Kodi Mkhalidwe wa Akufa Ngwotani?
KUWOPA akufa kwazikidwa pa lingaliro limodzi longoyerekezera—lakuti akufa ali ndi moyo kapena ali ndi mzimu umene umapitiriza kukhala ndi moyo pambuyo pa imfa. Ngati Baibulo limaphunzitsa momvekera bwino kuti lingaliro limeneli nlonama, pamenepo chikayikiro chakuti kaya akufa angakuvulazeni kapena ayi chathetsedwa. Chotero, pamenepa, kodi nchiyani chimene Baibulo limanena?
Ponena za mkhalidwe wa akufa, Mawu a Mulungu amati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiŵalika. Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano; ndipo nthaŵi yamuyaya sagaŵa konse kanthu kalikonse kachitidwa pansi pano.”—Mlaliki 9:5, 6.
Polingalira zimenezo, kodi akufa angakuthandizeni kapena kukuvulazani? Ayi, Malemba akutero. Akufa sadziŵa kanthu ndipo ali mumkhalidwe wachete. Ali osakhoza kulankhulana ndi amoyo kapena kusonyeza mkhalidwe uliwonse—chikondi kapena mdano—kapena kuchita ntchito ina iliyonse. Simufunikira kuwawopa konse.
‘Chabwino, inde, zimenezo zingakhale zoona ngati mukunena za imfa ya thupi,’ ena angatero. ‘Komatu imfa ya thupi sili mapeto a moyo; imangotulutsa mzimu m’thupi. Mzimuwo ungathandize kapena kuvulaza amoyo.’ Mamiliyoni a anthu padziko lapansi lonse amalingalira motero.
Mwachitsanzo, m’Madagascar moyo umangolingaliridwa kukhala njira yodzerapo, chotero maliro ndi kufukula mtembo zimalingaliridwa kukhala zofunika kwambiri kuposa ukwati. Kumalingaliridwa kuti munthuyo anachokera kwa makolo ake ndipo amabwerera kwa iwo pa imfa. Chifukwa chake, nyumba za amoyo zimamangidwa ndi mitengo ndi njerwa zosaotcha, zomangira zimene zimawonongeka m’kupita kwanthaŵi, pamene kuli kwakuti manda, “nyumba” za akufa, kaŵirikaŵiri zimakhala zolinganizidwa bwino ndi zolimba. Pa kufukula mtembo, banja ndi mabwenzi amalingalira kuti adzadalitsidwa, ndipo akazi amakhulupirira kuti ngati akhudza mafupa a wachibale wakufayo, adzakhala obala ana. Koma, kachiŵirinso, kodi nchiyani chimene Mawu a Mulungu amanena?
Imfa Sinalinganizidwire Mtundu wa Anthu
Nkokondweretsa kudziŵa kuti Yehova Mulungu analenga munthu kuti akhale ndi moyo, ndipo ananena za imfa kokha monga chotulukapo cha kusamvera. (Genesis 2:17) Mwachisoni, mwamuna ndi mkazi oyamba anachimwa, ndipo monga chotulukapo chake, uchimo unayambukira mtundu wonse wa anthu monga choloŵa chakupha. (Aroma 5:12) Chotero munganene kuti imfa yakhala chinthu chenicheni chochiyembekezera m’moyo chiyambire pa kusamvera kwa anthu oyamba aŵiriwo, inde, chinthu chenicheni choŵaŵa m’moyo. Tinalengedwera kukhala ndi moyo, kumene kuli chifukwa china chimene kulili kovuta kwambiri kwa mamiliyoni osaŵerengeka kulingalira za imfa kukhala mapeto.
Malinga ndi kunena kwa cholembedwa cha Baibulo, Satana anayesa kunyenga anthu aŵiri oyamba ponena za imfa mwa kutsutsa chenjezo la Mulungu lakuti kusamvera kukadzetsa imfa. (Genesis 3:4) Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, kunakhala kwachionekere kuti anthu amafa monga momwedi Mulungu ananenera kuti akatero. Motero, m’zaka mazana ambiri Satana anadza ndi bodza linanso—lakuti mbali inayake yauzimu mwa munthu imapitirizabe kukhala ndi moyo pa imfa ya thupi. Chinyengo chotero chimayenerera bwino lomwe Satana Mdyerekezi, amene Yesu anamfotokoza kukhala “atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Mosiyana ndi zimenezo, yankho la Mulungu pa imfa ndilo lonjezo lolimbikitsa.
Lonjezo Lotani?
Lili lonjezo la chiukiriro cha ambiri. Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “chiukiriro” ndilo a·naʹsta·sis. Kwenikweni limatanthauza “kuimiriranso,” ndipo limanena za kuuka kuchokera mu imfa. Inde, munthu amagona mu imfa, koma Mulungu mwa mphamvu yake angathe kuukitsanso munthu. Munthu amataya moyo, koma Mulungu angampatsenso moyo. Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anati “ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Mtumwi Paulo anasonyeza “chiyembekezo [chake] cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Yobu, mtumiki wa Mulungu wokhulupirika m’nthaŵi za Chikristu chisanadze, analengezanso za chiyembekezo chake m’chiukiriro kuti: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga. Mukadaitana [Mulungu], ndipo ndikadakuyankhani.”—Yobu 14:14, 15.
Kodi lonjezo lomveka bwino la chiukiriro silimasonyeza bodza la lingaliro lakuti akufa ali amoyo mumpangidwe wauzimu? Ngati akufa akanakhala amoyo ndi kukhala kumwamba kapena kudziko lina la mizimu, kodi chifuno cha chiukiriro chikanakhala chotani? Kodi iwo sakanakhala atalandira kale mphotho kapena choikidwiratu chawo? Kupenda Mawu a Mulungu kumavumbula kuti akufa ngakufadi, osadziŵa kanthu, agona kufikira pa kugalamutsidwa kwakukuluko mwa chiukiriro m’dziko latsopano—paradaiso—lolonjezedwa ndi Atate wathu wachikondi, Yehova. Koma ngati imfa sitanthauza kulekana kwa thupi ndi mzimu ndipo ngati mzimu sumapitiriza kukhala ndi moyo, bwanji nanga za zochitika zoonekera ngati mawu ochokera kwa mizimu?
Mawu Ochokera kwa Mizimu
Zochitika zosaŵerengeka zasimbidwa zonena za mawu olingaliridwa kukhala ochokera kwa mizimu. Kodi nkuti kwenikweni kumene amachokera? Baibulo limatichenjeza kuti “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo.” (2 Akorinto 11:14, 15) Inde, kuti zinyenge ndi kusocheretsa anthu mosavuta kwambiri, ziŵanda (angelo opanduka) zalankhula ndi amoyo, nthaŵi zina zikumayerekezera kukhala zothandiza.
Mtumwi Paulo amapereka chenjezo lina ponena za mkupiti umenewu wa kunyenga: “Ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.” (1 Timoteo 4:1) Chotero mchitidwe uliwonse wogwirizanitsidwa ndi akufa mwachionekere ungakhale uli wochokera kwa ziŵanda zimene zimadzionetsa ngati “atumiki achilungamo” ndi kuchirikiza bodza lachipembedzo, zikumaika anthu mu ukapolo wa kukhulupirira malaulo kumene kumawachotsa pa choonadi cha Mawu a Mulungu.
Potsimikiziritsa kuti akufa sanganene chilichonse, kuchita chilichonse, kapena kumva chilichonse, Salmo 146:3, 4 limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. [Mzimu, NW] wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” Kodi ndi mzimu wotani umene ‘umachoka’? Ndiwo mphamvu ya moyo ya munthuyo imene imachirikizidwa ndi kupuma. Chifukwa chake, pamene munthu womwalira analeka kupuma, mikhalidwe yake sinagwirenso ntchito konse. Iye amaloŵa m’mkhalidwe wa kusazindikira mpang’ono pomwe. Chotero nkosatheka kuti iye alamulire amoyo.
Nchifukwa chake Baibulo limayerekezera imfa ya munthu ndi ya nyama, likumanena kuti zonsezo zimakhala zosadziŵa kanthu pa imfa ndipo zimabwerera ku fumbi limene zinapangidwa nalo. Mlaliki 3:19, 20 amati: “Chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi [mzimu, NW] umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. Onse apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.”
Podziŵa kuti ziŵanda zimayesa kunyenga anthu kuyamba kuganiza kuti angalankhulane ndi kuyambukiridwa ndi akufa, Yehova Mulungu anachenjeza anthu ake, Israyeli wakale kuti: “Asapezeke mwa inu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10-12.
Mwachionekere, lingaliro lakuti akufa angathe kutivulaza silimachokera kwa Mulungu. Iye ndiye Mulungu wa choonadi. (Salmo 31:5; Yohane 17:17) Ndipo iye wasungira mtsogolo mwabwino kwambiri okonda choonadi amene amamlambira “mumzimu ndi m’choonadi.”—Yohane 4:23, 24.
Yehova, Mulungu wa Choonadi ndi wa Chikondi
Atate wathu wakumwamba wachikondi, “wosanamayo,” walonjeza kuti: Mamiliyoni ambiri amene afa ndi amene aikidwa m’manda adzaukitsidwa limodzi ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano lachilungamo! (Tito 1:1, 2; Yohane 5:28) Lonjezo lachikondi limeneli la chiukiriro limasonyeza kuti Yehova ali ndi chikondwerero chachikulu pa ubwino wa zolengedwa zake zaumunthu ndi chikhumbo chachikulu cha kuchotsa imfa, chisoni, ndi zoŵaŵa. Chotero palibe chifukwa chowopera akufa kapena kudera nkhaŵa mosayenera ponena za iwo ndi ziyembekezo zawo. (Yesaya 25:8, 9; Chivumbulutso 21:3, 4) Mulungu wathu wachikondi ndi wolungamayo, Yehova, angathe ndipo adzawaukitsa, akumachotsa zoŵaŵa za imfa.
Mawu a Mulungu, Baibulo, amafotokoza zambiri ponena za mikhalidwe imene idzakhala padziko lapansi m’dziko latsopano lolonjezedwa limenelo lachilungamo. (Salmo 37:29; 2 Petro 3:13) Idzakhala nthaŵi ya mtendere ndi chimwemwe ndi ya chikondi cha anthu anzathu onse. (Salmo 72:7; Yesaya 9:7; 11:6-9; Mika 4:3, 4) Onse adzakhala ndi nyumba zosungika ndi zabwino, ndi ntchito yokondweretsa. (Yesaya 65:21-23) Padzakhala zakudya zabwino zambiri kaamba ka onse. (Salmo 67:6; 72:16) Onse adzakhala ndi thanzi labwino kwambiri. (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Pamene kuli kwakuti atumwi ndi chiŵerengero china chowonjezereka chaching’ono adzalamulira kumwamba ndi Yesu, Baibulo silimatchula za mikhalidwe yodalitsika yakumwamba ya miyoyo ya ena pambuyo pa imfa. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Zimenezi zingakhale zachilendo ngati mamiliyoni zikwi zambiri a awo amene afa akukhalabe ndi moyo pambuyo pa imfa.
Komatu sizachilendo pamene tidziŵa chiphunzitso cha Baibulo chomvekera bwino: Akufa amaleka kukhalapo monga amoyo. Sangakuvulazeni. Awo amene ali m’manda achikumbukiro akungopumula, osadziŵa kanthu kufikira pa chiukiriro chawo m’nthaŵi yake ya Mulungu. (Mlaliki 9:10; Yohane 11:11-14, 38-44) Pamenepo, ziyembekezo zathu ndi zikhumbo, zimadalira mwa Mulungu. “Tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.”—Yesaya 25:9.
[Chithunzi patsamba 7]
Monga momwe Mawu a Mulungu amasonyezera bwino, akufa ali osakhoza kuchita kalikonse kufikira pa chiukiriro