Adamu ndi Hava
Tanthauzo: Adamu anali cholengedwa choyamba chaumunthu. Liwu Lachihebri lakuti ’a·dhamʹ latembenuzidwanso moyenelera “mwamuna,” “mwamuna wanthaka,” ndi “munthu.” Hava, mkazi woyamba, anali mkazi wa Adamu.
Kodi Adamu ndi Hava anali anthu ongoyerekezera chabe (ongopeka)?
Kodi kuli kupanda nzeru kukhulupirira kuti tonsefe tinachokera kwa makolo oyambirira amodzimodzi?
“Tsopano sayansi ikuvomereza zimene zipembedzo zambiri zazikulu zakhala zikulalikira kwa nthaŵi yaitali kuti: Anthu a mafuko onse ali . . . mbadwa zochokera kwa munthu woyamba mmodzimodziyo.”—Heredity in Humans (Philadelphia ndi New York, 1972), Amram Scheinfeld, p. 238.
“Mbiri Yabaibulo ya Adamu ndi Hava, atate ndi amayi a fuko lonse laumunthu, inasimba zaka mazana ambiri zapitazo chowonadi chimodzimodzicho chimene sayansi yasonyeza lerolino: kuti anthu onse a padziko lapansi ali banja limodzi ndipo ali ndi magwero ofanana.”—The Races of Mankind (New York, 1978), Ruth Benedict ndi Gene Weltfish, p. 3.
Mac. 17:26: “Ndi mmodzi [Mulungu] analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pankhope ya dziko lapansi.”
Kodi Baibulo limasonyeza Adamu kukhala munthu wopeka chabe woimira anthu onse oyambirira?
Yuda 14: “Henoke, wachisanu ndi chiŵiri kuyambira kwa Adamu, ananenera.” (Henoke sanali wachisanu ndi chiŵiri kuyambira kwa anthu oyambirira onse.)
Luka 3:23-38: “Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye . . . mwana wa Davide . . . mwana wa Abrahamu . . . mwana Adamu.” (Davide ndi Abrahamu ali anthu odziŵika bwino lomwe m’mbiri. Chotero kodi sikuli kwanzeru kunena kuti Adamu anali munthu weniweni?)
Gen. 5:3: “Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m’chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.” (Ndithudi Seti sanali mwana wa anthu onse oyambirira, ndiponso anthu onse oyambirira amenewo sanabale ana aamuna pamsinkhu wazaka 130 za kubadwa.)
Kodi mawu akuti njoka inalankhula kwa Hava angachititse kuti cholembedwacho chikhale chongoyerekezera?
Gen. 3:1-4: “Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu? Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, . . . Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai.”
Yoh. 8:44: “[Yesu anati:] Mdyerekezi . . . ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.” (Chotero Mdyerekezi anali magwero a bodza loyamba, lonenedwa m’Edene. Anagwiritsira ntchito njoka monga cholankhulira chowoneka. Cholembedwa cha Genesis sichikugwiritsira ntchito zolengedwa zongopeka posimba mfundoyi. Wonaninso Chivumbulutso 12:9.)
Chitsanzo: Sikuli kwachilendo kwa katswiri wolankhula atatseka pakamwa kupangitsa kuwonekera ngati kuti liwu lake likuchokera kumagwero ena. Yerekezerani ndi Numeri 22:26-31, limene likusimba kuti Yehova anachititsa bulu wa Balamu kulankhula.
Ngati ‘Adamu woyamba’ anali wongoyerekezera, bwanji za “Adamu wotsirizayo,” Yesu Kristu?
1 Akor. 15:45, 47: “Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wa kulenga moyo. Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiŵiri ali wakumwamba.” (Chotero kukana kuti Adamu anali munthu weniweni amene anachimwira Mulungu kumatanthauza kukaikira umunthu wa Yesu Kristu. Kukana kotero kumatsogolera ku kukanidwa kwa chifukwa chimene chinachititsa kufunika kwakuti Yesu apereke moyo wake kaamba ka anthu. Kukana zimenezo kumatanthauza kukanidwa kwa chikhulupiriro Chachikristu.)
Kodi ndimotani mmene Yesu mwiniyo anawonera cholembedwa cha Genesis?
Mat. 19:4, 5: “[Yesu] anayankha, nati, Kodi simunaŵerenga [pa Genesis 1:27; 2:24] kuti iye amene adalenga anthu [Adamu ndi Hava] pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi, mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi limodzi?” (Popeza kuti Yesu anakhulupirira cholembedwa cha Genesis kukhala chotsimikizirika, kodi nafenso sitiyenera kuchikhulupirira?)
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Uchimo wa Adamu unali chifuniro cha Mulungu, kakonzedwe ka Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Anthu ambiri anena zimenezo. Koma ngati ine ndinafunikira kuchita kanthu kena kamene inu munafuna kuti ndichite, kodi mukanditsutsa nako kanthuko? . . . Pamenepa, ngati uchimo wa Adamu unali chifuniro cha Mulungu, kodi nchifukwa ninji Adamu anathamangitsidwa m’munda wa Edene monga wochimwa? (Gen. 3:17-19, 23, 24)’
Kapena mukanati: ‘Imeneyo iri mfundo yokondweretsa, ndipo yankho limaphatikizapodi mtundu wa munthu amene Mulungu ali. Kodi kukakhala kolungama kapena kwachikondi kutsutsa munthu kaamba ka kuchita chinthu chimene inu mwini mwamlinganizira kuti achite?’ Ndiyeno mwinamwake mungawonjezere: (1) ‘Yehova ali Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Njira zake zonse ndichiweruzo. (Sal. 37:28; Deut. 32:4) Sichinali chifuniro cha Mulungu kuti Adamu achimwe; iye anachenjeza Adamu kusatero. (Gen. 2:17)’ (2) ‘Mulungu analoleza Adamu, monga momwe amachitira kwa ife, ufulu wa kusankha chimene akachita. Ungwiro sunaletse kugwiritsira ntchito ufulu wa kusankha kusamvera. Adamu anasankha kupandukira Mulungu, mosasamala kanthu za chenjezo lakuti imfa ikakhala chotulukapo.’ (Wonaninso tsamba 118.)