Nyimbo 60
Ufumu wa Mulungu wa Zaka Chikwi
1. M’lungu wati pakhale zaka chikwi.
Zoti Mwana wake alamule anthu.
Odzozedwa adzalamula naye.
Adzakhalatu mafumu ndi ansembe.
2. Nakomera mtima anthu onsewo,
Adzakondwa ndi ntchito yochotsa tchimo.
Paradaiso adzakuta dziko.
Owomboledwa onsewo atama Ya.
3. Zaka chikwi, mu Ufumu wa Kristu!
Ndi chikhulupiliro tikuziwona:
Oukawo aphunzira za M’lungu.
Ndi tsiku loweruza mu chilungamo.
4. Tiyenitu tiyesetse mwamphamvu;
Kukhala maso tsiku layandikira.
Molimba mtima tichite mwanzeru,
Kuitana onse kudza kwa Mulungu.