo tsopano iripo, imene olambira owona adzalambira Atate mu mzimu ndi m’chowonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mu mzimu ndi m’chowonadi.”
Kodi nchiyembekezo chotani chimene chiripo kaamba ka mtsogolo cha kugwirizanitsa ziŵalo zabanja, kuphatikizapo awo amene anafa?
Yoh. 5:28, 29: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene anachita zoipa kukuuka kwa kuŵeruza.”